Deuteronomo 23:1-25

23  “Mwamuna wofulidwa+ mwa kuphwanya mavalo+ ake kapena woduka maliseche asalowe mumpingo wa Yehova.  “Mwana wapathengo+ asalowe mumpingo wa Yehova. Ana ake asalowe mumpingo wa Yehova kufikira m’badwo wa 10.  “Muamoni kapena Mmowabu asalowe mumpingo wa Yehova.+ Ana awo asalowe mumpingo wa Yehova kufikira m’badwo wa 10, ngakhalenso mpaka kalekale.  Chifukwa chake n’chakuti, sanakuthandizeni+ ndi mkate ndi madzi pamene munali pa ulendo mutatuluka mu Iguputo,+ ndiponso chifukwa chakuti analemba ganyu Balamu mwana wa Beori, amene kwawo ndi ku Petori ku Mesopotamiya kuti akutemberereni.+  Yehova Mulungu wanu sanafune kumvera Balamu,+ m’malomwake Yehova Mulungu wanu anakusinthirani temberero kukhala dalitso,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu anakukondani.+  Musachite kanthu kowathandiza kupeza mtendere ndi chitukuko masiku onse a moyo wanu, mpaka kalekale.+  “Usaipidwe ndi Mwedomu, chifukwa ndi m’bale wako.+ “Usaipidwe ndi Mwiguputo, chifukwa unali mlendo m’dziko lawo.+  Ana awo a m’badwo wachitatu angalowe mumpingo wa Yehova.  “Ukamanga msasa kuti umenyane ndi adani ako, uzidzipatula ku choipa chilichonse.+ 10  Pakati panu pakakhala mwamuna amene sali woyera chifukwa cha chodetsa chochitika usiku,+ azipita kunja kwa msasa. Asalowe mumsasamo.+ 11  Madzulo asambe ndipo dzuwa likalowa angathe kulowa mumsasa.+ 12  Muzikhala ndi malo obisika kunja kwa msasa kumene muzipita. 13  Uzikhalanso ndi chokumbira pamodzi ndi zida zako. Ndiyeno podzithandiza kunja kwa msasa, uzikumba dzenje ndi chokumbiracho ndipo ukamaliza kudzithandiza uzitembenuka ndi kufotsera zoipazo.+ 14  Pakuti Yehova Mulungu wanu akuyendayenda mumsasa wanu kuti akulanditseni+ ndi kupereka adani anu m’manja mwanu.+ Choncho msasa wanu uzikhala woyera,+ kuti asaone choipa chilichonse pakati panu ndi kutembenuka n’kuleka kuyenda nanu limodzi.+ 15  “Kapolo akathawira kwa iwe kuchokera kwa mbuye wake, usam’bweze kwa mbuye wakeyo.+ 16  Apitirize kukhala ndi iwe pakati panu, pamalo alionse amene iye angasankhe mu umodzi mwa mizinda yanu,+ kulikonse kumene wakonda. Usamamuzunze.+ 17  “Mwana wamkazi aliyense wachiisiraeli asakhale hule wa pakachisi,+ ndiponso mwana wamwamuna aliyense wachiisiraeli asakhale hule wa pakachisi.*+ 18  Usabweretse malipiro+ a hule kapena malipiro a galu*+ m’nyumba ya Yehova Mulungu wako kuti ukwaniritse lonjezo lililonse, chifukwa zonsezo ndi zonyansa kwa Yehova Mulungu wako. 19  “M’bale wako usamulipiritse chiwongoladzanja+ pa ndalama, chakudya+ kapena chilichonse chimene munthu angafunepo chiwongoladzanja. 20  Mlendo+ ungamulipiritse chiwongoladzanja, koma m’bale wako usamulipiritse chiwongoladzanja,+ kuti Yehova Mulungu wako akudalitse pa zochita zako zonse m’dziko limene ukupita kukalitenga kukhala lako.+ 21  “Ukapereka lonjezo kwa Yehova+ Mulungu wako usachedwe kulikwaniritsa kuopera kuti ungachimwe,+ chifukwa Yehova Mulungu wako adzafuna ndithu kuti ukwaniritse chimene walonjezacho.+ 22  Koma ukapanda kulonjeza, sunachimwe.+ 23  Uzisunga mawu a pakamwa pako+ ndipo uzikwaniritsa lonjezo limene unapereka kwa Yehova Mulungu wako monga nsembe yaufulu. Uzichita zimenezi chifukwa unalonjeza ndi pakamwa pako.+ 24  “Ukapita m’munda wa mpesa wa mnzako uzidya mphesa kungoti ukhute pa nthawiyo, koma usaike zina m’chotengera chako.+ 25  “Ukalowa m’munda wa tirigu wa mnzako, uzipulula ndi dzanja lako tirigu yekhayo amene wacha, koma usamwete tirigu wa mnzako ndi chikwakwa.+

Mawu a M'munsi

Kutanthauza mnyamata wosungidwira kugonedwa ndi amuna.
Mawu awa angatanthauze munthu amene makamaka amagona mnyamata kumbuyo.