Deuteronomo 22:1-30

22  “Ukaona ng’ombe kapena nkhosa ya m’bale wako ikusochera usaisiye mwadala.+ Uziikusa ndithu ndi kuipititsa kwa m’bale wako.+  Ngati mwiniwake sakhala pafupi ndi iwe ndiponso sukumudziwa, uzitengera chiwetocho kunyumba yako. Uzisunga chiwetocho kufikira mwiniwakeyo atafika kudzachifufuza ndipo uzim’bwezera.+  Uzichitanso chimodzimodzi ndi bulu wa m’bale wako, nsalu yake, kapena chilichonse chimene m’bale wako wataya iwe n’kuchipeza. Suyenera kungozisiya osazitola.  “Ukaona bulu wa m’bale wako kapena ng’ombe yake itagwa pamsewu usailekerere. Uzim’thandiza m’bale wako mwa kuidzutsa.+  “Mkazi asavale chovala cha mwamuna ndipo mwamuna asavale chovala cha mkazi,+ pakuti aliyense wochita zimenezi ndi wonyansa kwa Yehova Mulungu wanu.  “Ukapeza chisa cha mbalame mumtengo kapena pansi, muli ana+ kapena mazira, make atafungatira ana kapena mazirawo, usatenge make ndi ana omwe.+  Uonetsetse kuti wapitikitsa make, koma anawo ungathe kuwatenga. Uzichita zimenezi kuti zinthu zikuyendere bwino ndiponso kuti utalikitse masiku a moyo wako.+  “Ukamanga nyumba yatsopano uzimanganso kampanda padenga*+ la nyumbayo kuopera kuti ungaike mlandu wa magazi panyumba yako ngati munthu atagwa kuchokera padengapo.  “M’munda wako wa mpesa usabzalemo mbewu zamitundu iwiri,+ kuopera kuti ungakakamizike kupereka zokolola zako zonse ndi mphesa zako kumalo opatulika. 10  “Usamange ng’ombe ndi bulu kuti uzilimitse pamodzi.+ 11  “Usavale chovala chimene anachiwomba mophatikiza ubweya wa nkhosa ndi ulusi wa thonje.+ 12  “Uzimanga mphonje m’makona anayi a chovala chako.+ 13  “Mwamuna akatenga mkazi ndi kugona naye koma sakum’kondanso,+ 14  ndipo akumuimba mlandu wochita zinthu zonyansa ndi zochititsa manyazi, mwakuti wamuipitsira mbiri+ yake ponena kuti, ‘Ine ndinatenga mkazi uyu ndi kugona naye, koma sindinapeze umboni uliwonse woti anali namwali.’+ 15  Pamenepo bambo ndi mayi a mtsikanayo azibweretsa umboni wosonyeza kuti mtsikanayo anali namwali kwa akulu a mzinda kuchipata cha mzindawo.+ 16  Bambo a mtsikanayo aziuza akuluwo kuti, ‘Ine ndinapereka mwana wa mkazi kwa mwamuna uyu kuti akhale mkazi wake ndipo akumuda.+ 17  Pano akumuimba mlandu wochita zinthu zonyansa ndi zochititsa manyazi+ kuti: “Ndaona kuti palibe umboni wosonyeza kuti mwana wanuyu anali namwali.”+ Koma nawu umboni wa unamwali wa mwana wanga.’ Pamenepo azifunyulula chofunda pamaso pa akulu a mzinda. 18  Ndiyeno akulu+ a mzindawo azigwira mwamunayo ndi kum’langa.+ 19  Akatero azimulipiritsa masekeli* 100 asiliva, ndipo azipereka ndalamazo kwa bambo a mtsikanayo chifukwa waipitsa mbiri ya namwali wa mu Isiraeli.+ Mtsikanayo apitirize kukhala mkazi wake ndipo sadzaloledwa kumusiya ukwati masiku onse a moyo wake. 20  “Koma zimenezi zikatsimikizika kuti ndi zoona, palibedi umboni wa unamwali wa mtsikanayo,+ 21  azim’bweretsa mtsikanayo pakhomo la nyumba ya bambo ake ndipo amuna a mumzindawo azim’ponya miyala kuti afe, chifukwa wachita chinthu chopusa ndi chochititsa manyazi mu Isiraeli,+ mwa kuchita uhule m’nyumba ya bambo ake.+ Motero muzichotsa woipayo pakati panu.+ 22  “Mwamuna akapezeka akugona ndi mkazi wa mwiniwake,+ mwamuna ndi mkaziyo, onsewo azifera pamodzi. Mwamuna wogona ndi mkaziyo ndiponso mkaziyo azifera pamodzi.+ Motero uzichotsa oipawo mu Isiraeli.+ 23  “Pakakhala namwali wolonjezedwa kukwatiwa,+ ndipo mwamuna wina wam’peza mumzinda ndi kugona naye,+ 24  onsewo muziwabweretsa kuchipata cha mzindawo ndi kuwaponya miyala kuti afe. Mtsikanayo afe chifukwa chakuti sanakuwe mumzindawo ndipo mwamunayo afe chifukwa waipitsa mkazi wa mnzake.+ Motero muzichotsa oipawo pakati panu.+ 25  “Koma ngati mwamunayo wapeza mtsikana wolonjezedwa kukwatiwayo kuthengo ndipo wamugwira ndi kugona naye, mwamunayo afe yekha. 26  Mtsikanayo musam’chite chilichonse. Iye sanachite tchimo loyenera imfa, chifukwa mlanduwu ukufanana ndi wa munthu amene waukira mnzake ndi kumupha,+ kuchotsa moyo wake. 27  Popeza kuti anam’peza kuthengo, mtsikana wolonjezedwa kukwatiwayo anakuwa, koma panalibe womulanditsa. 28  “Mwamuna akapeza ndi kugwira mtsikana, namwali wosalonjezedwa kukwatiwa, n’kugona naye+ ndipo onsewo agwidwa,+ 29  mwamunayo azipereka masekeli 50 asiliva kwa bambo a mtsikanayo,+ ndipo akhale mkazi wake chifukwa chakuti wamunyazitsa. Sadzaloledwa kumusiya ukwati masiku onse a moyo wake.+ 30  “Pasapezeke mwamuna aliyense wotenga mkazi wa bambo ake kuopera kuti angavule bambo akewo.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “patsindwi.”
“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.