Deuteronomo 14:1-29

14  “Inu ndinu ana a Yehova Mulungu wanu.+ Musamadzichekecheke+ kapena kumeta+ nsidze* zanu chifukwa cha anthu akufa.  Pakuti ndinu anthu oyera+ kwa Yehova Mulungu wanu, ndipo Yehova wakusankhani kuti mukhale anthu ake, chuma chake chapadera,+ mwa anthu onse okhala padziko lapansi.  “Musadye chinthu chilichonse chonyansa.+  Mitundu ya nyama zimene muyenera kudya ndi izi:+ ng’ombe, nkhosa, mbuzi,  mbawala yamphongo, insa, ngondo,+ mbuzi yakuthengo, mphalapala, nkhosa yakuthengo ndi chinkhoma.  Nyama iliyonse ya ziboda zogawanika, zokhala ndi mpata pakati imenenso imabzikula,+ imeneyo mungadye.  Simuyenera kudya mitundu iyi yokha mwa nyama zonse zimene zimabzikula kapena zokhala ndi ziboda zogawanika, zokhala ndi mpata pakati: ngamila,+ kalulu+ ndi mbira,+ chifukwa zimabzikula koma si zogawanika ziboda. Nyama zimenezi n’zodetsedwa kwa inu.  Musamadyenso nkhumba+ chifukwa ndi ya ziboda zogawanika koma sibzikula. Imeneyi ndi yodetsedwa kwa inu. Musamadye nyama yake ndipo ikafa musamaikhudze.+  “Mwa mitundu yonse ya zinthu zokhala m’madzi, zimene mungadye ndi izi: Chilichonse chokhala ndi zipsepse ndi mamba mungadye.+ 10  Chilichonse chimene chilibe zipsepse ndi mamba musadye.+ Chimenecho n’chodetsedwa kwa inu. 11  “Mbalame iliyonse yosadetsedwa mungadye. 12  Koma mbalame izi ndi zimene simuyenera kudya: chiwombankhanga, nkhwazi, muimba wakuda,+ 13  mphamba wofiira, mphamba wakuda+ ndi mtundu uliwonse wa kamtema. 14  Simuyeneranso kudya mtundu uliwonse wa khwangwala.+ 15  Musadyenso nthiwatiwa,+ kadzidzi, kakowa ndi mtundu uliwonse wa kabawi. 16  Musadyenso nkhwezule, mantchichi,+ tsekwe, 17  vuwo,+ muimba, chiswankhono, 18  dokowe, sadzu, mleme+ ndi mtundu uliwonse wa chimeza. 19  Tizilombo tonse ta mapiko timene timapezeka tambiri n’todetsedwa kwa inu.+ Timeneti simuyenera kudya. 20  Cholengedwa chilichonse chouluka chosadetsedwa mungadye. 21  “Musadye nyama iliyonse imene mwaipeza yakufa.+ Muziipereka kwa mlendo wokhala mumzinda wanu kuti adye, kapena muziigulitsa kwa mlendo* chifukwa inu ndinu anthu oyera kwa Yehova Mulungu wanu. “Musawiritse mwana wa mbuzi mumkaka wa mayi wake.+ 22  “Usalephere kupereka chakhumi cha mbewu zako zonse zokolola m’munda mwako chaka ndi chaka.+ 23  Uzidzadya zinthu zako pamaso pa Yehova Mulungu wako, pamalo amene iye adzasankhe kuikapo dzina lake. Uzidzadya chakhumi cha mbewu zako,+ kumwa vinyo wako watsopano, kudya mafuta ako, ana oyamba a ng’ombe ndi a nkhosa zako.+ Uzichita zimenezi kuti uphunzire kuopa Yehova Mulungu wako nthawi zonse.+ 24  “Ndiyeno ulendo ukakhala wautali kwa iwe,+ ndipo sungathe kunyamula chakhumicho, popeza malo amene Yehova Mulungu wako adzasankhe kuikapo dzina lake+ ali kutali ndi iwe (chifukwa Yehova Mulungu wako adzakudalitsa,)+ 25  uzidzagulitsa chakhumicho ndipo uzidzatenga ndalamazo ndi kuzifumbata m’manja mwako popita kumalo amene Yehova Mulungu wako adzasankhe. 26  Ndalamazo udzagulire chilichonse chimene mtima wako wakhumba,+ kaya ndi ng’ombe, nkhosa, mbuzi, vinyo, chakumwa choledzeretsa+ ndi chilichonse chimene mtima wako wafuna. Ndipo uzidzadya zinthuzi pamaso pa Yehova Mulungu wako ndi kukondwera,+ iweyo ndi banja lako. 27  Mlevi wokhala mumzinda wanu usamutaye,+ pakuti alibe gawo kapena cholowa monga iwe.+ 28  “Kumapeto kwa zaka zitatu uzidzabweretsa chakhumi cha zokolola zako zonse m’chaka chimenecho,+ ndipo uzidzachisiya mkati mwa mzinda wanu. 29  Ndiyeno Mlevi,+ popeza alibe gawo kapena cholowa monga iwe, komanso mlendo wokhala pakati panu,+ mwana wamasiye* ndi mkazi wamasiye+ wokhala mumzinda wanu, azibwera kudzadya ndi kukhuta kuti Yehova Mulungu wako akudalitse+ pa chilichonse+ chimene dzanja lako likuchita.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “kumeta mpala pachipumi panu.”
Mawu ake enieni, “munthu amene si Mwisiraeli.”
Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”