Afilipi 2:1-30
2 Chotero, ngati pakati panu pali kulimbikitsana kulikonse mwa Khristu,+ kaya kutonthozana kulikonse kwa chikondi, kaya mzimu woganizirana,+ kaya chikondi chachikulu+ chilichonse ndi chifundo,
2 chititsani chimwemwe changa kusefukira pokhala ndi maganizo amodzi,+ ndi chikondi chofanana. Mukhalenso ogwirizana mu mzimu umodzi, ndi mtima umodzi.+
3 Musachite chilichonse ndi mtima wokonda mikangano+ kapena wodzikuza,+ koma modzichepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani.+
4 Musamaganizire zofuna zanu zokha,+ koma muziganiziranso zofuna za ena.+
5 Khalani ndi maganizo amenewa, amenenso Khristu Yesu anali nawo.+
6 Ngakhale kuti iye anali ndi maonekedwe a Mulungu,+ kukhala wolingana ndi Mulungu sanakuganizirepo ngati chinthu choti angalande.+
7 Sanatero ayi, koma anasiya zonse zimene anali nazo n’kukhala ngati kapolo,+ ndi kukhala wofanana ndi anthu.+
8 Kuposanso pamenepo, atakhala munthu,+ anadzichepetsa ndi kukhala womvera mpaka imfa.+ Anakhala womvera mpaka imfa ya pamtengo wozunzikirapo.*+
9 Pa chifukwa chimenechinso, Mulungu anamukweza n’kumuika pamalo apamwamba.+ Ndipo anamukomera mtima n’kumupatsa dzina loposa lina lililonse.+
10 Anachita zimenezi kuti m’dzina la Yesu, onse akumwamba, apadziko lapansi, ndi apansi pa nthaka apinde mawondo awo.+
11 Kutinso aliyense avomereze poyera ndi lilime lake+ kuti Yesu Khristu ndiye Ambuye,+ polemekeza Mulungu Atate.+
12 Chotero, okondedwa anga, monga mmene mwakhalira omvera nthawi zonse,+ osati pokhapokha ine ndikakhalapo,* koma mofunitsitsa kwambiri tsopano pamene ine kulibe, pitirizani kukonza chipulumutso chanu, mwamantha+ ndi kunjenjemera.
13 Pakuti Mulungu amachita zinthu m’njira imene imamusangalatsa. Iye amalimbitsa zolakalaka zanu+ kuti muchite zinthu zonse zimene iye amakonda.+
14 Muzichita zinthu zonse popanda kung’ung’udza+ ndi kutsutsana,+
15 kuti mukhale opanda chifukwa chokunenezani nacho ndiponso osalakwa.+ Mukhale ana a Mulungu opanda chilema+ pakati pa m’badwo wopotoka maganizo ndi wokhotakhota,+ umene mukuwala pakati pawo monga zounikira m’dzikoli.+
16 Muchite zimenezi pamene mukupitirizabe kugwira mwamphamvu mawu amoyo,+ kuti ndikakhale ndi chifukwa chosangalalira m’tsiku la Khristu,+ poona kuti sindinathamange pachabe, kapena kuchita khama pachabe.+
17 Ngakhale kuti ndikudzipereka ngati nsembe yachakumwa imene ikuthiridwa+ pansembe+ ndi pa ntchito yotumikira anthu imene chikhulupiriro chakupatsani,+ ndine wokondwa ndipo ndikukondwera+ ndi inu nonse.
18 Tsopano inunso khalani okondwa ndipo sangalalani limodzi ndi ine.+
19 Koma ine, mwa Ambuye Yesu ndikuyembekeza kutumiza Timoteyo kwa inu posachedwapa, kuti ndidzasangalale+ ndikadzamva mmene zinthu zilili kwa inu.
20 Pakuti ndilibe wina wamtima ngati iye, amene angasamaledi+ za inu moona mtima.
21 Pakuti ena onse akungofuna za iwo eni,+ osati za Khristu Yesu.
22 Koma inu mukudziwa kudalirika kumene iye anaonetsa, kuti monga mwana+ ndi bambo ake, watumikira monga kapolo limodzi ndi ine kupititsa patsogolo uthenga wabwino.
23 Choncho, ameneyu ndiye munthu amene ndikuyembekeza kumutumiza kwa inu, ndikangodziwa mmene zinthu zikhalire kwa ine.
24 Ndithudi, ndikukhulupirira mwa Ambuye kuti inenso ndibwera posachedwa.+
25 Komabe, ndaona kuti n’kofunika kutumiza Epafurodito kwa inu.+ Ameneyu ndi m’bale wanga, wantchito mnzanga+ ndi msilikali mnzanga.+ Komanso iye ndi nthumwi yanu ndi wonditumikira pa zosowa zanga.
26 Pakuti iye akulakalaka kukuonani nonsenu, ndipo akuvutika maganizo chifukwa munamva kuti anali kudwala.
27 Inde, n’zoona, anadwaladi kutsala pang’ono kufa. Koma Mulungu anam’chitira chifundo.+ Ndipo chifundo chimenecho sanachitire iye yekha ayi, koma inenso, kuti chisoni changa chisawonjezeke.
28 Choncho, ndikumutumiza mofulumira kwambiri, kuti inu mukamuona musangalale, ndiponso kuti chisoni changa chichepe.
29 Chotero, mulandireni monga mwa nthawi zonse,+ mwa Ambuye ndi chimwemwe chonse. Ndipo abale okhala ngati iyeyu muziwalemekeza kwambiri,+
30 pakuti chifukwa cha ntchito ya Ambuye, anatsala pang’ono kufa.+ Anaika moyo wake pachiswe, kuti adzanditumikire m’malo mwa inu,+ popeza simuli kuno.