Afilipi 4:1-23
4 Choncho abale anga okondedwa, inu amene ndimakukondani ndiponso amene ndimalakalaka kukuonani, inu chimwemwe changa ndi chisoti changa chaulemerero,+ pitirizani kulimbikira+ mwa Ambuye.
2 Ndikudandaulira Eodiya ndi Suntuke, kuti akhale amaganizo amodzi+ mwa Ambuye.
3 Ndikupempha iwenso wantchito mnzanga weniweni,+ kuti upitirize kuwathandiza amayi amenewa. Iwo ayesetsa limodzi ndi ine pa ntchito+ ya uthenga wabwino. Achita zimenezi limodzinso ndi Kilementi ndi antchito anzanga ena onse,+ amene mayina awo+ ali m’buku la moyo.+
4 Nthawi zonse kondwerani mwa Ambuye.+ Ndibwerezanso, Kondwerani.+
5 Anthu onse adziwe kuti ndinu ololera.+ Ambuye ali pafupi.+
6 Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse,+ koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero,+ pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.+
7 Mukatero, mtendere+ wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu+ ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
8 Chomalizira abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zofunika kwambiri, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera,+ zilizonse zachikondi, zilizonse zoyamikirika, khalidwe labwino lililonse, ndi chilichonse chotamandika, pitirizani kuganizira zimenezi.+
9 Zinthu zimene munaphunzira, zimene munazivomereza, zimene munazimva, ndi zimene munaziona kwa ine, muzichita zimenezo,+ ndipo Mulungu wamtendere+ adzakhala nanu.
10 Ine ndikukondwera kwambiri mwa Ambuye, kuti tsopano mwayambanso kundiganizira.+ Ndipo n’zimene munalidi kufuna kungoti munali kusowa mpata.
11 Si kuti ndikulankhula izi kusonyeza kuti ndikusowa kanthu, pakuti m’zochitika zosiyanasiyana ine ndaphunzira kukhala wokhutira ndi zimene ndili nazo.+
12 Ndithudi, kukhala wosowa ndimakudziwa,+ kukhala ndi zochuluka ndimakudziwanso. M’zinthu zonse ndi m’zochitika zosiyanasiyana, ndaphunzira chinsinsi chokhala wokhuta ndi chokhala wanjala. Ndaphunziranso chinsinsi chokhala ndi zochuluka, ndi chokhala wosowa.+
13 Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.+
14 Komabe, munachita bwino pondithandiza+ m’chisautso changa.+
15 Ndipo inu Afilipi, mukudziwanso kuti pamene ndinayamba kulengeza uthenga wabwino, komanso pamene ndinanyamuka ku Makedoniya, panalibe mpingo ndi umodzi womwe umene unathandizana nane pa nkhani ya kupatsa ndi kulandira, kupatulapo inu nokha.+
16 Chifukwa ngakhale ku Tesalonika, inu munanditumizira kenakake pa zosowa zanga ndipo munachita zimenezi kawiri konse.
17 Si kuti mtima wanga uli pa mphatsoyo ayi,+ koma ndikufunitsitsa kuti mulandire madalitso+ amene adzawonjezere phindu pa zimene muli nazo.
18 Komabe, ine ndili ndi zonse zimene ndimafunikira, ndipo n’zokwanira ndi zosefukira. Sindikusowa kanthu, pakuti tsopano ndalandira kwa Epafurodito+ zinthu zochokera kwa inu. Zili ngati fungo lonunkhira bwino+ ndiponso nsembe yovomerezeka+ yosangalatsa kwa Mulungu.
19 Nayenso Mulungu wanga+ adzakupatsani zosowa zanu zonse+ mogwirizana ndi kuchuluka kwa chuma chake+ chaulemerero, kudzera mwa Khristu Yesu.
20 Tsopano kwa Mulungu wathu ndi Atate, kukhale ulemerero mpaka muyaya.+ Ame.
21 Mundiperekere moni+ kwa aliyense amene ali woyera mwa+ Khristu Yesu. Abale amene ali nane akukupatsani moni.
22 Oyera onse akupereka moni, koma makamaka a m’nyumba ya Kaisara.+
23 Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu Khristu kukhale nanu, chifukwa muli ndi maganizo abwino.+