Deuteronomo 30:1-20
30 “Ndiyeno zikadzachitika kuti mawu onsewa akwaniritsidwa pa inu, madalitso+ ndi matemberero+ amene ndakuikirani pamaso panu, ndipo mwakumbukira mawu amenewa mumtima mwanu+ muli pakati pa mitundu yonse kumene Yehova Mulungu wanu adzakubalalitsirani,+
2 moti mwabwerera kwa Yehova Mulungu wanu+ ndi kumvera mawu ake ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse,+ mogwirizana ndi zonse zimene ndikukulamulani lero, inuyo ndi ana anu,
3 Yehova Mulungu wanu adzabweza kwawo anthu a mtundu wanu amene anagwidwa ndi kupita kudziko lina,+ ndipo adzakumverani chifundo+ n’kukusonkhanitsaninso pamodzi kuchokera pakati pa anthu onse kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsirani.+
4 Anthu a mtundu wanu obalalitsidwawo akadzakhala kumalekezero kwa thambo, Yehova Mulungu wanu adzakusonkhanitsani ndi kukutengani kumeneko.+
5 Choncho Yehova Mulungu wanu adzakulowetsanidi m’dziko limene makolo anu analitenga kukhala lawo, ndipo inu mudzalitenga kukhala lanu. Pamenepo, adzakuchitirani zabwino ndi kukuchulukitsani kuposa makolo anu.+
6 Yehova Mulungu wanu adzachita mdulidwe wa mitima yanu+ ndi mitima ya ana anu,+ kuti muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kuti mukhale ndi moyo.+
7 Ndipo Yehova Mulungu wanu adzaikadi matemberero onsewa pa adani anu, ndi onse odana ndi inu amene anakuzunzani.+
8 “Koma iwe udzatembenuka ndi kumvera mawu a Yehova ndi kutsatira malamulo ake onse amene ndikukupatsa lero.+
9 Ndipo Yehova Mulungu wako adzakuchititsa kukhala ndi zinthu zosefukira pa ntchito iliyonse ya manja ako,+ chipatso cha mimba yako, chipatso cha ziweto zako+ ndi chipatso cha nthaka yako.+ Pamenepo udzatukuka+ chifukwa Yehova adzakondweranso nawe kuti akuchitire zabwino, monga mmene anakondwera ndi makolo ako.+
10 Adzachita zimenezi popeza udzamvera mawu a Yehova Mulungu wako ndi kusunga malamulo ake ndi mfundo zake zolembedwa m’buku ili la chilamulo,+ chifukwa udzabwerera kwa Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse ndi moyo wako wonse.+
11 “Lamulo limene ndikukupatsa lero si lovuta kwa iwe kulitsatira, ndipo si lapatali.+
12 Silili kumwamba kuti unene kuti, ‘Ndani adzakwera kumwamba ndi kukatitengera lamulolo kuti ife tilimve ndi kulitsatira?’+
13 Ndiponso silili tsidya lina la nyanja kuti unene kuti, ‘Ndani adzawoloka kupita tsidya lina la nyanja kukatitengera lamulolo kuti ife tilimve ndi kulitsatira?’
14 Pakuti mawu a chilamulowo ali pafupi kwambiri ndi iwe, ali m’kamwa mwako ndi mumtima mwako+ kuti uwatsatire.+
15 “Taona, ine ndikuika pamaso pako lero moyo ndi zinthu zabwino, imfa ndi zinthu zoipa.+
16 [Ngati udzamvera malamulo a Yehova Mulungu wako,] amene ndikukupatsa lero ndi kukonda Yehova Mulungu wako,+ kuyenda m’njira zake ndi kusunga malamulo ake,+ mfundo zake ndi zigamulo zake,+ pamenepo udzakhaladi ndi moyo+ ndi kuchulukana. Ndipo Yehova Mulungu wako adzakudalitsa m’dziko limene ukupita kukalitenga kukhala lako.+
17 “Koma mtima wako ukatembenukira kwina ndipo sukumvera,+ moti wanyengeka, n’kugwadira milungu ina ndi kuitumikira,+
18 ndikukuuzani lero kuti mudzatheratu.+ Simudzatalikitsa masiku anu panthaka imene mukupita kukaitenga kukhala yanu mutawoloka Yorodano.
19 Ndaika moyo ndi imfa, dalitso+ ndi temberero+ pamaso panu.+ Kumwamba ndi dziko lapansi ndi mboni pa zochita zanu.+ Choncho inuyo ndi mbadwa zanu+ musankhe moyo kuti mukhalebe ndi moyo.+
20 Musankhe moyo mwa kukonda Yehova Mulungu wanu,+ kumvera mawu ake ndi kum’mamatira,+ chifukwa iye ndiye wokupatsani moyo ndi masiku ambiri+ kuti mukhale panthaka imene Yehova analumbira kwa makolo anu, Abulahamu, Isaki ndi Yakobo kuti adzawapatsa.”+