Deuteronomo 18:1-22

18  “Ansembe achilevi, kapena kuti fuko lonse la Levi,+ asakhale ndi gawo kapena cholowa pakati pa Isiraeli. Iwo azidya nsembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova. Azidya cholowa chake.+  Choncho asalandire cholowa pakati pa abale awo. Yehova ndiye cholowa chawo,+ monga mmene anawauzira.  “Ndipo izi ndi zinthu zimene ansembe ayenera kulandira kuchokera kwa anthu. Amene akupereka nsembe ya ng’ombe kapena nkhosa, azipereka kwa wansembe mwendo wakutsogolo, nsagwada ndi chifu.  Uziperekanso gawo loyamba la mbewu zako, vinyo wako watsopano, mafuta ndi ubweya wa nkhosa wometedwa moyambirira.+  Pakuti iye ndi amene Yehova Mulungu wako wam’sankha pakati pa mafuko anu onse, kuti iye pamodzi ndi ana ake aimirire ndi kutumikira m’dzina la Yehova nthawi zonse.+  “Ngati Mlevi watuluka mu umodzi mwa mizinda yonse ya Isiraeli, umene iye anakhalamo kwa kanthawi,+ ndiyeno wabwera pamalo amene Yehova adzasankhe, chifukwa chakuti mtima wake walakalaka kukatumikira pamalopo,+  azitumikiranso m’dzina la Yehova Mulungu wake mofanana ndi abale ake onse Alevi, amene aimirira kumeneko pamaso pa Yehova.+  Ngakhale kuti wapeza chuma atagulitsa katundu wa makolo ake, gawo la chakudya chake lizikhala lofanana ndi ansembe onse.+  “Ukakalowa m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa, usakaphunzire kuchita zinthu zonyansa zimene anthu a mitundu imeneyo akuchita.+ 10  Pakati panu pasapezeke munthu wotentha mwana wake pamoto,*+ wolosera,+ wochita zamatsenga,+ woombeza,*+ wanyanga,+ 11  kapena wolodza* ena,+ aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu,+ wolosera zam’tsogolo+ kapena aliyense wofunsira kwa akufa.+ 12  Pakuti aliyense wochita zimenezi ndi wonyansa kwa Yehova. Ndipo chifukwa chakuti anthu a mitundu ina akuchita zimenezi, Yehova Mulungu wako akuwapitikitsa pamaso pako.+ 13  Ukhale wopanda cholakwa pamaso pa Yehova Mulungu wako.+ 14  “Mitundu imene ukuilanda dziko inali kumvera anthu ochita zamatsenga+ ndi olosera.+ Koma iwe, Yehova Mulungu wako sanakulole kuchita zimenezi.+ 15  Yehova Mulungu wanu adzakupatsani mneneri ngati ine, kuchokera pakati panu, kuchokera pakati pa abale anu, ndipo inu mudzamvere mneneri ameneyo.+ 16  Adzakupatsani mneneri poyankha zonse zimene munapempha Yehova Mulungu wanu ku Horebe, tsiku limene munasonkhana kuphiri.+ Munapempha kuti, ‘Tiloleni tisamvenso mawu a Yehova Mulungu wathu, ndipo tisaonenso moto waukulu uwu, kuopera kuti tingafe.’+ 17  Pamenepo Yehova anandiuza kuti, ‘Mawu onse amene iwo anena ali bwino.+ 18  Ndidzawapatsa mneneri ngati iwe kuchokera pakati pa abale awo.+ Ndidzaika mawu anga m’kamwa mwake,+ ndipo adzawauza zonse zimene ndidzamulamula.+ 19  Pamenepo munthu amene sadzamvera mawu anga amene iye adzalankhule m’dzina langa, adzayankha mlandu kwa ine.+ 20  “‘Koma mneneri amene adzadzikuza mwa kulankhula m’dzina langa mawu amene sindinamulamule kuti alankhule,+ kapena kulankhula m’dzina la milungu ina,+ mneneri ameneyo afe ndithu.+ 21  Mumtima mwako ukanena kuti: “Tidzadziwa bwanji kuti si Yehova amene walankhula mawuwo?”+ 22  Mneneri akalankhula m’dzina la Yehova, koma mawuwo sanachitike kapena kukwaniritsidwa, ndiye kuti si Yehova amene walankhula mawu amenewo.+ Mneneriyo walankhula mawu amenewo mwa iye yekha, modzikuza. Iwe usachite naye mantha.’+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Le 19:26.
Mawu ake enieni, “kudutsitsa pamoto.”
Mawu akuti ‘kulodza’ kapena ‘kuchisa’ amatanthauza kupweteka kapena kulepheretsa munthu kuchita chinachake mwa njira ya matsenga.