Amosi 2:1-16

2  “Yehova wanena kuti, ‘“Popeza kuti Mowabu+ anapanduka mobwerezabwereza, sindidzamusinthira chigamulo changa. Sindidzamusinthira chigamulocho chifukwa chakuti anatentha mafupa a mfumu ya Edomu kuti apeze laimu.+  Ndidzatumiza moto ku Mowabu, ndipo udzanyeketsa nsanja zokhalamo za Kerioti.+ Mowabu adzafa pakati pa phokoso la asilikali, kulira kwa chizindikiro chochenjeza ndiponso lipenga la nyanga ya nkhosa.+  Ndidzapha woweruza pamodzi ndi akalonga ake onse amene ali naye limodzi,”+ watero Yehova.’  “Yehova wanena kuti, ‘Popeza kuti Yuda+ anapanduka mobwerezabwereza, sindidzamusinthira chigamulo changa. Sindidzamusinthira chigamulocho chifukwa chakuti anakana lamulo la Yehova+ ndiponso sanasunge malangizo ake koma anasocheretsedwa ndi mabodza+ amene makolo awo anali kutsatira.+  Ndidzatumiza moto mu Yuda ndipo udzanyeketsa nsanja zokhalamo za Yerusalemu.’+  “Yehova wanena kuti, ‘Popeza kuti Isiraeli anapanduka mobwerezabwereza,+ sindidzamusinthira chigamulo changa. Sindidzamusinthira chigamulocho chifukwa chakuti anagulitsa munthu wolungama kuti apeze siliva komanso anagulitsa munthu wosauka pa mtengo wa nsapato.+  Iwo akufunitsitsa kuti fumbi la padziko lapansi ligwere pamitu ya anthu wamba+ ndipo sakuchitira chilungamo anthu ofatsa.+ Mwana pamodzi ndi bambo ake akugona ndi mtsikana mmodzi+ ndi cholinga chofuna kuipitsa dzina langa loyera.+  Iwo amayala zovala pafupi ndi guwa lililonse lansembe+ ndi kugonapo. Zovala zimenezo zimakhala zimene alanda anthu ena monga chikole.+ Amagula vinyo ndi ndalama zimene alipiritsa anthu ndipo amakamwera vinyoyo kunyumba za milungu yawo.’+  “‘Koma ine ndinawononga Aamori+ chifukwa cha anthu anga. Aamoriwo misinkhu yawo inali yofanana ndi mitengo ya mkungudza ndipo mphamvu zawo zinali zofanana ndi za mitengo ikuluikulu.+ Ndinawononga zipatso zawo m’mwamba ndiponso mizu yawo pansi.+ 10  Koma ine ndinatulutsa anthu inu m’dziko la Iguputo+ ndi kukuyendetsani m’chipululu zaka 40+ kuti mukatenge dziko la Aamori.+ 11  Ena mwa ana anu ndinali kuwachititsa kukhala aneneri+ ndipo ena ndinali kuwachititsa kukhala Anaziri.+ Kodi mmenemu si mmene zinayenera kukhalira, inu ana a Isiraeli?’ watero Yehova. 12  “‘Koma inu munapitiriza kupatsa Anaziri vinyo kuti amwe+ ndipo aneneri munawalamula kuti: “Musamanenere.”+ 13  Tsopano ine ndigwedeza nthaka imene mwapondapo ngati mmene ngolo imene yanyamula tirigu amene amumweta kumene imagwedezekera. 14  Malo othawirapo munthu waliwiro adzawonongeka+ ndipo palibe munthu wamphamvu amene adzalimbe, komanso palibe munthu wamphamvu amene adzapulumutse moyo wake.+ 15  Munthu wogwira uta sadzaima, munthu waliwiro kwambiri sadzatha kuthawa ndipo wokwera pahatchi* sadzatha kupulumutsa moyo wake.+ 16  Ndipo munthu wolimba mtima pakati pa anthu amphamvu adzathawa ali maliseche pa tsiku limenelo,’+ watero Yehova.”

Mawu a M'munsi

Ena amati “hosi,” kapena “kavalo.”