Akolose 4:1-18

4  Inu anthu amene muli ambuye, pitirizani kuchitira akapolo+ anu zinthu zachilungamo ndi zoyenera, podziwa kuti inunso muli ndi Ambuye kumwamba.+  Muzilimbikira kupemphera.+ Mukhale maso pa nkhani ya kupemphera ndipo mukhale oyamikira.+  Muzitipemphereranso ifeyo,+ kuti Mulungu atitsegulire khomo+ kuti tithe kulalikira mawu ndi kulankhula za chinsinsi chopatulika+ chonena za Khristu, chimene ndinamangidwira n’kukhala m’ndende muno,+  kuti ndidzalalikire ndi kulankhula za chinsinsicho ngati mmene ndiyenera kulankhulira.+  Pitirizani kuyenda mwanzeru pochita zinthu ndi anthu akunja,*+ ndipo muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.*+  Nthawi zonse mawu anu azikhala achisomo,+ okoma ngati kuti mwawathira mchere,+ kuti mudziwe mmene mungayankhire+ wina aliyense.  Tukiko,+ m’bale wanga wokondedwa komanso mtumiki wokhulupirika, ndi kapolo mnzanga mwa Ambuye, adzakudziwitsani zonse za ine.  Ndikumutumiza ndi cholinga chimenechi, kuti inuyo mudziwe za ife, ndi kutinso alimbikitse mitima yanu.+  Ndamutumiza limodzi ndi Onesimo,+ m’bale wanga wokhulupirika ndi wokondedwa, amene anachokera pakati panu. Amenewa adzakusimbirani zonse zakuno. 10  Arisitako+ mkaidi mnzanga akuti moni nonse. Komanso Maliko+ msuweni* wa Baranaba, (amene ndinakulangizani kuti mumulandire+ nthawi iliyonse akadzafika kwa inu,) 11  ndi Yesu, wotchedwanso Yusito, akuti moni. Amenewa ali m’gulu la anthu odulidwa. Okhawa ndiwo antchito anzanga pa zinthu zokhudzana ndi ufumu wa Mulungu, ndipo amenewa andithandiza ndi kundilimbikitsa. 12  Epafura,+ amene anachokera pakati panu, kapolo wa Khristu Yesu, akuti moni. Iye amakupemphererani mwakhama nthawi zonse, kuti pomalizira pake mukhale okhwima mwauzimu+ ndi osakayika ngakhale pang’ono za chifuniro chonse cha Mulungu. 13  Ndikumuchitiradi umboni kuti amadzipereka kwambiri chifukwa cha inu ndi abale a ku Laodikaya+ ndi ku Herapoli. 14  Luka,+ dokotala wokondedwa, akuti moni nonse. Dema+ nayenso akuti moni. 15  Mundiperekere moni kwa abale a ku Laodikaya ndi kwa Numfa ndi mpingo umene umasonkhana panyumba pake.+ 16  Ndipo kalatayi mukaiwerenga kwanuko, konzani zoti ikawerengedwenso+ ku mpingo wa Alaodikaya, ndiponso mukawerenge yochokera ku Laodikaya. 17  Komanso Arikipo+ mumuuze kuti: “Uonetsetse kuti utumiki umene unaulandira mwa Ambuye ukuukwaniritsa.” 18  Tsopano landirani moni wanga wolemba ndekha ndi dzanja langa,+ ineyo Paulo. Pitirizani kukumbukira maunyolo+ amene andimanga nawo kundende kuno. Kukoma mtima kwakukulu kukhale nanu.

Mawu a M'munsi

Amenewa ndi anthu amene sali mumpingo wachikhristu.
Mawu ake enieni, “muzigula nthawi yoikidwa.”
Kapena kuti, “mwana wa amalume a Baranaba.”