Agalatiya 3:1-29

3  Kalanga ine, Agalatiya opusa inu! Kodi ndani anakupotozani maganizo,+ inu amene munakhala ngati mwaona Yesu Khristu atapachikidwa pamtengo?+  Ndikufuna mundiuze: Kodi munalandira mzimu+ chifukwa cha ntchito za chilamulo+ kapena chifukwa chokhulupirira zimene munamva?+  Kodi ndinu opusa chonchi? Munayamba ndi kudalira mzimu,+ kodi tsopano mukufuna kumaliza ndi kudalira zinthu zochokera kwa anthu opanda ungwiro?+  Kodi kuvutika konse kuja kunangopita pachabe?+ Ndikukhulupirira kuti sikunapite pachabe.  Iye amene amakupatsani mzimu+ ndi kuchita zinthu zamphamvu+ pakati panu, kodi amazichita chifukwa chakuti inuyo mukuchita ntchito za chilamulo kapena chifukwa chakuti munakhulupirira uthenga wabwino umene munamva?  Zili monga mmene Abulahamu “anakhulupirira mwa Yehova, ndipo Mulunguyo anamuona Abulahamu ngati wolungama.”+  Ndithudi mukudziwa kuti amene amakhalabe ndi chikhulupiriro+ ndiwo ana a Abulahamu.+  Ndiyeno, Malemba ataoneratu kuti Mulungu adzayesa anthu a mitundu ina kukhala olungama chifukwa cha chikhulupiriro, analengezeratu uthenga wabwino kwa Abulahamu, kuti: “Kudzera mwa iwe, mitundu yonse idzadalitsidwa.”+  Chotero, amene akugwiritsitsa chikhulupiriro akudalitsidwa+ limodzi ndi Abulahamu wokhulupirikayo.+ 10  Pakuti onse odalira ntchito za chilamulo ndi otembereredwa, chifukwa Malemba amati: “Ndi wotembereredwa aliyense wosapitiriza kuyenda m’zinthu zonse zolembedwa mumpukutu wa Chilamulo ndi kuzichita.”+ 11  Komanso, mfundo yakuti palibe munthu amene angaonedwe ngati wolungama+ ndi Mulungu mwa chilamulo ndi yoonekeratu, chifukwa “wolungama adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro chake.”+ 12  Tsopano, Chilamulo sichidalira chikhulupiriro, koma “wochita za m’Chilamulo adzakhala ndi moyo potsatira chilamulocho.”+ 13  Khristu anatigula+ ndi kutimasula+ ku temberero la Chilamulo ndipo iyeyo anakhala temberero+ m’malo mwa ife, chifukwa Malemba amati: “Ndi wotembereredwa aliyense wopachikidwa pamtengo.”+ 14  Cholinga chake chinali chakuti mitundu ipeze madalitso amene Abulahamu analonjezedwa kudzera mwa Yesu Khristu,+ kuti tidzalandire mzimu wolonjezedwawo+ chifukwa cha chikhulupiriro chathu.+ 15  Abale, ndipereke fanizo mogwirizana ndi zimene zimachitika pakati pa anthu: Pangano likakhazikitsidwa, ngakhale kuti ndi pangano la anthu, palibe angachotsepo kapena kuwonjezerapo mfundo zina.+ 16  Tsopano, malonjezo anaperekedwa kwa Abulahamu+ ndi kwa mbewu yake.+ Malemba sanena kuti: “Kwa mbewu zako,” ngati kuti mbewuzo n’zambiri, koma amanena za mbewu imodzi+ kuti: “Kwa mbewu yako,”+ amene ndi Khristu.+ 17  Komanso ineyo ndikuti: Chilamulo chimene chinadzakhalapo zaka 430+ pambuyo pa panganolo, limene kalekalelo linatsimikizidwa ndi Mulungu,+ sichingathetse mphamvu ya panganolo, kapena kufafaniza lonjezolo.+ 18  Pakuti ngati cholowa chimene Mulungu amapereka chimadzera m’chilamulo, ndiye kuti sichidaliranso lonjezo,+ koma Mulungu mokoma mtima wachipereka kwa Abulahamu mwa lonjezo.+ 19  Nanga tsopano Chilamulo chinakhalapo chifukwa chiyani? Anachiwonjezerapo kuti machimo aonekere,+ mpaka amene ali mbewuyo atafika,+ amene anapatsidwa lonjezolo. Ndipo Chilamulocho chinaperekedwa kudzera mwa angelo,+ kudzeranso m’dzanja la mkhalapakati.+ 20  Tsopano, sipakhala mkhalapakati ngati pangano lili la munthu mmodzi yekha, koma Mulungu anali yekha.+ 21  Chotero kodi Chilamulo chimatsutsa malonjezo a Mulungu?+ Zimenezo sizingachitike ngakhale pang’ono. Pakanaperekedwa lamulo lopatsa moyo,+ bwenzi chilungamo chikudzera m’chilamulo.+ 22  Koma Malemba+ anatsekera zinthu zonse n’kuziika pansi pa uchimo,+ kuti lonjezolo, limene limakhalapo mwa kukhulupirira Yesu Khristu, liperekedwe kwa okhulupirirawo.+ 23  Komabe chikhulupirirocho chisanafike,+ chilamulo chinali kutiyang’anira+ ndipo chinatiika mu ukapolo. Pa nthawi imeneyo, tinali tikuyembekezera chikhulupiriro chimene chinali kudzaonekera.+ 24  N’chifukwa chake Chilamulo chakhala mtsogoleri* wotifikitsa kwa Khristu,+ kuti tiyesedwe olungama+ chifukwa cha chikhulupiriro. 25  Koma popeza chikhulupirirocho tsopano chafika,+ sitilinso pansi pa mtsogoleriyo.+ 26  Koma nonsenu ndinu ana+ a Mulungu chifukwa cha chikhulupiriro chanu mwa Khristu Yesu. 27  Pakuti nonsenu amene munabatizidwa mwa Khristu+ mwavala Khristu.+ 28  Palibe Myuda kapena Mgiriki,+ palibe kapolo kapena mfulu,+ palibenso mwamuna kapena mkazi.+ Nonsenu ndinu munthu mmodzi mwa Khristu Yesu.+ 29  Ndiponso ngati muli a Khristu, ndinudi mbewu ya Abulahamu,+ olandira cholowa mogwirizana ndi lonjezolo.+

Mawu a M'munsi

Mawu achigiriki amene tawamasulira kuti “mtsogoleri” amatanthauza munthu amene anali kugwira ntchito yoyang’anira kapena kuteteza ana.