Deuteronomo 24:1-22

24  “Mwamuna akatenga mkazi kuti akhale mkazi wake, ndiyeno ngati mkaziyo sanamusangalatse chifukwa wam’peza ndi vuto linalake,+ azimulembera kalata yothetsera ukwati+ ndi kum’patsa m’manja mwake, n’kumuchotsa panyumba pake.+  Pamenepo mkaziyo azituluka m’nyumba ya mwamunayo ndi kukakhala mkazi wa mwamuna wina.+  Mwamuna wachiwiriyu akadana nayenso mkaziyo ndipo wamulembera kalata yothetsera ukwati n’kuiika m’manja mwake ndi kum’chotsa panyumba pake, kapena ngati mwamuna wachiwiriyu amene anam’tenga kukhala mkazi wake wamwalira,  mwamuna woyamba amene anam’chotsa uja sadzaloledwa kum’tenganso kuti akhale mkazi wake pambuyo poti waipitsidwa.+ Kuchita zimenezo n’konyansa pamaso pa Yehova, chotero usachimwitse dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa monga cholowa.  “Mwamuna akatenga mkazi watsopano,+ sayenera kukhala m’gulu lankhondo, ndiponso asakakamizidwe kuchita china chilichonse. Akhale kunyumba osachita zinthu zimenezi kwa chaka chimodzi kuti asangalatse mkazi amene watenga.+  “Munthu asalande mnzake mphero kapena mwala woperera monga chikole.+ Kumulanda zimenezi monga chikole ndiko kumulanda moyo.  “Munthu akaba+ mmodzi mwa abale ake, ana a Isiraeli, n’kumuchitira nkhanza ndiponso kum’gulitsa,+ wakuba munthuyo afe ndithu. Muzichotsa woipayo pakati panu.+  “Samalani ndi mliri wa khate+ ndi kuonetsetsa kuti mukuchita zonse zimene ansembe achilevi adzakulangizani.+ Muzichita mosamala zonse zimene ndawalamula.+  Muzikumbukira zimene Yehova Mulungu wanu anachitira Miriamu panjira mutatuluka m’dziko la Iguputo.+ 10  “Ukakongoza mnzako ngongole ya mtundu wina uliwonse,+ usamalowe m’nyumba yake kukatenga chimene walonjeza kukupatsa monga chikole.+ 11  Uziima panja, ndipo munthu amene wam’kongozayo azibweretsa yekha chikolecho kwa iwe, panjapo. 12  Ngati munthuyo ndi wovutika, usagone ndi chinthu chake chimene wakupatsa monga chikolecho.+ 13  Uzionetsetsa kuti wam’bwezera chikolecho dzuwa likangolowa,+ kuti akagone m’chovala chake.+ Pamenepo adzakudalitsa,+ ndipo udzakhala utachita chilungamo pamaso pa Yehova Mulungu wako.+ 14  “Usachitire chinyengo waganyu wovutika ndiponso wosauka n’kumubera, kaya akhale mmodzi wa abale ako kapena mmodzi mwa alendo okhala m’dziko lanu, amene ali m’mizinda yanu.+ 15  Uzim’patsa malipiro ake+ tsiku lililonse, ndipo dzuwa lisalowe usanam’patse malipiro ake chifukwa iye ndi wovutika. Iye akuyembekezera malipiro akewo mwachidwi, ndipo angafuule kwa Yehova chifukwa cha zimene iweyo wam’chitira,+ iwe n’kupezeka kuti wachimwa.+ 16  “Abambo asaphedwe chifukwa cha machimo a ana, ndipo ana asaphedwe chifukwa cha machimo a abambo.+ Aliyense aziphedwa chifukwa cha tchimo lake.+ 17  “Usapotoze chiweruzo cha mlandu wa mlendo+ kapena mlandu wa mwana wamasiye,*+ ndipo usalande mkazi wamasiye chovala chake monga chikole.+ 18  Uzikumbukira kuti unali kapolo m’dziko la Iguputo, ndipo Yehova Mulungu wako anakuwombola kumeneko.+ N’chifukwa chake ndikukulamula kuti uzichita zimenezi. 19  “Ukaiwala mtolo wa tirigu pokolola m’munda wako,+ usabwerere kukatenga mtolowo. Uzisiyira mlendo wokhala m’dziko lanu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye.+ Uzichita zimenezi kuti Yehova Mulungu wako akudalitse pa chilichonse chimene dzanja lako likuchita.+ 20  “Pokolola maolivi mwa kukwapula mitengo yake, usabwerere m’mbuyo kukaona ngati m’nthambi zake muli zipatso zotsala. Zimenezo zikhale za mlendo wokhala m’dziko lanu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye.+ 21  “Pokolola mphesa m’munda wako, usabwerere kukakunkha zotsala. Mphesa zotsalazo zikhale za mlendo wokhala m’dziko lanu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye. 22  Uzikumbukira kuti unali kapolo m’dziko la Iguputo.+ N’chifukwa chake ndikukulamula kuti uzichita zimenezi.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”