Deuteronomo 21:1-23
21 “Ukapeza munthu wakufa pathengo, m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa kuti ulitenge kukhala lako, ndipo amene wapha munthuyo sakudziwika,+
2 akulu ndi oweruza anu+ azipita kukayeza mtunda kuchokera pamene pali munthu wakufayo kukafika kumizinda yonse yozungulira malo amene munthuyo wapezekapo.
3 Ndipo azipeza mzinda umene uli pafupi ndi malo amene munthu wophedwayo wapezeka. Pamenepo akulu a mzinda wapafupiwo azitenga ng’ombe yaing’ono yaikazi imene sanaigwiritsepo ntchito, imene sinasenzepo goli n’kukoka chilichonse.
4 Pamenepo akulu a mzindawo azitenga ng’ombeyo ndi kutsikira nayo kuchigwa* chokhala ndi madzi ndithu, chigwa chimene sichinalimidwepo kapena kubzalidwa mbewu. Akafika kumeneko aziipha mwa kuithyola khosi.+
5 “Ansembe, ana a Levi, azifika pafupi chifukwa ndi amene Yehova Mulungu wanu wawasankha kuti am’tumikire+ ndi kudalitsa+ m’dzina la Yehova. Iwo ndiwo ayenera kuthetsa mkangano uliwonse wokhudza choipa chilichonse chimene chachitika.+
6 Ndiyeno akulu onse a mzinda umene uli pafupi ndi munthu wophedwayo azisamba m’manja+ pamwamba pa ng’ombe imene yathyoledwa khosi m’chigwa ija.
7 Pamenepo aziyankha kuti, ‘Manja athu sanakhetse magazi awa, ndiponso maso athu sanaone magaziwa akukhetsedwa.+
8 Musawerengere anthu anu Aisiraeli mlanduwu, anthu amene munawawombola,+ inu Yehova, ndipo musaike mlandu wa magazi osalakwa+ pakati pa anthu anu Aisiraeli.’ Akatero mlandu wa magaziwo usakhale pa iwo.
9 Ndipo inuyo mudzachotsa mlandu wa magazi a munthu wosalakwa pakati panu,+ chifukwa mudzakhala mutachita choyenera pamaso pa Yehova.+
10 “Ukapita kunkhondo kukamenyana ndi adani ako, ndipo Yehova Mulungu wako wawapereka m’manja mwako,+ iwe n’kuwagwira ndi kuwatenga,+
11 ndipo pakati pa anthu ogwidwawo waonapo mkazi wamaonekedwe okongola ndipo wakopeka+ naye ndi kum’tenga kuti akhale mkazi wako,
12 pamenepo uzim’tenga ndi kulowa naye m’nyumba yako. Kenako azimeta tsitsi lake+ ndi kusamalira zikhadabo zake.
13 Azisintha chovala chimene anavala pamene anali kugwidwa ndipo akhale m’nyumba mwako ndi kulira maliro a bambo ake ndi a mayi ake kwa mwezi wathunthu.+ Kenako umutenge kukhala mkazi wako. Akhale mkwatibwi wako ndipo ugone naye.
14 Ndiyeno ngati sukusangalala naye uzimulola kuchoka+ ngati iyenso akuvomereza, koma uonetsetse kuti usamugulitse ndi ndalama. Usam’chitire nkhanza+ pambuyo poti wamunyazitsa.
15 “Mwamuna akakhala ndi akazi awiri, wina wokondedwa ndi wina wosakondedwa, ndipo onse awiri, wokondedwa ndi wosakondedwayo, abereka ana aamuna ndi mwamunayo, koma mwana wa mkazi wosakondedwayo ndiye woyamba kubadwa,+
16 tsiku limene adzagawa zinthu zake monga cholowa kwa ana ake aamuna, sadzaloledwa kutenga mwana wamwamuna wa mkazi wokondedwa uja ngati mwana wake woyamba kubadwa m’malo mwa mwana wamwamuna wa mkazi wosakondedwayo, amene ndiyedi woyamba kubadwa.+
17 Pakuti ayenera kuvomereza kuti mwana wamwamuna wa mkazi wake wosakondedwayo ndiye woyamba kubadwa. Azivomereza mwa kum’patsa magawo awiri pa chilichonse chimene ali nacho,+ chifukwa mwanayo ndiye chiyambi cha mphamvu zake zobereka.+ Mwana ameneyo ndiye woyenera kulandira udindo wa mwana woyamba kubadwa.+
18 “Munthu akakhala ndi mwana wamwamuna wosamvera ndi wopanduka,+ amene samvera mawu a bambo ake kapena a mayi ake,+ ndipo amulangiza koma sawamvera,+
19 bambo ake ndi mayi ake azimugwira ndi kubwera naye kwa akulu, kuchipata cha mzinda umene akukhala,+
20 ndipo aziuza akulu a mzindawo kuti, ‘Mwana wathuyu ndi wosamvera ndiponso ndi wopanduka. Iye samvera mawu athu+ ndipo ndi wosusuka+ ndiponso ndi chidakwa.’+
21 Pamenepo amuna onse a mumzinda wawo azim’ponya miyala ndi kumupha. Muzichotsa woipayo pakati panu, ndipo Aisiraeli onse adzamva ndi kuchita mantha kwambiri.+
22 “Pakakhala munthu amene wachita tchimo loyenera chiweruzo choti aphedwe, ndiyeno munthuyo waphedwa,+ ndipo wam’pachika pamtengo,+
23 mtembo wake usakhale pamtengopo usiku wonse,+ koma uzionetsetsa kuti wamuika m’manda tsiku lomwelo, chifukwa aliyense wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa ndi Mulungu.+ Usaipitse nthaka yako imene Yehova Mulungu wako akukupatsa monga cholowa.+