Deuteronomo 28:1-68

28  “Ukamveradi mawu a Yehova Mulungu wako mwa kuonetsetsa kuti ukutsatira malamulo ake onse amene ndikukupatsa lero,+ Yehova Mulungu wako adzakukweza ndithu pamwamba pa mitundu yonse ya padziko lapansi.+  Madalitso onsewa adzakutsata ndi kukupeza+ chifukwa ukumvera mawu a Yehova Mulungu wako:  “Udzakhala wodalitsika mumzinda,+ udzakhala wodalitsika m’munda.+  “Chidzadalitsika chipatso cha mimba yako,+ chipatso cha m’dziko lanu, chipatso cha ziweto zako,+ ana a ng’ombe zako ndi ana a nkhosa zako.+  “Lidzadalitsika dengu lako+ ndi chiwiya chako chokandiramo ufa.+  “Udzadalitsika pa zochita zako zonse.+  “Yehova adzachititsa adani ako amene adzakuukira kugonja pamaso pako.+ Pobwera kwa iwe adzadutsa njira imodzi, koma pothawa pamaso pako, adzadutsa njira 7.+  Yehova adzaika madalitso pankhokwe+ ndi pa zochita zako zonse+ ndipo adzakudalitsa m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.  Yehova adzakukhazikitsani monga anthu ake oyera,+ monga mmene analumbirira kwa inu,+ chifukwa mwapitiriza kusunga malamulo+ a Yehova Mulungu wanu ndipo mwayenda m’njira zake. 10  Pamenepo mitundu yonse ya anthu padziko lapansi adzaona kuti mukutchedwa ndi dzina la Yehova,+ ndipo adzachita nanu mantha.+ 11  “Yehova adzachulukitsa chuma chako pa zipatso za mimba yako,+ zipatso za ziweto zako ndi zipatso za m’munda mwako,+ m’dziko limene Yehova analumbirira makolo ako kuti adzakupatsa.+ 12  Yehova adzakutsegulira kumwamba, nyumba yake yabwino yosungiramo zinthu, kuti akupatse mvula pa nyengo yake+ m’dziko lako ndi kuti adalitse ntchito iliyonse ya manja ako.+ Udzakongoza mitundu yambiri koma iwe sudzakongola kanthu kwa iwo.+ 13  Yehova adzakuchititsa kukhala kumutu osati kumchira. Pamenepo udzangokhala pamwamba+ ndipo sudzakhala m’munsi, chifukwa ukumvera malamulo+ a Yehova Mulungu wako amene ndikukupatsa lero kuti uwasunge ndi kuwatsatira. 14  Usapatuke pa mawu onse amene ndikukulamula lero, kupita kudzanja lamanja kapena lamanzere+ kuti utsatire milungu ina ndi kuitumikira.+ 15  “Mukapanda kumvera mawu a Yehova Mulungu wanu ndi kuonetsetsa kuti mukutsatira malamulo ake onse ndi mfundo zake zimene ndikukupatsani lero, matemberero otsatirawa adzakugwerani ndi kukupezani:+ 16  “Udzakhala wotembereredwa mumzinda,+ udzakhala wotembereredwa m’munda.+ 17  “Lidzakhala lotembereredwa dengu lako+ ndi chiwiya chako chokandiramo ufa.+ 18  “Chidzakhala chotembereredwa chipatso cha mimba yako,+ chipatso cha nthaka yako,+ ana a ng’ombe zako ndi ana a nkhosa zako.+ 19  “Udzakhala wotembereredwa pa zochita zako zonse.+ 20  “Yehova adzakutumizira matemberero,+ chisokonezo+ ndi chilango+ pa ntchito zako zonse zimene ukuyesa kugwira. Adzakuchitira zimenezi kufikira utafafanizidwa ndi kutha mofulumira, chifukwa cha kuipa kwa zochita zako popeza kuti wandisiya.+ 21  Yehova adzachititsa mliri kukumamatira kufikira atakufafaniza m’dziko limene ukupita kukalitenga kukhala lako.+ 22  Yehova adzakulanga ndi chifuwa chachikulu,+ kuphwanya kwa thupi koopsa, kutupa, kutentha thupi kwambiri, lupanga,+ mphepo yotentha yowononga mbewu+ ndi matenda a mbewu.+ Zimenezi zidzakusautsa kufikira utawonongeka. 23  Thambo limene lili pamwamba pa mutu wako lidzakhala ngati mkuwa, ndipo nthaka yako idzakhala ngati chitsulo.+ 24  Yehova adzakugwetsera mchenga ndi fumbi ngati mvula m’dziko lako. Adzakugwetsera zimenezi kuchokera kumwamba kufikira utafafanizika. 25  Yehova adzakuchititsani kuti mugonje pamaso pa adani anu.+ Pokamenyana nawo nkhondo mudzadutsa njira imodzi, koma pothawa pamaso pawo mudzadutsa njira 7. Mudzakhala chinthu chonyansa kwa mafumu onse a dziko lapansi.+ 26  Mitembo yanu idzakhala chakudya cha cholengedwa chilichonse chouluka m’mlengalenga ndi zilombo zakutchire, ndipo sipadzakhala woziopsa.+ 27  “Yehova adzakulanga ndi zithupsa za ku Iguputo,+ matenda a mudzi,* ziwengo ndi zotupa, ndipo sudzachira matenda amenewa. 28  Yehova adzakulanga ndi misala,+ khungu+ ndipo adzakuchititsa kudabwa kwambiri.+ 29  Udzafufuzafufuza masana ngati mmene wakhungu amafufuzirafufuzira mu mdima,+ ndipo sudzapambana. Iwe wekha udzakhala wodyeredwa ndi kulandidwa zinthu nthawi zonse, popanda wokupulumutsa.+ 30  Udzalonjeza kukwatira mkazi koma mwamuna wina adzamugwirira.+ Udzamanga nyumba koma sudzakhalamo.+ Udzabzala mitengo ya mpesa koma sudzadya zipatso zake.+ 31  Ng’ombe yako idzaphedwa iwe ukuona, koma nyama yake sudzadyako. Bulu wako adzalandidwa ndi achifwamba iwe ukuona, ndipo sudzamuonanso. Nkhosa yako idzaperekedwa kwa adani ako, koma sipadzakhala wokupulumutsa.+ 32  Ana ako aamuna ndi ana ako aakazi adzaperekedwa kwa anthu ena+ iwe ukuona ndipo udzawalakalaka nthawi zonse, koma manja ako adzakhala opanda mphamvu.+ 33  Anthu amene sunawadziwe adzadya zipatso za m’dziko lako ndi mbewu zako zonse.+ Motero udzakhala wodyeredwa ndi woponderezedwa nthawi zonse.+ 34  Pamenepo udzasokonezeka mutu chifukwa cha zimene maso ako adzaona.+ 35  “Yehova adzakulanga ndi zithupsa zonyeka m’mawondo onse ndi m’ntchafu monse. Matenda amenewa adzayambira kumapazi mpaka paliwombo, ndipo sudzachira.+ 36  Yehova adzakuyendetsa+ pamodzi ndi mfumu+ yako imene udzadziikira, kukupititsa ku mtundu umene iweyo kapena makolo ako simunaudziwe. Kumeneko udzatumikira milungu ina, yamtengo kapena yamwala.+ 37  Pamenepo udzakhala chodabwitsa,+ adzakupekera mwambi+ ndi kukutonza pakati pa mitundu yonse ya anthu amene Yehova adzakupititsako. 38  “Udzapita ndi mbewu zambiri kumunda, koma udzakolola zochepa+ chifukwa dzombe lidzadya mbewuzo.+ 39  Udzalimadi ndi kubzala mitengo ya mpesa, koma sudzakolola mphesa zake ndi kumwa vinyo,+ chifukwa mbozi zidzadya mpesawo.+ 40  Udzakhala ndi mitengo ya maolivi m’dera lako lonse, koma sudzadzola mafuta chifukwa maolivi ako adzayoyoka.+ 41  Udzabereka ana aamuna ndi ana aakazi, koma sadzapitiriza kukhala ako chifukwa adzatengedwa kupita ku ukapolo.+ 42  Mitengo yako yonse ndi zipatso za m’dziko lako zidzakhala za tizilombo ta mapiko tochita mkokomo. 43  Mlendo wokhala pakati panu adzapitirizabe kutukuka kukuposani, koma inuyo mudzapitirizabe kutsika pansi.+ 44  Iye adzakhala wokukongoza koma iweyo sudzatha kumukongoza.+ Iye adzakhala mutu koma iweyo udzakhala mchira.+ 45  “Matemberero onsewa+ adzakugwera, kukutsatira ndi kukupeza kufikira utafafanizika,+ chifukwa sunamvere mawu a Yehova Mulungu wako mwa kusunga malamulo ndi mfundo zake zimene anakupatsa.+ 46  Matembererowa adzapitiriza pa iwe ndi ana ako monga chizindikiro ndi cholosera mpaka kalekale,+ 47  chifukwa chakuti sunatumikire Yehova Mulungu wako mokondwera, ndi mtima wosangalala,+ pamene unakhala ndi zochuluka pa chilichonse.+ 48  Udzatumikira adani ako+ amene Yehova adzawatuma kuti akuukire. Udzawatumikira uli ndi njala,+ ludzu, usiwa ndiponso ukusowa china chilichonse. Adzakuveka goli lachitsulo m’khosi lako kufikira atakufafaniza.+ 49  “Yehova adzautsa mtundu wakutali, kumalekezero a dziko,+ mtundu umene chilankhulo chake sudzachimva.+ Mtunduwo udzakuukira monga mmene chiwombankhanga chimakhwathulira nyama yake,+ 50  mtundu wa nkhope yoopsa+ umene sudzaikira kumbuyo munthu wachikulire kapena kukondera mnyamata.+ 51  Iwo adzadya chipatso cha ziweto zako ndi zipatso za nthaka yako kufikira utafafanizidwa,+ ndipo sadzakusiyirako mbewu, vinyo watsopano kapena mafuta, mwana wa ng’ombe yako kapena mwana wa nkhosa yako kufikira atakuwonongeratu.+ 52  Chotero adzakuzungulirani m’mizinda yanu yonse kufikira mipanda yanu yaitali ndi yolimba kwambiri imene muzidzaidalira itagwa m’dziko lanu lonse. Adzakuzungulirani ndithu m’mizinda yanu yonse m’dziko lanu limene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.+ 53  Pamenepo udzadya chipatso cha mimba yako, mnofu wa ana ako aamuna ndi ana ako aakazi,+ amene Yehova Mulungu wako wakupatsa, chifukwa cha zovuta ndi nsautso zimene adani ako adzakupanikiza nazo. 54  “Koma mwamuna wolobodoka nkhongono ndi wachisasati* pakati panu, adzayang’ana ndi diso+ loipa m’bale wake, mkazi wake wokondedwa ndi ana ake aamuna amene atsala, 55  kuti asagawireko aliyense wa iwo mnofu uliwonse wa ana ake aamuna amene adzawadya. Adzatero poona kuti alibiretu china chilichonse, chifukwa cha zovuta ndi nsautso zimene mdani wanu adzakupanikizani nazo m’mizinda yanu yonse.+ 56  Ndipo mkazi wolobodoka nkhongono ndi wachisasati pakati panu, amene sanayesepo n’komwe kupondetsa phazi lake pansi chifukwa cha kuleredwa mwachisasati ndi kulobodoka nkhongono,+ ameneyu adzayang’ana ndi diso loipa mwamuna wake wokondedwa, mwana wake wamwamuna ndi mwana wake wamkazi. 57  Adzayang’ananso ndi diso loipa zotuluka m’mimba mwake pambuyo pobereka komanso ana ake aamuna amene iye anabereka,+ chifukwa adzawadya mseri pokhala wosowa chilichonse chifukwa cha zovuta ndi nsautso zimene mdani wanu adzakupanikizani nazo m’mizinda yanu.+ 58  “Ngati sudzatsatira mosamala mawu onse a chilamulo ichi olembedwa m’buku ili,+ kuti uziopa dzina laulemerero+ ndi lochititsa manthali,+ dzina lakuti Yehova,+ amene ndi Mulungu wako, 59  Yehova adzakulitsa kwambiri miliri yako ndi miliri ya ana ako. Miliri imeneyo idzakhala yaikulu kwambiri ndi yokhalitsa,+ ndipo udzagwidwa ndi matenda onyansa ndi okhalitsa.+ 60  Adzakubweretsera matenda onse a ku Iguputo amene unachita nawo mantha, ndipo adzakumamatira.+ 61  Kuwonjezera pamenepo, Yehova adzakubweretsera nthenda iliyonse ndi mliri uliwonse umene sunalembedwe m’buku la chilamulo ili, kufikira utafafanizika. 62  Ngakhale kuti mwachuluka ngati nyenyezi zakumwamba,+ mudzatsala ochepa+ chifukwa chosamvera mawu a Yehova Mulungu wanu. 63  “Chotero, monga mmene Yehova anasangalalira kuti akuchitireni zabwino ndi kukuchulukitsani,+ momwemonso adzasangalala kuti akuwonongeni ndi kukufafanizani.+ Pamenepo mudzatheratu m’dziko limene mukupita kukalitenga kukhala lanu.+ 64  “Yehova adzakumwazani mwa anthu a mitundu yonse kuchokera kumalekezero ena a dziko mpaka kumalekezero enanso a dziko.+ Kumeneko mukatumikira milungu ina imene inuyo kapena makolo anu simunaidziwe, milungu yamtengo ndi milungu yamwala.+ 65  Pakati pa mitundu imeneyo sudzakhala mwamtendere,+ ndipo sudzapeza malo oti phazi lako liponde kuti lipumulirepo. Kumeneko, Yehova adzakupatsa mtima wachinthenthe,+ adzachititsa maso ako+ khungu ndipo adzakutayitsa mtima. 66  Pamenepo moyo wako udzakhala pangozi yaikulu koopsa, ndipo udzakhala wamantha usiku ndi usana, moti sudzakhala wotsimikiza za moyo wako.+ 67  M’mawa udzanena kuti, ‘Zikanakhala bwino akanakhala madzulo!’ ndipo madzulo udzanena kuti, ‘Zikanakhala bwino ukanakhala m’mawa!’ chifukwa cha mantha amene adzagwira mtima wako, ndiponso chifukwa cha zimene maso ako adzaona.+ 68  Yehova adzakubwezerani ku Iguputo pa zombo kudzera njira imene ndinakuuzani kuti, ‘Simudzaionanso.’+ Kumeneko mudzalakalaka kudzigulitsa kwa adani anu kuti mukhale akapolo aamuna ndi aakazi,+ koma sipadzakhala wokugulani.”

Mawu a M'munsi

Ena amati “matenda a mdidi,” kapena “matenda otuluka thumbo.”
Munthu wosasatitsidwa ndi munthu wopusa chifukwa chakuti anamulera momulekerera ndipo sanaphunzire ntchito kapena zinthu zina zomuthandiza pamoyo wake.