Amosi 1:1-15

1  Awa ndi mawu a Amosi amene anali mmodzi mwa anthu oweta nkhosa ku Tekowa.+ Anauzidwa mawu amenewa m’masomphenya okhudza Isiraeli,+ m’masiku a Uziya+ mfumu ya Yuda ndi m’masiku a Yerobowamu+ mwana wa Yowasi,+ mfumu ya Isiraeli, zaka ziwiri chivomezi chisanachitike.+  Iye anati: “Yehova adzabangula ngati mkango mu Ziyoni,+ ndipo adzafuula mu Yerusalemu.+ Malo amene abusa amadyetserako ziweto adzalira, ndipo pansonga ya phiri la Karimeli padzauma.”+  “Yehova wanena kuti, ‘“Popeza kuti Damasiko+ anapanduka mobwerezabwereza,* sindidzamusinthira chigamulo changa. Sindidzamusinthira chigamulocho chifukwa chakuti anapuntha Giliyadi+ ndi zida zachitsulo zopunthira.  Ndidzatumiza moto+ panyumba ya Hazaeli,+ ndipo udzanyeketsa nsanja zokhalamo za Beni-hadadi.+  Ndidzathyola mipiringidzo ya zipata za Damasiko+ ndi kupha anthu a ku Bikati-aveni. Ndidzaphanso munthu wogwira ndodo yachifumu wa ku Beti-edeni, ndipo anthu a ku Siriya adzatengedwa kupita ku ukapolo ku Kiri,”+ watero Yehova.’  “Yehova wanena kuti, ‘“Chifukwa chakuti Gaza wandipandukira mobwerezabwereza,+ sindidzamusinthira chigamulo changa. Sindidzamusinthira chigamulocho chifukwa chakuti anthu onse ogwidwa ukapolo+ anawapereka ku Edomu.+  Ndidzatumiza moto pakhoma la Gaza+ ndipo udzanyeketsa nsanja zake zokhalamo.  Ndidzapha anthu a ku Asidodi+ pamodzi ndi wogwira ndodo yachifumu wa ku Asikeloni.+ Ndidzalanga+ Ekironi+ ndipo ndidzafafaniza otsala mwa Afilisiti,”+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’  “Yehova wanena kuti, ‘Popeza kuti Turo+ anapanduka mobwerezabwereza, sindidzamusinthira chigamulo changa. Sindidzamusinthira chigamulocho chifukwa chakuti anapereka ku Edomu gulu lonse la anthu ogwidwa ukapolo, ndiponso chifukwa chakuti sanakumbukire pangano la pa ubale.+ 10  Ndidzatumiza moto pakhoma la Turo ndipo udzanyeketsa nsanja zake zokhalamo.’+ 11  “Yehova wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti Edomu wandipandukira mobwerezabwereza,+ sindidzamusinthira chigamulo changa. Sindidzamusinthira chigamulocho chifukwa chakuti anathamangitsa m’bale wake ndi lupanga,+ sanasonyeze chifundo,+ akupitiriza kukhadzulakhadzula zinthu ali wokwiya komanso akukhalabe wokwiya mosalekeza.+ 12  Ndidzatumiza moto ku Temani+ ndipo udzanyeketsa nsanja zokhalamo za ku Bozira.’+ 13  “Yehova wanena kuti, ‘“Chifukwa chakuti ana a Amoni+ andipandukira mobwerezabwereza, sindidzawasinthira chigamulo changa.+ Sindidzawasinthira chigamulocho chifukwa chakuti anatumbula akazi apakati a ku Giliyadi ndi cholinga chakuti afutukule malo awo okhala.+ 14  Ndidzayatsa mpanda wa Raba+ ndipo motowo udzanyeketsa nsanja zake zokhalamo. Padzakhala chizindikiro chochenjeza pa tsiku la nkhondo ndiponso mphepo yamkuntho pa tsiku la chimvula champhamvu.+ 15  Pamenepo mfumu yawo idzagwidwa ndi kupita ku ukapolo pamodzi ndi akalonga ake,”+ watero Yehova.’

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “Chifukwa cha kupanduka katatu ndiponso chifukwa cha kupanduka kanayi.”