Deuteronomo 17:1-20

17  “Usapereke kwa Yehova Mulungu wako nsembe ya ng’ombe kapena nkhosa yokhala ndi chilema kapena vuto lililonse, chifukwa zimenezi ndi zonyansa kwa Yehova Mulungu wako.+  “Pakati panu pakapezeka mwamuna kapena mkazi wochita zinthu zoipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu, mu umodzi mwa mizinda yanu imene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, ndipo akuphwanya pangano la Mulungu,+  moti akupita kukalambira milungu ina ndi kuigwadira, kapena kugwadira dzuwa, mwezi kapena khamu lonse la zinthu zakuthambo,+ chinthu chimene ine sindinakulamuleni,+  ndipo inu mwamva mutauzidwa, ndiponso mutafufuza mwatsimikizira kuti ndi zoona,+ chinthu choipachi chachitikadi mu Isiraeli,  muzitulutsira mwamuna kapena mkazi wochita chinthu choipayo kunja kwa mzinda, ndipo muzim’ponya miyala kuti afe.+  Munthuyo aziphedwa mutamva umboni wa pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu.+ Asaphedwe chifukwa cha umboni wa munthu mmodzi.+  Dzanja la mbonizo lizikhala loyamba kum’ponya miyala kuti afe, ndipo anthu ena onse azibwera pambuyo.+ Choncho muzichotsa woipayo pakati panu.+  “Mlandu wofuna chigamulo ukakukulira kwambiri,+ monga mlandu wokhudza kukhetsa magazi,+ mlandu umene munthu wakasuma,+ mlandu wokhudza zachiwawa kapena mkangano+ umene wachitika mumzinda wanu, pamenepo uzinyamuka ndi kupita kumalo amene Yehova Mulungu wako adzasankhe.+  Uzipita kwa ansembe+ achilevi ndi kwa woweruza+ amene aziweruza m’masiku amenewo. Uziwafotokozera nkhaniyo ndipo iwo azikuuza chigamulo.+ 10  Zimene akuuza kumalo amene Yehova adzasankhe uzichita zomwezo. Uzionetsetsa kuti ukuchita zonse zimene akulangiza. 11  Uzichita mogwirizana ndi chilamulo chimene akupatsa ndi chigamulo chimene akuuza.+ Usapatukire kudzanja lamanja kapena lamanzere pa mawu amene akupatsa.+ 12  Munthu amene adzadzikuza mwa kusamvera wansembe amene akutumikira Yehova Mulungu wako kapena mwa kusamvera woweruza,+ munthu ameneyo afe ndithu.+ Muzichotsa woipayo mu Isiraeli.+ 13  Anthu onse adzamva zimenezo ndi kuchita mantha+ ndipo sadzadzikuzanso. 14  “Ukakafika m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa, n’kulitengadi kukhala lako ndi kukhalamo,+ pamenepo iwe n’kunena kuti, ‘Ndidziikire mfumu ngati mitundu ina yonse yondizungulira,’+ 15  uzidziikira mfumu imene Yehova Mulungu wako adzasankhe.+ Mfumu imene udzadziikire idzachokere pakati pa abale ako. Sudzaloledwa kudziikira mlendo amene si m’bale wako kukhala mfumu. 16  Koma asadzichulukitsire mahatchi+ kapena kuchititsa anthu kubwerera ku Iguputo kuti akakhale ndi mahatchi ochuluka+ pakuti Yehova wakuuzani kuti, ‘Musabwererenso kudzera njira iyi.’ 17  Asachulukitsenso akazi kuti mtima wake ungapatuke,+ ndipo asachulukitsenso kwambiri siliva ndi golide wake.+ 18  Akakhala pampando wachifumu, ayenera kukopera buku lakelake la chilamulo ichi, kuchokera m’buku limene ansembe achilevi amasunga.+ 19  “Buku limeneli azikhala nalo nthawi zonse ndipo aziliwerenga masiku onse a moyo wake,+ kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wake ndi kusunga mawu onse a chilamulo ichi, kutinso azitsatira malangizo ake.+ 20  Azichita zimenezi kuti mtima wake usadzikweze pamaso pa abale ake,+ komanso kuti asachoke pachilamulo mwa kupatukira kudzanja lamanja kapena lamanzere.+ Azichita zimenezi kuti iyeyo ndi ana ake atalikitse masiku a ufumu wawo+ mu Isiraeli.

Mawu a M'munsi