Deuteronomo 12:1-32
12 “Awa ndi malangizo+ ndi zigamulo+ zimene muyenera kuzitsatira mosamala,+ masiku onse amene mudzakhala m’dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu adzakulolani kuti mulitenge kukhala lanu.+
2 Mudzawononge+ malo onse amene ali pamapiri ataliatali, pazitunda ndi pansi pa mitengo ikuluikulu ya masamba obiriwira, pamene mitundu imene mukukailanda dziko lawo imatumikirirapo milungu yawo.+
3 Mudzagwetse maguwa awo ansembe+ ndi kuphwanya zipilala zawo zopatulika.+ Mudzatenthe mizati yawo yopatulika+ ndi kudula zifaniziro zogoba+ za milungu yawo, ndipo mudzafafanize mayina awo pamalo amenewo.+
4 “Musapembedze Yehova Mulungu wanu m’njira imeneyi,+
5 koma mudzafunefune malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe pakati pa mafuko anu onse kuti aikepo dzina lake, kuti lizikhala pamenepo. Amenewo ndiwo malo amene muzidzapitako.+
6 Nsembe zanu zopsereza+ ndi nsembe zina, zopereka zanu za chakhumi,*+ chopereka chochokera m’manja mwanu,+ nsembe zanu za lonjezo,+ nsembe zanu zaufulu,+ ana oyamba kubadwa a ng’ombe ndi a nkhosa zanu,+ zonsezi muzidzazibweretsa kumalo amenewo.
7 Kumalo amenewo, inuyo ndi mabanja anu muzidzadya zimenezi ndi kusangalala ndi zochita zanu zonse+ pamaso pa Yehova,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu wakudalitsani.
8 “Musakachite zimene tikuchita kuno lero, aliyense kumangochita zimene akufuna,+
9 chifukwa simunafike kumalo anu a mpumulo+ ndi kulandira cholowa chimene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.
10 Choncho muwoloke Yorodano+ ndi kukhala m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kukhala lanu.+ Iye adzakupumitsani kwa adani anu onse okuzungulirani, ndipo mudzakhaladi otetezeka.+
11 Ndiyeno malo+ amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kuti pakhale dzina lake n’kumene muzidzabweretsa zonse zimene ndikukulamulani, nsembe zanu zopsereza+ ndi nsembe zina, zopereka zanu za chakhumi,+ chopereka+ chochokera m’manja mwanu ndi zonse zimene mwasankha kukhala nsembe zanu za lonjezo,+ zimene mudzalonjeza Yehova.
12 Ndipo muzisangalala pamaso pa Yehova Mulungu wanu,+ inuyo ndi ana anu aamuna, ana anu aakazi, akapolo anu aamuna, akapolo anu aakazi ndi Mlevi wokhala mumzinda wanu, chifukwa iye alibe gawo kapena cholowa monga inu.+
13 Samalani kuti musadzapereke nsembe zanu zopsereza pamalo ena alionse amene mungaone.+
14 Koma muzidzapereka nsembe zanu zopsereza pamalo amene Yehova adzasankhe mu limodzi la mafuko anu, ndipo muzichita zonse zimene ndakulamulani pamalo amenewo.+
15 “Muzipha chiweto chanu ndi kudya nyama yake nthawi iliyonse imene mwafuna.+ Muzidya nyamayo malinga ndi dalitso limene Yehova Mulungu wanu wakupatsani m’mizinda yanu yonse. Munthu wodetsedwa+ komanso munthu woyera ali ndi ufulu wakudya nyamayo, monga mmene amadyera insa ndi mbawala yamphongo.+
16 Koma musadye magazi ake.+ Muziwathira panthaka ngati madzi.+
17 Simudzaloledwa kudyera m’mizinda yanu chakhumi cha mbewu zanu,+ vinyo wanu watsopano, mafuta anu, ana oyamba kubadwa a ng’ombe zanu ndi a nkhosa zanu,+ iliyonse mwa nsembe zanu za lonjezo zimene mudzalonjeza, nsembe zanu zaufulu+ kapena chopereka chochokera m’manja mwanu.+
18 Koma udzazidyera pamaso pa Yehova Mulungu wako, pamalo amene Yehova Mulungu wako adzasankhe.+ Udzazidyera pamalowo iweyo, mwana wako wamwamuna, mwana wako wamkazi, kapolo wako wamwamuna, kapolo wako wamkazi ndi Mlevi wokhala mumzinda wanu. Ndipo uzidzasangalala+ pamaso pa Yehova Mulungu wako pa zochita zako zonse.
19 Samala kuti usataye Mlevi+ masiku onse amene udzakhala m’dzikolo.
20 “Yehova Mulungu wako akadzafutukula malire a dziko lako+ monga mmene wakulonjezera,+ ndipo iwe n’kudzanena kuti, ‘Ndikufuna kudya nyama,’ chifukwa walakalaka kudya nyama, nthawi iliyonse imene mtima wako walakalaka kudya nyama uzidzadya.+
21 Ndiyeno malo amene Yehova Mulungu wako adzasankha kuikapo dzina lake+ akadzakhala kutali kwambiri ndi iwe, uzidzapha zina mwa ng’ombe zako kapena zina mwa nkhosa zako zimene Yehova wakupatsa, monga mmene ndakulamulira, ndipo uzidzadyera mumzinda mwako nyamazo, nthawi iliyonse imene mtima wako wafuna.+
22 Uzidzaidya mmene ungadyere insa ndi mbawala yamphongo.+ Munthu wodetsedwa+ komanso munthu woyera ali ndi ufulu wakudya nyamayo.
23 Koma ungokhala wotsimikiza mtima kwambiri kusadya magazi,+ chifukwa magazi ndiwo moyo,+ ndipo suyenera kudya nyama pamodzi ndi moyo wake.
24 Usadye magazi. Uziwathira pansi ngati madzi.+
25 Usadye magazi, kuti zinthu zikuyendere bwino iweyo+ ndi ana ako obwera m’mbuyo mwako, chifukwa ukatero udzachita choyenera pamaso pa Yehova.+
26 Pobwera kumalo amene Yehova adzasankhe,+ uzingotenga zinthu zako zopatulika+ zokapereka nsembe, ndi nsembe zako za lonjezo.+
27 Ukatero uzipereka nsembe zako zopsereza,+ nyama ndi magazi,+ paguwa lansembe la Yehova Mulungu wako. Magazi a nsembe zako uziwathira pansi pafupi ndi guwa lansembe la Yehova+ Mulungu wako, koma nyamayo utha kuidya.
28 “Samala. Uzimvera mawu onsewa amene ndikukuuza,+ kuti zinthu zikuyendere bwino+ mpaka kalekale, iweyo ndi ana ako aamuna obwera m’mbuyo mwako, chifukwa ukatero udzachita chabwino ndi choyenera pamaso pa Yehova Mulungu wako.+
29 “Yehova Mulungu wako akadzawononga ndi kuchotsa pamaso pako mitundu imene ukupita kukailanda dziko,+ ukailandedi dziko lawolo ndi kukhalamo.+
30 Samala kuti usagwidwe mumsampha wawo,+ pambuyo poti awonongedwa ndi kuchotsedwa pamaso pako, kutinso usafufuze za milungu yawo kuti, ‘Kodi mitundu imeneyi inali kutumikira bwanji milungu yawo? Ndithudi inenso ndidzachita zomwezo.’
31 Usapembedze Yehova Mulungu wako m’njira imeneyi,+ pakuti iwo amachitira milungu yawo zonse zimene zili zonyansa kwa Yehova, zimene iye amadana nazo. Pakuti iwo nthawi zonse amatentha ana awo aamuna ndi aakazi pamoto monga nsembe kwa milungu yawo.+
32 Muzichita mosamala mawu onse amene ndikukuuzani.+ Musawonjezepo kapena kuchotsapo kalikonse.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti “gawo limodzi mwa magawo 10.”