Deuteronomo 25:1-19

25  “Amuna akakangana+ n’kupita kwa oweruza,+ oweruzawo azigamula mlanduwo. Wolungama azimuweruza kuti ndi wolungama ndipo woipa azimuweruza kuti ndi woipa.+  Ngati woipayo akuyenera kukwapulidwa,+ woweruza azilamula kuti woipayo amugoneke pansi, ndipo azim’kwapula+ pamaso pa woweruzayo. Azimukwapula zikoti zogwirizana ndi choipa chimene wachita.  Azimukwapula zikoti 40. Asapitirire pamenepo, kuopera kuti akapitiriza kumukwapula zikoti zambiri+ anganyazitse m’bale wako pamaso pako.  “Usamange ng’ombe pakamwa pamene ikupuntha mbewu.+  “Ngati amuna apachibale akukhala moyandikana, ndiyeno mmodzi n’kumwalira asanabereke mwana wamwamuna, mkazi wa womwalirayo asakwatiwe ndi mlendo wochokera m’banja lina. Mlamu wake apite kwa iye ndi kum’tenga kukhala mkazi wake, ndipo achite ukwati wa pachilamu.+  Mwana woyamba amene mkaziyo angabereke, atenge dzina la mwamuna womwalira uja,+ kuti dzina la m’bale wake lisafafanizike mu Isiraeli.+  “Ngati mwamunayo sakufuna kutenga mkazi wamasiye wa m’bale wakeyo, mkaziyo azinyamuka ndi kupita kuchipata kwa akulu+ ndi kuwauza kuti, ‘M’bale wa mwamuna wanga wakana kusunga dzina la m’bale wake mu Isiraeli. Sanavomereze kuchita ukwati wa pachilamu ndi ine.’  Pamenepo akulu a mzindawo amuitane ndi kulankhula naye. Iye aime pamaso pawo ndi kunena kuti, ‘Sindikufuna kutenga mkazi ameneyu.’+  Zikatero mkazi wamasiyeyo aziyandikira m’bale wa mwamuna wakeyo akuluwo akuona ndipo azim’vula nsapato+ ndi kumulavulira kumaso.+ Pamenepo azinena kuti, ‘Izi ndiye zoyenera kuchitikira munthu wokana kumanga nyumba ya m’bale wake.’+ 10  Ndiyeno mu Isiraeli monse azidziwika ndi dzina lakuti, ‘Nyumba ya amene anavulidwa nsapato uja.’ 11  “Amuna akamamenyana ndipo mkazi wa mmodzi mwa amunawo wabwera kudzalanditsa mwamuna wake m’manja mwa amene akumumenya, ndipo mkaziyo watambasula dzanja ndi kugwira mwamuna winayo kumaliseche,+ 12  uzidula dzanja la mkaziyo. Diso lako lisamve chisoni.+ 13  “M’thumba lako, usakhale ndi miyezo iwiri yosiyana yoyezera kulemera kwa chinthu,+ usakhale ndi muyezo waukulu ndi wina waung’ono. 14  Usakhale ndi miyezo iwiri yosiyana ya efa*+ m’nyumba yako, usakhale ndi muyezo waukulu ndi muyezo waung’ono. 15  Muyezo wako woyezera kulemera kwa chinthu uzikhala wolondola ndi woyenera. Muyezo wako wa efa uzikhala wolondola ndi woyenera kuti masiku ako achuluke m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.+ 16  Pakuti aliyense wochita zimenezi, aliyense wosachita chilungamo, n’ngonyansa kwa Yehova Mulungu wako.+ 17  “Muzikumbukira zimene Aamaleki anakuchitirani panjira pamene munali kutuluka mu Iguputo.+ 18  Iwo anakumana nanu panjira ndi kupha anthu oyenda movutika m’gulu lanu amene anali kumbuyo. Iwo anachita izi pamene munali olefuka ndi otopa ndipo sanaope Mulungu.+ 19  Motero Yehova Mulungu wanu akakupumitsani kwa adani anu onse okuzungulirani, m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti mulitenge kukhala cholowa chanu,+ mufafanize dzina la Amaleki pansi pa thambo.+ Musaiwale zimenezi.

Mawu a M'munsi

Muyezo umodzi wa efa ndi wofanana ndi chitini cha malita 22.