Agalatiya 2:1-21

2  Ndiyeno patapita zaka 14, ndinapita ku Yerusalemu kachiwiri+ limodzi ndi Baranaba,+ ndipo ndinatenganso Tito.  Ndinapita kumeneko chifukwa ndinauzidwa m’masomphenya kuti ndipiteko.+ Ndipo ndinafotokozera+ amuna odalirika, uthenga wabwino umene ndikuulalikira kwa anthu a mitundu ina. Ndinachita zimenezo chifukwa ndinkaopa kuti mwina ndinali kuthamanga+ popanda phindu, kapena ndinali nditathamanga kale pachabe.+ Koma ndinawafotokozera zimenezi kumbali.  Ndipo ngakhale Tito,+ amene ndinali naye limodzi, sanafunikire kudulidwa,+ ngakhale kuti iye ndi Mgiriki.  Chifukwa cha abale onyenga+ amene analowa pakati pathu mwakachetechete+ ndiponso mozemba monga akazitape, n’cholinga choti awononge ufulu wathu+ umene tili nawo mogwirizana ndi Khristu Yesu, ndiponso kuti atisandutse akapolo+ . . .  anthu amenewa sitinawagonjere,+ ngakhale kwa ola limodzi, kuti inuyo mupitirize kukhala ndi choonadi+ cha uthenga wabwino.  Tsopano kunena za anthu amene ankaoneka ngati apadera,+ kaya pa chiyambi anali anthu otani, zilibe kanthu kwa ine,+ Mulungu sayang’ana nkhope ya munthu,+ kwa ine, amuna odalirika amenewo sanandiphunzitse kalikonse katsopano.  Koma iwo ataona kuti ndapatsidwa+ ntchito yolalikira uthenga wabwino kwa anthu osadulidwa,+ mmene Petulo anapatsidwira ntchito yoti akalalikire uthenga wabwino kwa anthu odulidwa,+  (pajatu iye amene anapatsa Petulo mphamvu yokhala mtumwi kwa anthu odulidwa ndi amene anapatsanso ine mphamvu+ kuti ndikalalikire kwa anthu a mitundu ina)  iwo atazindikira kukoma mtima kwakukulu+ kumene ndinapatsidwa,+ Yakobo,+ Kefa ndi Yohane, amene anali ngati mizati,+ anagwira chanza ineyo ndi Baranaba.+ Anatero posonyeza kuti agwirizana nazo+ zoti ife tipite kwa anthu a mitundu ina, ndipo iwo apite kwa odulidwa. 10  Anangotipempha kuti tizikumbukira aumphawi.+ Ndipo ndayesetsa moona mtima kuchita zimenezi.+ 11  Koma Kefa+ atabwera ku Antiokeya,+ ndinamutsutsa pamasom’pamaso, chifukwa anali wolakwa.+ 12  Pakuti asanafike anthu ena ochokera kwa Yakobo,+ iye anali kudya+ limodzi ndi anthu a mitundu ina, koma anthuwo atafika, iye anadzipatula ndipo anasiya kuchitira nawo zinthu limodzi, chifukwa ankaopa+ anthu odulidwawo.+ 13  Ayuda enawonso anagwirizana naye pochita zachiphamaso zimenezi.+ Ngakhale Baranaba+ nayenso anachita nawo zachiphamasozi. 14  Koma nditaona kuti sanali kuyenda mogwirizana ndi choonadi cha uthenga wabwino,+ ndinanena kwa Kefa pamaso pa onse+ kuti: “Ngati iweyo, ngakhale kuti ndiwe Myuda, ukukhala ngati anthu a mitundu ina, osati ngati Ayuda, n’chifukwa chiyani ukufuna kuchititsa anthu a mitundu ina kuti azitsatira chikhalidwe cha Ayuda?”+ 15  Ifeyo ndife a mtundu wachiyuda.+ Si ife ochimwa+ ochokera mwa anthu a mitundu ina. 16  Popeza tikudziwa kuti munthu amayesedwa wolungama+ mwa kukhulupirira+ Khristu Yesu, osati chifukwa cha ntchito za chilamulo, ife takhulupirira Khristu Yesu. Tachita zimenezi kuti tiyesedwe olungama chifukwa cha chikhulupiriro chathu mwa Khristu,+ osati mwa ntchito zotsatira chilamulo. Tatero chifukwa palibe munthu adzayesedwa wolungama chifukwa cha ntchito zotsatira chilamulo.+ 17  Tsopano ngati ife, pofuna kuyesedwa olungama kudzera mwa Khristu,+ tapezedwanso kuti ndife ochimwa,+ kodi ndiye kuti Khristu wakhala mtumiki wa uchimo?+ Ayi ndithu. 18  Pakuti ngati ndikumanganso zomwezo zimene ndinagwetsa,+ ndiye kuti ndikusonyeza kuti ndine wophwanya malamulo.+ 19  Mwa chilamulo, ine ndinafa ku chilamulo,+ moti sindingachitsatirenso, kuti ndikhale wamoyo kwa Mulungu.+ 20  Ndinapachikidwa limodzi ndi Khristu.+ Si inenso amene ndikukhala ndi moyo,+ koma Khristu ndi amene akukhala ndi moyo mwa ine.+ Zoonadi, moyo umene ndikukhala tsopano,+ ndikukhala mokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene anandikonda ndi kudzipereka yekha chifukwa cha ine.+ 21  Sindikukankhira kumbali kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu,+ chifukwa ngati munthu amakhala wolungama kudzera mwa chilamulo,+ ndiye kuti Khristu anangofa pachabe.+

Mawu a M'munsi