Amosi 7:1-17

7  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, anandionetsa masomphenya awa: Ndinamuona akutumiza dzombe, anthu atatsala pang’ono kubzala mbewu zomaliza.+ Nthawi imeneyi inali yobzala mbewu zomaliza, anthu atamweta udzu wopita kwa mfumu.  Ndiyeno dzombelo litamaliza kudya zomera zonse za m’dziko, ine ndinati: “Inu Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, chonde khululukani.+ Kodi Yakobo adzapulumuka bwanji, pakuti ndi wamng’ono?”+  Yehova anamva chisoni+ ndipo Yehova anati, “Zimenezi sizidzachitika.”  Kenako, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, anandionetsanso masomphenya awa: Ndinaona Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, akuuza anthu ake kuti alimbane naye pogwiritsira ntchito moto.+ Motowo unaumitsa madzi akuya ndiponso unawononga kachigawo ka dziko.  Ndiyeno ine ndinati: “Inu Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, chonde musatero.+ Kodi Yakobo adzapulumuka bwanji, pakuti ndi wamng’ono?”+  Pamenepo Yehova anamva chisoni+ ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, anati, “Zimenezinso sizidzachitika.”  Kenako, iye anandionetsanso masomphenya awa: Ndinaona Yehova ataima pamwamba pa khoma limene linamangidwa pogwiritsa ntchito chingwe chowongolera,+ ndipo iye anali ndi chingwe chowongolera m’dzanja lake.  Ndiyeno Yehova anandifunsa kuti: “Kodi ukuona chiyani Amosi?” Ndinamuyankha kuti: “Ndikuona chingwe chowongolera.” Pamenepo Yehova anati: “Ine ndiika chingwe chowongolera pakati pa anthu anga Aisiraeli,+ ndipo sindidzawakhululukiranso.+  Malo okwezeka a Isaki+ adzawonongedwa, ndipo malo opatulika+ a Isiraeli nawonso adzasakazidwa.+ Ine ndidzaukira nyumba ya Yerobowamu* ndi lupanga.”+ 10  Ndiyeno Amaziya wansembe wa ku Beteli,+ anatumiza uthenga kwa Yerobowamu+ mfumu ya Isiraeli kuti: “Amosi wakukonzerani chiwembu mkati mwenimweni mwa Isiraeli,+ ndipo anthu atopa nawo mawu akewo.+ 11  Amosi wanena kuti, ‘Yerobowamu adzaphedwa ndi lupanga, ndipo mosalephera Isiraeli adzagwidwa m’dziko lake ndi kutengedwa kupita ku ukapolo.’”+ 12  Ndiyeno Amaziya anauza Amosi kuti: “Iwe wamasomphenya,+ choka, thawira kudziko la Yuda, ndipo kumeneko uzikadya mkate ndi kunenera. 13  Koma usapitirize kunenera ku Beteli kuno,+ pakuti ndi malo opatulika a mfumu,+ ndiponso Beteli ndi nyumba ya ufumu uno.” 14  Pamenepo Amosi anayankha Amaziya kuti: “Ine sindinali mneneri kapena mwana wa mneneri,+ koma ndinali m’busa+ ndiponso woboola nkhuyu. 15  Koma Yehova ananditenga kumene ndinali kuweta nkhosa, ndipo Yehova anandiuza kuti, ‘Pita ukanenere kwa anthu anga Aisiraeli.’+ 16  Tsopano mvera mawu a Yehova, ‘Kodi iwe ukundiuza kuti: “Usanenere zinthu zoipa zokhudza Isiraeli,+ ndipo usatchule mawu alionse oipa+ okhudza nyumba ya Isaki”? 17  Yehova wanena kuti: “Mkazi wako adzakhala hule mumzindawu.+ Ana ako aamuna ndi ana ako aakazi adzaphedwa ndi lupanga. Anthu adzagawana dziko lako mochita kuyeza ndi chingwe, ndipo iweyo udzafera m’dziko lodetsedwa.+ Ndithudi, Isiraeli adzagwidwa m’dziko lake ndi kutengedwa kupita ku ukapolo.”’”+

Mawu a M'munsi

Ameneyu ndi Yerobowamu Wachiwiri, mwana wa Yowasi (Yehowasi). Onani Amo 1:1.