Deuteronomo 3:1-29

3  “Ndiyeno tinatembenuka ndi kulowera njira ya ku Basana. Pamenepo, Ogi+ mfumu ya Basana inatuluka pamodzi ndi anthu ake onse kudzamenyana nafe nkhondo ku Edirei.+  Chotero Yehova anandiuza kuti, ‘Usamuope ameneyu,+ chifukwa ndim’pereka ndithu m’manja mwako. Ndim’pereka pamodzi ndi anthu ake onse ndi dziko lake. Umuchite zimene unachitira Sihoni+ mfumu ya Aamori, amene anali kukhala m’Hesiboni.’  Pamenepo Yehova Mulungu wathu anaperekanso Ogi mfumu ya Basana ndi anthu ake onse m’manja mwathu, ndipo tinam’kantha moti sipanatsale ndi mmodzi yemwe wopulumuka mwa anthu ake.+  Pa nthawi imeneyo tinalanda mizinda yake yonse. Panalibe mzinda umene sitinawalande. Tinalanda mizinda 60+ m’chigawo chonse cha Arigobi,+ m’dera lonse la ufumu wa Ogi ku Basana.+  Mizinda yonseyi inali ya mipanda yolimba kwambiri ndiponso yaitali, yokhala ndi zitseko ndi mipiringidzo. Kuwonjezera pamenepo, tinalandanso matauni ambirimbiri akumidzi.  Yonseyo tinaiwononga,+ monga mmene tinachitira ndi Sihoni mfumu ya Hesiboni, mwa kuwononga mzinda uliwonse, amuna, akazi ndi ana aang’ono.+  Ndipo tinatenga ziweto ndi zofunkha zonse za m’mizindayo.+  “Pa nthawi imeneyo tinalanda dziko m’manja mwa mafumu awiri amenewo a Aamori+ amene anali kukhala m’dera la Yorodano, kuyambira m’chigwa* cha Arinoni+ mpaka kuphiri la Herimoni.+  (Asidoni anali kutcha phiri la Herimoni kuti Sirioni,+ pamene Aamori anali kulitcha kuti Seniri.)+ 10  Tinalanda mizinda yonse ya kudera lokwererapo, m’Giliyadi monse, m’Basana monse, mpaka ku Saleka+ ndi ku Edirei,+ mizinda ya m’dera la ufumu wa Ogi ku Basana. 11  Mwa Arefai+ onse, Ogi yekha mfumu ya Basana ndi amene anali atatsala. Chithatha chimene anaikapo mtembo wake chinali chachitsulo. Kodi si chija chili ku Raba+ wa ana a Aamoni? N’chachitali mikono* 9, ndipo m’lifupi mwake mikono inayi, kutsatira muyezo wodziwika. 12  Choncho pa nthawi imeneyo tinatenga dzikoli kukhala lathu. Mafuko a Rubeni ndi Gadi+ ndinawapatsa Aroweli,+ mzinda umene uli m’chigwa cha Arinoni, ndi hafu ya dera lamapiri la Giliyadi, ndi mizinda yake. 13  Hafu ya fuko la Manase ndinalipatsa dera lotsala la Giliyadi+ ndi Basana+ yense wa ufumu wa Ogi. Kodi si paja dera lonse la Arigobi+ limene ndi Basana yense, limatchedwa dziko la Arefai?+ 14  “Yairi+ mwana wamwamuna wa Manase anatenga dera lonse la Arigobi+ mpaka kumalire a Agesuri+ ndi a Amaakati,+ ndipo midzi ya ku Basana imeneyo anaitcha dzina la iye mwini lakuti, Havoti-yairi*+ kufikira lero. 15  Makiri+ ndinam’patsa Giliyadi.+ 16  Mafuko a Rubeni+ ndi Gadi ndinawapatsa dera lochokera ku Giliyadi+ kukafika kuchigwa cha Arinoni, ndipo malire anali pakati pa chigwacho. Dera limeneli linakafikanso kuchigwa cha Yaboki, amene ndi malire a ana a Amoni.+ 17  Ndinawapatsa Araba, Yorodano ndi tsidya lake la kum’mawa, kuchokera ku Kinereti*+ mpaka kunyanja ya Araba. Imeneyi ndi Nyanja Yamchere+ imene ili m’munsi mwa Pisiga,+ kotulukira dzuwa. 18  “Chotero ndinakulamulani pa nthawi imeneyo kuti, ‘Yehova Mulungu wanu wakupatsani dzikoli kuti mulitenge kukhala lanu. Amuna nonse olimba mtima muwoloke, mukuyenda patsogolo pa abale anu, ana a Isiraeli, muli okonzeka ndi zida.+ 19  Akazi anu okha ndi ana anu aang’ono ndiwo atsale m’mizinda yanu imene ndakupatsani.+ Ziweto zanunso zitsale (ndikudziwa kuti muli ndi ziweto zambiri), 20  kufikira Yehova atapatsa abale anu ndi inu nomwe mpumulo, ndiponso kufikira iwo atatenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akulipereka kwa iwo tsidya linalo la Yorodano. Mukatero mudzabwerera, aliyense kumalo ake amene ndakupatsani.’+ 21  “Pa nthawi imeneyo ndinalamula Yoswa+ kuti, ‘Iwe ukuona ndi maso zonse zimene Yehova Mulungu wanu wachita ndi mafumu awiriwa. Yehova adzachitanso chimodzimodzi ndi maufumu onse amene ali kumene mukuwolokera.+ 22  Amuna inu, musawaope amenewo, chifukwa Yehova Mulungu wanu ndiye akukumenyerani nkhondo.’+ 23  “Pa nthawi imeneyo ndinam’chonderera Yehova kuti atikomere mtima, ndipo ndinati, 24  ‘Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, inu ndinu amene mwayamba kuchititsa atumiki anu kuti aone ukulu wanu+ ndi dzanja lanu lamphamvu.+ Ndi mulungu winanso uti, kumwamba kapena padziko lapansi, amene akuchita ntchito ngati zanu, ndiponso ntchito zamphamvu ngati zanu?+ 25  Ndiloleni chonde ndiwoloke, kuti ndione dziko labwino+ limene lili kutsidya kwa Yorodano, dera lamapiri labwinoli+ ndi Lebanoni.’+ 26  Pamenepo Yehova anapitiriza kundikwiyira chifukwa cha inu,+ ndipo sanandimvere. Motero Yehova anandiuza kuti, ‘Basi khala chete! Usatchulenso nkhani imeneyi kwa ine. 27  Kwera pamwamba pa Pisiga+ ndi kukweza maso ako, ndipo uyang’ane kumadzulo, kumpoto, kum’mwera ndi kum’mawa, uone dzikolo ndi maso ako, chifukwa suwoloka Yorodano uyu.+ 28  Uike Yoswa kukhala mtsogoleri+ ndipo umulimbikitse ndi kumulimbitsa, chifukwa ndiye adzawolotsa+ anthuwa ndi kuwachititsa kulandira dziko limene ulionelo kukhala cholowa chawo.’+ 29  Zonsezi zinachitika tili m’chigwa moyang’anana ndi Beti-peori.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.
Dzinali limatanthauza “Midzi ya Mahema ya Yairi.”
“Kinereti” ndi dzina loyambirira la Nyanja ya Galileya.