Deuteronomo 20:1-20
20 “Mukapita kunkhondo kukamenyana ndi adani anu, musachite nawo mantha mukaona kuti ali ndi mahatchi ndi magaleta ankhondo,+ ndiponso mukaona kuti adani anuwo ndi ochuluka kwambiri kuposa inu. Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo ali ndi inu.+
2 Mukayandikira kuti mumenyane nawo, wansembe azifika pafupi nanu ndi kulankhula ndi anthu+
3 kuti, ‘Mverani Aisiraeli inu. Lero mukuyandikira adani anu kuti mumenyane nawo. Mitima yanu isachite mantha.+ Musaope ndipo musathawe mwamantha kapena kunjenjemera chifukwa cha iwo,+
4 chifukwa Yehova Mulungu wanu akuyenda limodzi nanu kuti akumenyereni nkhondo ndi kukupulumutsani kwa adani anu.’+
5 “Atsogoleri+ nawonso azilankhula ndi anthuwo kuti, ‘Kodi pali amene wamanga nyumba yatsopano koma sanaitsegulire? Achoke ndi kubwerera kunyumba yakeyo, kuopera kuti angafe pankhondo, ndipo munthu wina angatsegulire nyumbayo.+
6 Kodi pali amene walima munda wa mpesa koma sanayambe kukolola zipatso zake? Achoke ndi kubwerera kunyumba yake, kuopera kuti angafe pankhondo ndipo munthu wina angakolole za m’munda wakewo.+
7 Kodi pali amene analonjeza mkazi kuti adzamukwatira ndipo sanamutenge? Achoke ndi kubwerera kunyumba yake,+ kuopera kuti angafe pankhondo ndipo mwamuna wina angatenge mkaziyo.’
8 Ndiyeno atsogoleri apitirize kulankhula ndi anthuwo kuti, ‘Kodi pali wamantha ndi wosalimba mtima?+ Achoke ndi kubwerera kunyumba yake, kuti angachititse mantha mitima ya abale ake ngati mmene wachitira mtima wake.’+
9 Atsogoleriwo akamaliza kulankhula ndi anthu, azisankha akulu a magulu ankhondo oti akhale patsogolo pa anthuwo.
10 “Mukayandikira mzinda kuti mumenyane nawo, muzilengeza kumzindawo mfundo za mtendere.+
11 Ndiyeno ngati mzindawo wakupatsani yankho la mtendere ndipo akutsegulirani zipata zake, pamenepo anthu onse opezeka mmenemo azikhala anu kuti azikugwirirani ntchito yaukapolo. Iwo azikutumikirani.+
12 Koma ngati mzindawo sukukhazikitsa mtendere ndi inu,+ ndipo ukuchita nanu nkhondo, moti inuyo mwauzungulira,
13 Yehova Mulungu wanu adzaupereka ndithu m’manja mwanu, ndipo zikatero muzipha mwamuna aliyense ndi lupanga.+
14 Koma musaphe akazi, ana aang’ono,+ ziweto+ ndi chilichonse chopezeka mumzindawo. Muzifunkha+ zinthu zonse za mumzindawo ndipo muzidya zimene mwafunkha kwa adani anu amene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.+
15 “Muzichita zimenezi ndi mizinda yonse yakutali kwambiri ndi inu imene siili pakati pa mizinda ya mitundu iyi.
16 Mizinda yokhayi ya anthu awa a mitundu ina imene Yehova Mulungu wanu akukupatsani monga cholowa, ndi imene simuyenera kusiyamo chilichonse chopuma chili chamoyo,+
17 chifukwa muyenera kuwawononga ndithu. Mukawononge Ahiti, Aamori, Akanani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi,+ monga mmene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani.
18 Mukawawononge kuti asakakuphunzitseni kuchita zinthu zawo zonse zonyansa zimene achitira milungu yawo, kuti mungachimwire Yehova Mulungu wanu.+
19 “Mukazungulira mzinda kwa masiku ambiri mwa kumenyana nawo kuti muulande, musawononge mitengo yake mwa kuisamulira nkhwangwa. Muyenera kudya zipatso za mitengoyo, chotero simuyenera kuidula.+ Kodi mtengo wa m’munda ndi munthu kuti muwuukire?
20 Mungathe kuwononga mtengo wokhawo umene mukuudziwa kuti subereka zipatso zakudya. Mtengo woterowo mungaudule ndi kumangira mpanda wozungulira+ mzinda wa adani umene ukuchita nanu nkhondo, kufikira mzindawo utagwa.