Deuteronomo 11:1-32

11  “Nthawi zonse uzikonda Yehova Mulungu wako+ ndi kuchita zofuna zake, kutsatira mfundo zake, zigamulo zake+ ndi malamulo ake.  Inuyo mukudziwa bwino lero, (sindikulankhulatu ndi ana anu amene sanadziwe ndi kuona chilango* cha Yehova+ Mulungu wanu, ukulu wake+ ndi dzanja lake lamphamvu+ ndi mkono wake wotambasula,+  kapena zizindikiro ndi zochita zake zimene anachita pakati pa dziko la Iguputo+ kwa Farao mfumu ya Iguputo, ndi zimene anachitira dziko lake lonse.  Amenenso sanaone zimene Mulungu anachitira gulu lankhondo la Aiguputo, mahatchi* ake ndi magaleta* ake ankhondo, amene anawamiza m’madzi a m’Nyanja Yofiira pamene anali kukuthamangitsani,+ ndipo Yehova anawononga Iguputo moti ndi mmene zilili kufikira lero.+  Sindikulankhula ndi ana anu amene sanaone zimene Mulungu wakuchitirani m’chipululu kudzafika malo ano,  kapena zimene anachitira Datani ndi Abiramu,+ ana a Eliyabu, mwana wa Rubeni, pamene dziko linatsegula pakamwa pake ndi kuwameza pamodzi ndi mabanja awo, mahema awo, ndi chamoyo china chilichonse chimene chinali pakati pawo. Dziko linawameza ali pakati pa Aisiraeli onse).+  Pakuti inu munaona ndi maso anu zochita zonse zazikulu zimene Yehova anachita.+  “Chotero muzisunga malamulo onse+ amene ndikukupatsani lero, kuti mukhale amphamvu ndi kuti mulowedi m’dziko limene mukuwolokerako ndi kulitenga kukhala lanu,+  kutinso mutalikitse masiku anu+ m’dziko limene Yehova analumbirira makolo anu kuti adzawapatsa iwowo ndi mbewu yawo,+ dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ 10  “Pakuti dziko limene mukupita kukalitenga kukhala lanu, si lofanana ndi dziko la Iguputo limene munatulukamo. Kumeneko munali kufesa mbewu zanu ndi kuzithirira ndi mapazi* anu, ngati kuti mukuthirira dimba la ndiwo zamasamba. 11  Koma dziko limene mukuwolokerako kuti mukalitenge kukhala lanu ndi dziko lamapiri ndi zigwa.+ Ilo limamwa madzi a mvula, madzi ochokera kumwamba. 12  Limenelo ndi dziko limene Yehova Mulungu wanu akulisamalira. Nthawi zonse maso+ a Yehova Mulungu wanu amakhala padziko limeneli, kuyambira kuchiyambi kwa chaka mpaka kumapeto. 13  “Ndiyeno mukadzamveradi malamulo anga+ amene ndikukupatsani lero, moti n’kukonda Yehova Mulungu wanu ndi kum’tumikira ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse,+ 14  iyenso* adzakupatsani mvula pa nthawi yake m’dziko lanu,+ mvula yoyambirira ndi mvula yomaliza,+ ndipo mudzakololadi mbewu zanu ndi kukhaladi ndi vinyo wotsekemera* komanso mafuta. 15  Adzameretsanso msipu m’dziko lanu kuti ziweto zanu zidye,+ ndipo inu mudzadya ndi kukhuta.+ 16  Samalani kuti mitima yanu isakopeke+ ndipo musapatuke ndi kupembedza milungu ina n’kumaiweramira.+ 17  Mukatero mkwiyo wa Yehova udzakuyakirani. Adzatseka kumwamba moti mvula sidzagwa+ ndipo nthaka sidzatulutsa zipatso zake. Pamenepo mudzafafanizika mwamsanga m’dziko labwinolo limene Yehova akukupatsani.+ 18  “Chotero mawu angawa muwasunge m’mitima yanu+ ndi kuwatsatira m’moyo wanu. Muwamange monga chizindikiro padzanja lanu, ndipo akhale ngati chomanga pamphumi panu.*+ 19  Ana anu muwaphunzitsenso mawu amenewa, ndipo muzilankhula nawo za mawuwa mukakhala pansi m’nyumba mwanu, poyenda pamsewu, pogona ndi podzuka.+ 20  Muziwalemba pamafelemu a nyumba zanu ndi pazipata za mzinda wanu,+ 21  kuti masiku anu ndi masiku a ana anu achuluke+ m’dziko limene Yehova analumbirira makolo anu kuti adzawapatsa,+ kuti masikuwo achuluke monga masiku a thambo lokhala pamwamba pa dziko.+ 22  “Mukasungadi malamulo onsewa+ amene ndikukupatsani, kukonda Yehova Mulungu wanu,+ kuyenda m’njira zake zonse+ ndi kum’mamatira,+ 23  Yehova adzachotsa mitundu yonseyi chifukwa cha inu,+ ndipo mitundu yamphamvu ndi yaikulu kuposa inu mudzailanda dziko.+ 24  Malo alionse amene mapazi anu adzapondapo adzakhala anu.+ Malire a dziko lanu adzayambira kuchipululu kukafika ku Lebanoni, kuyambira ku mtsinje wa Firate, kukafika kunyanja ya kumadzulo.+ 25  Palibe munthu amene adzaima kuti alimbane nanu.+ Yehova Mulungu wanu adzachititsa dziko lonse limene mudzapondapo kugwidwa ndi mantha aakulu ndi kukuopani,+ monga mmene anakulonjezerani. 26  “Onani, ndikukuikirani pamaso panu lero dalitso ndi temberero:+ 27  dalitsoli mudzalilandira malinga ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu,+ omwe ndikukupatsani lero, 28  ndipo mudzalandira temberero+ limeneli ngati simudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu,+ n’kupatuka panjira imene ndikukulamulani lero kuti muziyendamo, n’kuyamba kutsatira milungu ina imene simukuidziwa. 29  “Ndiyeno Yehova Mulungu wanu akadzakulowetsani m’dziko limene mukupita kukalitenga kuti likhale lanu,+ mukatchule dalitsoli paphiri la Gerizimu+ ndipo temberero mukalitchulire paphiri la Ebala.+ 30  Si paja mapiri amenewa ali kuchigawo chotulukira dzuwa cha Yorodano, m’dziko la Akanani okhala mu Araba,+ moyang’anizana ndi Giligala,+ pafupi ndi mitengo ikuluikulu ya ku More?+ 31  Pakuti mukuwoloka Yorodano ndi kukalowa m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti mulitenge kukhala lanu. Mukalitengedi ndi kukhala momwemo.+ 32  Chotero muzisunga mosamala malangizo onse ndi zigamulo zonse+ zimene ndikuika pamaso panu lero.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2
Ena amati “mahosi” kapena “akavalo.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kutanthauza kuti, kuthirira pogwiritsa ntchito mapazi, mwina mwa kupalasa gudumu lotungira madzi kapena mwa kutsegula ndi kutseka ngalande ndi mapazi.
Mawu ake enieni, “Ine,” kutanthauza Mulungu.
Ena amati “wonzuna.”
Onani mawu a m’munsi pa De 6:8.