Deuteronomo 10:1-22

10  “Pa nthawi imeneyo Yehova anandiuza kuti, ‘Dzisemere miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija,+ ndipo udzipangire likasa lamatabwa.+ Ukatero ukwere m’phiri muno kwa ine.  Pamiyalayo ndidzalembapo mawu amene anali pamiyala yoyamba ija, imene unaswa, ndipo udzaiike m’likasalo.’  Choncho ndinapanga likasa la mtengo wa mthethe ndi kusema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija.+ Kenako ndinakwera m’phiri, miyala iwiriyo ili m’manja mwanga.  Pamenepo analemba pamiyalayo mawu ofanana ndi oyamba aja,+ Mawu Khumi,*+ amene Yehova anakuuzani m’phiri kuchokera pakati pa moto,+ tsiku limene munasonkhana kuphiri.+ Atatero, Yehova anandipatsa miyalayo.  Ndiyeno ndinatembenuka, n’kutsika m’phirimo,+ ndipo ndinaika miyala iwiriyo m’likasa limene ndinapanga kuti izikhala mmenemo, monga mmene Yehova anandilamulira.+  “Pamenepo ana a Isiraeli ananyamuka kuchoka ku Beeroti Bene-yaakana+ kupita ku Mosera. Aroni anafera kumalo amenewo, ndipo anamuikanso kumeneko.+ Mwana wake Eleazara anayamba kutumikira monga wansembe m’malo mwa Aroniyo.+  Ndiyeno ananyamuka pamalo amenewo kupita ku Gudigoda. Anachokanso ku Gudigoda kupita ku Yotibata,+ dziko la zigwa* zokhala ndi madzi ndithu.  “Pa nthawi imeneyo, Yehova anapatula fuko la Levi+ kuti lizinyamula likasa la pangano la Yehova,+ liziima pamaso pa Yehova pom’tumikira,+ ndi kuti lizidalitsa m’dzina lake kufikira lero.+  N’chifukwa chake Levi alibe gawo ndiponso cholowa+ monga abale ake. Yehova ndiye cholowa chake, monga mmene Yehova Mulungu wanu anamuuzira.+ 10  Ndipo ine ndinakhala m’phirimo masiku ofanana ndi oyamba aja, masiku 40, usana ndi usiku,+ ndipo Yehova anandimveranso pa nthawi imeneyi.+ Yehova sanafune kukuwonongani.+ 11  Kenako Yehova anandiuza kuti, ‘Nyamuka, tsogolera anthu kuti ayambe ulendo, kuti akalowe ndi kutenga dziko limene ndinalumbirira makolo awo kuti ndidzawapatsa.’+ 12  “Tsopano Aisiraeli inu, kodi Yehova Mulungu wanu akufuna kuti muzichita chiyani,+ koposa kuopa+ Yehova Mulungu wanu kuti muziyenda m’njira zake zonse,+ kukonda+ ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse,+ 13  kuti muzisunga malamulo a Yehova ndi mfundo zake+ zimene ndikukupatsani lero, kuti zinthu zikuyendereni bwino?+ 14  Taonani, kumwamba ndi kwa Yehova Mulungu wanu,+ kumwambamwamba ndi zonse zili kumeneko, dziko lapansi+ ndi zonse zili mmenemo ndi zake zonsezo. 15  Koma Yehova anadziphatika kwa makolo anu ndi kuwakonda, moti anasankha ana awo obadwa m’mbuyo mwawo,+ inuyo, pakati pa anthu onse monga mmene zilili lero. 16  Mitima yanu muichite mdulidwe+ ndipo musakhalenso ouma khosi.+ 17  Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wa milungu+ ndi Mbuye wa ambuye.+ Iye ndi Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa,+ amene sakondera+ munthu aliyense ndipo salandira chiphuphu.+ 18  Iye amaperekera chiweruzo ana amasiye* ndi akazi amasiye,+ ndipo amakonda mlendo wokhala pakati panu+ moti amam’patsa mkate ndi chofunda. 19  Inunso muzikonda mlendo wokhala pakati panu,+ chifukwa munali alendo m’dziko la Iguputo.+ 20  “Muziopa Yehova Mulungu wanu.+ Muzim’tumikira,+ kum’mamatira+ ndi kulumbira pa dzina lake.+ 21  Iye ndi amene muyenera kum’tamanda,+ ndipo iye ndi Mulungu wanu amene wakuchitirani zinthu zazikulu ndi zochititsa mantha, zimene mwaziona ndi maso anu.+ 22  Makolo anu anapita ku Iguputo ndi anthu 70,+ ndipo tsopano Yehova Mulungu wanu wakuchulukitsani ngati nyenyezi zakuthambo.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Eks 34:28.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”