Deuteronomo 1:1-46

1  Awa ndiwo mawu amene Mose analankhula ndi Aisiraeli onse m’chipululu, m’chigawo cha Yorodano,+ m’chipululu moyang’anana ndi Sufu, pakati pa Parana,+ Tofeli, Labani, Hazeroti+ ndi Dizahabi,  mtunda woyenda masiku 11 kuchokera ku Horebe kudzera njira ya kuphiri la Seiri yopita ku Kadesi-barinea.+  Ndiyeno m’chaka cha 40,*+ m’mwezi wa 11, pa tsiku loyamba la mweziwo, Mose analankhula ndi ana a Isiraeli zonse zimene Yehova anamulamula kuti awauze.  Apa n’kuti atagonjetsa Sihoni+ mfumu ya Aamori imene inali kukhala ku Hesiboni. Anali atagonjetsanso Ogi+ mfumu ya Basana imene inali kukhala ku Asitaroti.+ Mfumu imeneyi anaigonjetsera ku Edirei.+  Mose anayamba kufotokoza chilamulo ichi+ m’chigawo cha Yorodano m’dziko la Mowabu, kuti:  “Yehova Mulungu wathu anatilankhula tili ku Horebe,+ kuti, ‘Mwakhalitsa m’dera lino lamapiri.+  Tembenukani ndi kulowera kudera lamapiri la Aamori+ ndi anthu oyandikana nawo onse okhala ku Araba,+ kudera lamapiri,+ ku Sefela, ku Negebu,+ m’mbali mwa nyanja,+ m’dziko la Akanani+ ndi ku Lebanoni+ mpaka kumtsinje waukulu wa Firate.+  Taonani, ndikukupatsani dzikolo. Mukalowe m’dzikolo ndi kulitenga kuti likhale lanu, dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abulahamu, Isaki+ ndi Yakobo,+ kuti adzalipereka kwa iwo ndi kwa mbewu yawo.’+  “Pa nthawi imeneyo ndinakuuzani kuti, ‘Ndekha sindikwanitsa kusenza mtolo wokutsogolerani.+ 10  Yehova Mulungu wanu wakuchulukitsani ndipo onani lero mwachulukadi ngati nyenyezi zakuthambo.+ 11  Yehova Mulungu wa makolo anu achulukitse chiwerengero chanu+ pochiwirikiza kambirimbiri, ndipo akudalitsenidi+ mmene anakulonjezerani.+ 12  Inuyo ndinu mtolo ndi katundu wolemera. Ndingathe bwanji ndekha kukusenzani, ndi mikangano yanuyo?+ 13  Sankhani amuna anzeru, aluso+ ndi ozindikira+ m’mafuko anu, kuti ndiwaike kukhala atsogoleri anu.’+ 14  Pamenepo munandiyankha kuti, ‘Zimene mwatiuza kuti tichitezi n’zabwino.’ 15  Choncho ndinatenga atsogoleri a mafuko anu, amuna anzeru ndi ozindikira n’kuwaika kukhala atsogoleri a magulu a anthu 1,000, atsogoleri a magulu a anthu 100, atsogoleri a magulu a anthu 50, atsogoleri a magulu a anthu 10, ndi akapitawo a m’mafuko anu.+ 16  “Pa nthawi imeneyo ndinalamula oweruza anu kuti, ‘Mukamazenga mlandu wa pakati pa abale anu, muziweruza mwachilungamo+ pakati pa munthu ndi m’bale wake, kapena ndi mlendo wokhala m’nyumba mwake.+ 17  Musamakondere poweruza.+ Munthu wamba ndi munthu wolemekezeka onse muziwamvetsera chimodzimodzi.+ Musamaope munthu+ chifukwa mukuweruzira Mulungu.+ Mlandu umene wakuvutani muziubweretsa kwa ine kuti ndiumve.’+ 18  Pa nthawi imeneyo ndinakuuzani zonse zimene muyenera kuchita. 19  “Kenako tinachoka ku Horebe ndi kuyenda kudutsa chipululu chachikulu ndi chochititsa mantha chonse chija+ chimene munachiona, podzera njira ya m’dera lamapiri la Aamori,+ monga momwe Yehova Mulungu wathu anatilamulira, mpaka tinafika ku Kadesi-barinea.+ 20  Ndiyeno ndinakuuzani kuti, ‘Mwafika m’dera lamapiri la Aamori, limene Yehova Mulungu wathu akutipatsa.+ 21  Onani, Yehova Mulungu wanu wakusiyirani dzikoli.+ Pitani, litengeni kuti likhale lanu, monga momwe Yehova Mulungu wa makolo anu anakuuzirani.+ Musaope kapena kuchita mantha.’+ 22  “Koma nonsenu munabwera kwa ine ndi kunena kuti, ‘Tiloleni titumize amuna, atsogole kukationera dzikolo ndipo adzatiuze njira imene tiyenera kudzera ndiponso mizinda imene tikapeze kumeneko.’+ 23  Pamenepo, ndinaona kuti amenewo ndi maganizo abwino, moti ndinatenga amuna 12 pakati panu, mmodzi m’fuko lililonse.+ 24  Choncho iwo ananyamuka ndi kupita kulowa m’dera lamapiri.+ Anayenda mpaka anafika m’chigwa* cha Esikolo,+ ndipo anazonda dzikolo. 25  Motero anatengako zina mwa zipatso za m’dzikolo+ ndi kutibweretsera. Iwo anatiuza kuti, ‘Dziko limene Yehova Mulungu wathu akutipatsa ndi labwino.’+ 26  Koma inu simunafune kupita kukalowa m’dzikolo,+ ndipo munayamba kupandukira lamulo la Yehova Mulungu wanu.+ 27  Pamenepo munapitiriza kung’ung’udza m’mahema mwanu kuti, ‘Yehova anatitulutsa m’dziko la Iguputo+ chifukwa chodana nafe,+ kuti adzatipereke m’manja mwa Aamori kuti atiwononge.+ 28  Tipite kuti? Abale athu achititsa mantha mitima yathu+ potiuza kuti: “Kumeneko tinaonako anthu akuluakulu, ndiponso aatali kuposa ifeyo,+ ndi mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri yofika kumwamba.+ Kumeneko tinaonakonso ana a Anaki.”’+ 29  “Ndiye ine ndinakuuzani kuti, ‘Musachite mantha kapena kuwaopa.+ 30  Yehova Mulungu wanu ndiye akukutsogolerani. Adzakumenyerani nkhondo+ mofanana ndi zonse zimene anakuchitirani ku Iguputo inu mukuona,+ 31  komanso m’chipululu,+ kumene munaona mmene Yehova Mulungu wanu anakunyamulirani.+ M’njira yonse imene munayenda anakunyamulani ngati mmene bambo amanyamulira mwana wake, mpaka kufika malo ano.’+ 32  Ngakhale kuti munamva mawu amenewa, simunakhulupirire Yehova Mulungu wanu,+ 33  amene anali kutsogola kuti akuzondereni malo oti mumangepo msasa wanu.+ Usiku anali kukutsogolerani ndi moto kuti muziona njira yoyendamo, ndipo masana anali kukutsogolerani ndi mtambo.+ 34  “Nthawi yonseyi Yehova anali kumvetsera mawu anu. Motero anakwiya kwambiri, ndipo analumbira+ kuti, 35  ‘Palibe munthu ndi mmodzi yemwe mwa anthu a m’badwo woipa uwu amene adzaona dziko labwino limene ndinalumbira kuti ndidzalipereka kwa makolo anu,+ 36  kupatulapo Kalebe mwana wa Yefune.+ Iyeyu adzaliona, ndipo ndidzagawira dziko limene anafikako kwa iye ndi ana ake, chifukwa chakuti watsatira Yehova ndi mtima wonse.+ 37  (Ngakhale inenso Yehova anandikwiyira chifukwa cha inu, ndipo anati, ‘Iwenso sukalowamo.+ 38  Yoswa mwana wa Nuni, amene akukutumikira ndi amene akalowamo.’+ Mulungu wamulimbitsa+ chifukwa ndi amene adzatsogolere ana a Isiraeli pokalandira dzikolo.) 39  Koma ana anu amene munanena kuti: “Adzagwidwa ndi adani!”+ ndiponso ana anu aang’ono amene lero sakudziwa chabwino kapena choipa, amenewa ndiwo adzalowa m’dziko limenelo. Amenewa ndidzawapatsa dzikolo ndipo adzalitenga kukhala lawo. 40  Koma inu, sinthani njira ndipo muyambe kulowera kuchipululu, kudzera njira yopita ku Nyanja Yofiira.’+ 41  “Pamenepo munayankha ndi kundiuza kuti, ‘Tachimwira Yehova.+ Ife tipitadi kukamenya nkhondo mogwirizana ndi zonse zimene Yehova Mulungu wathu watilamula!’ Choncho aliyense wa inu anamanga m’chiuno zida zake zankhondo, ndipo munaona ngati n’zosavuta kukwera m’phirimo.+ 42  Koma Yehova anandiuza kuti, ‘Auze kuti: “Musakwere kukamenya nkhondo, chifukwa ine sindili pakati panu.+ Chifukwa mukapita mudzagonjetsedwa ndi adani anu.”’+ 43  Motero ine ndinalankhula nanu, ndipo simunamvere koma munayamba kupandukira+ lamulo la Yehova ndi kuchita zinthu modzikuza, motero munanyamuka kupita m’phiri.+ 44  Kumeneko Aamori okhala m’phiri limenelo anatuluka kudzakumana nanu ndipo anakuthamangitsani,+ mmene njuchi zimachitira, ndi kukubalalitsani m’phiri la Seiri mpaka kukafika ku Horima.+ 45  Zitatero munabwerera ndi kuyamba kulira pamaso pa Yehova, koma Yehova sanamve mawu anu+ ndipo sanakutchereni khutu.+ 46  Chotero munakhala ku Kadesi masiku ambiri.+

Mawu a M'munsi

Kutanthauza m’chaka cha 40 atachoka ku Iguputo.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.