Agalatiya 1:1-24

1  Ine Paulo,+ ndine mtumwi,+ osati wochokera kwa anthu kapena woikidwa kudzera mwa munthu, koma mwa Yesu Khristu+ ndi mwa Mulungu Atate+ amene anamuukitsa kwa akufa.+  Ineyo, pamodzi ndi abale onse amene ali ndi ine,+ ndikulembera kalata mipingo ya ku Galatiya:+  Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu, zikhale nanu.+  Iye anadzipereka chifukwa cha machimo athu,+ kuti atilanditse ku nthawi* yoipayi,+ mogwirizana ndi chifuniro+ cha Mulungu ndi Atate wathu.  Ulemu ukhale kwa Mulunguyo mpaka muyaya.+ Ame.  Ndine wodabwa kuti mwapatutsidwa mwamsanga, kuchoka kwa Iye+ amene anakuitanani mwa kukoma mtima kwakukulu kwa Khristu,+ ndipo mwakopeka ndi uthenga wabwino wamtundu wina.+  Koma umenewo sikuti ndi uthenganso wabwino, kungoti pali anthu ena amene akukusokonezani+ ndipo akufuna kupotoza uthenga wabwino wonena za Khristu.+  Komabe, ngati ifeyo kapena mngelo wochokera kumwamba angalengeze nkhani ina kwa inu monga uthenga wabwino, koma nkhaniyo n’kukhala yosiyana ndi uthenga wabwino umene tinaulengeza kwa inu, ameneyo akhale wotembereredwa.+  Monga mmene tanenera kale, ndikunenanso kuti, Aliyense amene akulengeza nkhani ina kwa inu monga uthenga wabwino, koma yosiyana ndi imene munalandira,+ ameneyo akhale wotembereredwa. 10  Kodi ndiye kuti tsopano ndikufuna kukopa anthu kapena Mulungu? Kapena kodi ndikungofuna kukondweretsa anthu?+ Ndikanakhala kuti ndikukondweretsabe anthu,+ sindikanakhala kapolo wa Khristu.+ 11  Pakuti ndikufuna mudziwe, abale, kuti uthenga wabwino umene ndinaulengeza monga uthenga wabwino sunachokere kwa anthu.+ 12  Uthengawu sindinaulandire kwa munthu, ndipo sindinachite kuuphunzira mwanjira ina, koma Yesu Khristu ndiye amene anandiululira uthenga umenewu.+ 13  Munamva ndithu zimene ndinali kuchita ndili m’Chiyuda,+ kuti ndinkazunza kwambiri+ mpingo wa Mulungu ndi kupitirizabe kuuwononga.+ 14  Ndinali kupita patsogolo kwambiri m’Chiyuda kuposa anzanga ambiri a fuko langa, omwe anali amsinkhu wanga.+ Pakuti ndinali wodzipereka kwambiri+ pa miyambo+ ya makolo anga. 15  Koma pamene Mulungu, amene anandichititsa kuti ndibadwe, anandiitana+ mwa kukoma mtima kwake kwakukulu,+ kunamukomera 16  kuulula za Mwana wake kudzera mwa ine,+ kuti ndilengeze kwa anthu a mitundu ina uthenga wabwino wonena za iye.+ Sindinapite kukakambirana ndi anthu a thupi la nyama ndi magazi nthawi yomweyo.+ 17  Sindinapitenso ngakhale ku Yerusalemu kwa amene anakhala atumwi ndisanakhale ine,+ koma ndinapita ku Arabiya, kenako ndinabwereranso ku Damasiko.+ 18  Ndiye pambuyo pa zaka zitatu ndinapita ku Yerusalemu+ kukacheza kwa Kefa+ ndipo ndinakhala naye masiku 15. 19  Koma sindinaone mtumwi winanso kupatulapo Yakobo,+ m’bale+ wa Ambuye. 20  Zimene ndikukulemberanizi, ndikukuuzani pamaso pa Mulungu kuti sindikunama.+ 21  Kenako ndinalowa+ m’madera a Siriya ndi Kilikiya. 22  Koma nkhope yanga inali yosadziwika kumipingo yogwirizana ndi Khristu, ya ku Yudeya.+ 23  Iwo ankangomva kuti: “Munthu amene anali kutizunza kale uja,+ tsopano akulengeza uthenga wabwino wonena za chikhulupiriro chimene anali kuwononga.”+ 24  Choncho anthuwo anayamba kulemekeza+ Mulungu chifukwa cha ine.

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.