Deuteronomo 31:1-30
31 Pamenepo Mose anapita ndi kukauza Aisiraeli onse mawu awa,
2 kuti: “Tsopano ndili ndi zaka 120.+ Sindidzaloledwanso kupitiriza ntchito yanga yokutsogolerani,+ pakuti Yehova wandiuza kuti, ‘Suwoloka Yorodano uyu.’+
3 Yehova Mulungu wanu akuwoloka patsogolo panu kuti akutsogolereni.+ Iye ndiye adzawononga mitundu imeneyi pamaso panu, ndipo inu mudzaipitikitse.+ Yoswa ndiye adzakutsogolerani ndi kukuwolotsani,+ monga mmene Yehova wanenera.
4 Ndipo Yehova adzachitira mitundu imeneyi zimene anachitira Sihoni+ ndi Ogi,+ mafumu a Aamori, ndiponso zimene anachitira dziko lawo, pamene anawawononga.+
5 Yehova wapereka mitunduyi kwa inu,+ ndipo muichitire mogwirizana ndi malamulo onse amene ndakupatsani.+
6 Limbani mtima ndipo chitani zinthu mwamphamvu.+ Musawaope kapena kuchita nawo mantha,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu ndi amene akuyenda patsogolo panu. Iye sadzakutayani kapena kukusiyani ngakhale pang’ono.”+
7 Pamenepo Mose anaitana Yoswa ndi kumuuza pamaso pa Aisiraeli onse kuti: “Limba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu,+ chifukwa ndiwe amene udzalowetsa anthu awa m’dziko limene Yehova analumbirira makolo awo kuti adzawapatsa.+ Ndipo iwe ndi amene udzawapatsa dzikolo monga cholowa chawo.
8 Yehova ndi amene akuyenda patsogolo panu. Iye adzapitiriza kuyenda nanu.+ Sadzakutayani kapena kukusiyani ngakhale pang’ono. Choncho musaope kapena kuchita mantha.”+
9 Pamenepo Mose analemba chilamulo chimenechi+ ndi kuchipereka kwa ansembe, ana a Levi,+ onyamula likasa la pangano la Yehova.+ Anachiperekanso kwa akulu onse a Isiraeli.
10 Ndiyeno Mose anawalamula kuti: “Kumapeto kwa zaka 7 zilizonse, pa nthawi yoikidwiratu m’chaka chopuma,+ pachikondwerero cha misasa,+
11 pamene Aisiraeli onse afika kudzaona nkhope ya Yehova+ Mulungu wanu pamalo amene iye adzasankhe,+ muziwerenga chilamulo ichi pamaso pa Aisiraeli onse m’makutu mwawo.+
12 Sonkhanitsani anthu,+ amuna, akazi, ana ndi alendo okhala m’mizinda yanu, kuti amvetsere ndi kuphunzira,+ pakuti ayenera kuopa Yehova Mulungu wanu+ ndi kutsatira mosamala mawu onse a m’chilamulo ichi.
13 Ana awo amene sadziwa chilamulo ichi azimvetsera,+ ndipo aphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu masiku onse amene mudzakhala panthaka imene mukupita kukaitenga kukhala yanu,+ mutawoloka Yorodano.”
14 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Taona, nthawi ya kufa kwako yayandikira.+ Itana Yoswa, ndipo muime m’chihema chokumanako kuti ndimuike kukhala mtsogoleri.”+ Choncho Mose ndi Yoswa anapita ndi kukaima m’chihema chokumanako.+
15 Ndiyeno Yehova anaonekera kuchihemako, mumtambo woima njo ngati chipilala, ndipo mtambowo unaima pakhomo la chihema.+
16 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “Iweyo ugona pamodzi ndi makolo ako,+ ndipo anthu awa adzaimirira+ ndi kuchita chiwerewere pakati pawo ndi milungu yachilendo ya m’dziko limene akupita.+ Iwo adzandisiya+ ndi kuphwanya pangano limene ndinapangana nawo.+
17 Pamenepo mkwiyo wanga udzawayakira tsiku limenelo,+ ndipo ndidzawasiya+ ndi kuwabisira nkhope yanga,+ motero adzakhala chinthu choyenera kuwonongedwa. Masoka ndi zowawa zambiri zidzawagwera,+ ndipo pa tsiku limenelo adzanena kuti, ‘Masoka amenewatu akutigwera chifukwa chakuti Mulungu wathu sali pakati pathu.’+
18 Koma ine ndidzawabisira nkhope yanga pa tsiku limenelo chifukwa cha zoipa zonse zimene achita, chifukwa chotembenukira kwa milungu ina.+
19 “Tsopano dzilembereni nyimbo iyi+ ndi kuwaphunzitsa ana a Isiraeli.+ Muiike m’kamwa mwawo kuti nyimbo imeneyi ikhale mboni yanga pamaso pa ana a Isiraeliwo.+
20 Pakuti ndidzawalowetsa m’dziko limene ndinalumbirira makolo awo,+ dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ Kumeneko iwo adzadya+ ndi kukhuta, ndipo adzatukuka+ ndi kutembenukira kwa milungu ina.+ Adzatumikira milungu imeneyo ndi kundichitira chipongwe, ndipo adzaphwanya pangano langa.+
21 Ndiyeno masoka ndi zowawa zambiri zikadzawagwera,+ nyimboyi idzawayankha monga mboni, chifukwa siyenera kuchoka pakamwa pa mbadwa zawo, pakuti ndikudziwa mtima+ umene akuyamba kukhala nawo lero ndisanawalowetse m’dziko limene ndawalumbirira.”
22 Chotero Mose analemba nyimboyi pa tsiku limeneli kuti aphunzitse ana a Isiraeli.+
23 Ndiyeno Mulungu anaika Yoswa mwana wa Nuni+ kukhala mtsogoleri, ndipo anamuuza kuti: “Limba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu,+ chifukwa iwe ndi amene udzalowetsa ana a Isiraeli m’dziko limene ndawalumbirira,+ ndipo ine ndidzapitiriza kukhala nawe.”
24 Mose atangomaliza kulemba mawu onse a chilamulo ichi m’buku,+
25 anayamba kupereka malamulo kwa Alevi onyamula likasa la pangano la Yehova,+ kuti:
26 “Tengani buku ili la chilamulo,+ muliike pambali pa likasa+ la pangano la Yehova Mulungu wanu, kuti likhale mboni ya Mulungu yokutsutsani.+
27 Pakuti ineyo ndikudziwa bwino khalidwe lanu lopanduka+ ndi kuuma khosi kwanu.+ Ngati lero pamene ndili moyo pamodzi nanu mwasonyeza khalidwe lopandukira Yehova,+ ndiye kuli bwanji pambuyo pa imfa yanga!
28 Sonkhanitsani akulu onse a mafuko anu ndi atsogoleri anu,+ kuti ndilankhule mawu awa m’makutu mwawo, ndipo nditenge kumwamba ndi dziko lapansi kukhala mboni zanga pamaso pawo.+
29 Pakuti ndikudziwa bwino kuti pambuyo pa imfa yanga, mosakayikira mudzachita zinthu zokuwonongetsani+ ndipo mudzapatuka ndi kusiya njira imene ndakulamulani kuyendamo. Pamapeto pake tsoka+ lidzakugwerani, chifukwa mudzachita zoipa pamaso pa Yehova ndi kumulakwira ndi ntchito za manja anu.”+
30 Chotero Mose anayamba kulankhula mawu onse a nyimbo iyi, mpingo wonse wa Isiraeli ukumva,+ ndipo anati: