Deuteronomo 16:1-22

16  “Muzisunga mwambo wa m’mwezi wa Abibu*+ pochita chikondwerero cha pasika kwa Yehova Mulungu wanu,+ chifukwa m’mwezi wa Abibu Yehova Mulungu wanu anakutulutsani mu Iguputo usiku.+  Uzipereka nsembe ya pasika kwa Yehova Mulungu wako.+ Uzipereka nkhosa ndi ng’ombe+ pamalo amene Yehova adzasankhe kuikapo dzina lake.+  Usadye nsembeyo pamodzi ndi chilichonse chokhala ndi chofufumitsa. Masiku 7+ uzidya mkate wopanda chofufumitsa, umene ndi mkate wa nsautso, chifukwa unatuluka mofulumira m’dziko la Iguputo.+ Uzichita zimenezi kuti uzikumbukira tsiku limene unatuluka m’dziko la Iguputo, masiku onse a moyo wako.+  Usapezeke ndi mtanda wa ufa wokanda wokhala ndi chofufumitsa m’dziko lako lonse masiku 7.+ Nyama iliyonse imene wapereka nsembe madzulo, pa tsiku loyamba, isagone mpaka m’mawa.+  Sudzaloledwa kupereka nsembe ya pasika mumzinda wanu uliwonse umene Yehova Mulungu wako akukupatsa.  Koma uzipereka nsembe ya pasikayo pamalo amene Yehova Mulungu wako adzasankhe kuikapo dzina lake.+ Uzipereka nsembeyo madzulo, dzuwa likangolowa,+ pa nthawi yofanana ndi imene unatuluka mu Iguputo.  Uziiwotcha ndi kuidya+ pamalo amene Yehova Mulungu wako adzasankhe,+ ndipo m’mawa mwake uzitembenuka ndi kubwerera kumahema ako.  Kwa masiku 6, uzidya mkate wopanda chofufumitsa, ndipo pa tsiku la 7 uzichitira Yehova Mulungu wako+ msonkhano wapadera. Pa tsikuli usagwire ntchito.  “Uziwerenga masabata 7. Uziyamba kuwerenga masabata 7 amenewo kuchokera pamene wayamba kumweta tirigu.+ 10  Ndiyeno uzichitira Yehova Mulungu wako+ chikondwerero cha masabata, popereka nsembe zaufulu zimene ungathe, monga mmene Yehova Mulungu wako angakudalitsire.+ 11  Pamenepo uzisangalala pamaso pa Yehova Mulungu wako,+ iweyo, mwana wako wamwamuna, mwana wako wamkazi, kapolo wako wamwamuna, kapolo wako wamkazi, Mlevi wokhala mumzinda wanu, mlendo wokhala pakati panu,+ mwana wamasiye*+ ndi mkazi wamasiye,+ amene ali pakati panu. Muzisangalala pamalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe kuikapo dzina lake.+ 12  Uzikumbukira kuti unali kapolo ku Iguputo,+ ndipo uzisunga ndi kutsatira malamulo amenewa.+ 13  “Uzichita chikondwerero cha misasa+ masiku 7, potuta zokolola kuchokera pamalo opunthira mbewu, pamalo oyengera mafuta ndi pamalo opondera mphesa. 14  Ndipo uzisangalala pa chikondwerero chimenecho,+ iweyo, mwana wako wamwamuna, mwana wako wamkazi, kapolo wako wamwamuna, kapolo wako wamkazi, Mlevi, mlendo wokhala pakati panu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye, amene ali mumzinda wanu. 15  Uzichitira Yehova Mulungu wako chikondwerero chimenecho masiku 7+ pamalo amene Yehova adzasankhe. Uzichita chikondwerero chimenecho chifukwa Yehova Mulungu wako adzakudalitsa+ pa zokolola zako zonse ndi pa chilichonse chimene dzanja lako likuchita, ndipo iwe uzikhala wosangalala basi.+ 16  “Mwamuna aliyense pakati panu azikaonekera katatu pa chaka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, pamalo amene Mulungu adzasankhe.+ Azikaonekera pa chikondwerero cha mkate wopanda chofufumitsa,+ chikondwerero cha masabata+ ndi pa chikondwerero cha misasa.+ Palibe amene ayenera kuonekera kwa Yehova chimanjamanja.+ 17  Mphatso yochokera m’manja mwa aliyense izikhala yolingana ndi madalitso amene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.+ 18  “Mudziikire oweruza+ ndi atsogoleri+ m’mizinda yanu yonse imene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, malinga ndi mafuko anu. Oweruza ndi atsogoleriwo aziweruza anthu ndi chiweruzo cholungama. 19  Usamapotoze chiweruzo.+ Usamakondere+ kapena kulandira chiphuphu, chifukwa chiphuphu chimachititsa khungu maso a anthu anzeru+ ndi kupotoza mawu a anthu olungama. 20  Uzitsatira chilungamo.+ Ndithudi uzitsatira chilungamo kuti ukhale ndi moyo ndi kukatengadi dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.+ 21  “Usabzale mtengo wa mtundu uliwonse kuti ukhale mzati woti uziulambira pafupi ndi guwa lansembe la Yehova Mulungu wako limene udzadzipangira.+ 22  “Ndipo usadziimikire chipilala chopatulika,+ chinthu chimene Yehova Mulungu wako amadana nacho kwambiri.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 13.
Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”