Agalatiya 6:1-18
6 Abale, ngati munthu wapatuka n’kuyamba kulowera njira yolakwika+ mosazindikira, inu oyenerera mwauzimu,+ yesani kumuthandiza munthu woteroyo ndi mzimu wofatsa.+ Pamene mukutero, aliyense wa inu asamale,+ kuopera kuti iyenso angayesedwe.+
2 Musaleke kunyamulirana zolemetsa.+ Mukatero mudzakhala mukukwaniritsa chilamulo cha Khristu.+
3 Pakuti ngati wina akudziona kuti ndi wofunika pamene si wotero,+ akudzinyenga.
4 Koma aliyense payekha ayese ntchito yake, kuti aone kuti ndi yotani.+ Akatero adzakhala ndi chifukwa chosangalalira ndi ntchito yake, osati modziyerekezera+ ndi munthu wina.
5 Pakuti aliyense ayenera kunyamula katundu wake.+
6 Komanso, aliyense amene akuphunzitsidwa mawuwo+ agawane+ zinthu zonse zabwino ndi amene akumuphunzitsayo.+
7 Musanyengedwe,+ Mulungu sapusitsika.+ Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.+
8 Pakuti amene akufesa ndi cholinga chopindulitsa thupi lake, adzakolola chiwonongeko kuchokera m’thupi lakelo,+ koma amene akutsatira mzimu wa Mulungu+ adzakolola moyo wosatha kuchokera ku mzimuwo.+
9 Choncho tisaleke kuchita zabwino,+ pakuti pa nyengo yake tidzakolola tikapanda kutopa.+
10 Chotero ngati tingathe,+ tiyeni tichitire onse zabwino, koma makamaka abale ndi alongo athu m’chikhulupiriro.+
11 Taonani zilembo zikuluzikulu zimene ndakulemberani ndekha ndi dzanja langali.+
12 Onse ofuna kudzionetsa ngati abwino pamaso pa anthu ndi amene akukuumirizani kuti muzidulidwa.+ Akuchita zimenezi kuti asazunzidwe chifukwa cha mtengo wozunzikirapo wa Khristu,+ amene ndi Yesu.
13 Pakuti ngakhale amene akudulidwawo sasunga Chilamulo,+ koma akufuna inuyo mudulidwe kuti iwo azidzitama chifukwa cha zimene zachitika pathupi lanu.
14 Ineyo sindidzadzitama pa chifukwa china chilichonse, koma chifukwa cha mtengo wozunzikirapo+ wa Ambuye wathu Yesu Khristu basi. Kudzera mwa ameneyu, kwa ine dziko lapansi lapachikidwa, ndipo malinga ndi kuona kwa dziko lapansi,+ ineyo ndapachikidwa.
15 Pakuti kudulidwa kapena kusadulidwa si kanthu,+ koma chofunika ndi kukhala wolengedwa mwatsopano.+
16 Ndipo onse otsatira lamulo limeneli la mmene tiyenera kukhalira, amene ndi Isiraeli wa Mulungu, akhale ndi mtendere ndiponso chifundo.+
17 Kuyambira tsopano, pasapezeke munthu wondivutitsa, pakuti thupi langali lili ndi zipsera za chizindikiro+ cha kapolo wa Yesu.+
18 Abale, kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye wathu Yesu Khristu, kukhale nanu chifukwa cha mzimu+ umene mumausonyeza. Ame.