Afilipi 1:1-30

1  Ine Paulo ndili pamodzi ndi Timoteyo monga akapolo+ a Khristu Yesu. Ndikulembera oyera onse ogwirizana ndi Khristu Yesu amene ali ku Filipi,+ komanso oyang’anira ndi atumiki othandiza:+  Kukoma mtima kwakukulu, ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi kwa Ambuye Yesu Khristu, zikhale nanu.+  Ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakumbukira za inu.+  Ndimachita zimenezi m’pembedzero langa lililonse limene ndimapereka mosangalala chifukwa cha nonsenu.+  Ndimamuyamika chifukwa cha chopereka+ chanu chimene mwakhala mukupereka ku uthenga wabwino, kuchokera pa tsiku loyamba mpaka pano.  Pakuti ndikutsimikizira kuti iyeyo amene anayambitsa ntchito yabwino kwa inu, adzaipitiriza ndi kuimalizitsa+ m’tsiku+ la Yesu Khristu.  N’zoyenera kwa ineyo kuganizira nonsenu mwa njira imeneyi, pakuti inu ndinu apamtima panga,+ ndiponso nonsenu ndinu ogawana+ nane m’kukoma mtima kwakukulu, m’maunyolo anga m’ndende,+ ndi pa kuteteza+ uthenga wabwino ndi kukhazikitsa mwalamulo ntchito ya uthenga wabwino.+  Mulungu ndiye mboni yanga kuti ndikufunitsitsa nditakuonani nonsenu. Ndikufunitsitsa nditakuonani ndi chikondi chachikulu+ ngati chimene Khristu Yesu ali nacho.  Ndipo ine ndikupitiriza kupemphera kuti chikondi chanu chipitirire kukula,+ limodzi ndi kudziwa zinthu molondola,+ komanso kuzindikira zinthu bwino kwambiri.+ 10  Chitani zimenezi kuti muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti,+ kuti mukhale opanda cholakwa+ ndi osakhumudwitsa+ ena kufikira tsiku la Khristu. 11  Muchite zimenezi kutinso mudzazidwe ndi zipatso zolungama+ kudzera mwa Yesu Khristu, kuti Mulungu akalemekezedwe ndi kutamandidwa.+ 12  Tsopano abale, ndikufuna mudziwe kuti zondichitikira zija, zathandiza kupititsa patsogolo uthenga wabwino+ m’malo moulepheretsa. 13  Moti, kumangidwa kwanga+ chifukwa cha Khristu, kwadziwika ndi aliyense+ pakati pa Asilikali Oteteza Mfumu ndi ena onse.+ 14  Abale ambiri mwa Ambuye, alimba mtima chifukwa cha kumangidwa kwanga, ndipo akuonetsa kulimba mtima kowonjezereka polankhula mawu a Mulungu mopanda mantha.+ 15  N’zoona kuti ena akulalikira Khristu mwakaduka ndiponso mwampikisano,+ koma ena akulalikira ndi cholinga chabwino.+ 16  Achiwiriwa akufalitsa Khristu chifukwa cha chikondi, pakuti akudziwa kuti ine ndili m’ndende muno kuti nditeteze+ uthenga wabwino. 17  Koma oyambawo akutero chifukwa cha mtima wokonda mikangano,+ osati ndi cholinga chabwino. Pakuti akungofuna kundiwonjezera masautso+ m’ndende muno. 18  Akatero ndiye kuti achita chiyani? Palibe! Mulimonse mmene zingakhalire, kaya ndi mwachiphamaso+ kapena m’choonadi, Khristu akufalitsidwabe.+ Choncho ine ndikukondwera. Ndipotu ndipitiriza kukondwera, 19  chifukwa ndikudziwa kuti mwa mapembedzero+ anu, ndi mwa mzimu wa Yesu Khristu,+ ndidzamasulidwa. 20  Zidzatero mogwirizana n’kuti ndikudikira mwachidwi,+ ndiponso ndili ndi chiyembekezo+ chakuti sindidzachititsidwa manyazi+ mwa njira iliyonse. Koma kuti mwa ufulu wanga wonse wa kulankhula,+ Khristu alemekezedwe mwa thupi langa tsopano, monga mmene zakhala zikuchitikira m’mbuyo monsemu.+ Kaya ndikhala ndi moyo kapena ndimwalira.+ 21  Pakuti kwa ine, ndikakhala moyo, ndikhalira moyo Khristu,+ ndipo ndikamwalira+ ndipindula. 22  Tsopano ngati ndipitirizabe kukhala ndi moyo m’thupi limene ndili naloli, ntchito ya manja anga idzawonjezeka,+ koma choti ndisankhe pamenepa, sindinena. 23  Ndapanikizika ndi zinthu ziwirizi,+ koma chimene ndikufuna ndicho kumasuka ndi kukhala ndi Khristu.+ Pakuti kunena zoona, chimenechi ndiye chabwino kwambiri.+ 24  Komabe, kukhalabe m’thupi kwa ine n’kofunika, makamaka chifukwa cha inu.+ 25  Choncho, pokhala wotsimikiza za chimenechi, ndikudziwa kuti ndikhalabe ndi moyo.+ Chotero ndidzakhala ndi inu nonse kuti mupite patsogolo,+ ndi kuti musangalale pa chikhulupiriro chanu. 26  Inde, kuti kusangalala kwanu kusefukire mwa Khristu Yesu, chifukwa cha ine pokhalanso limodzi ndi inu. 27  Chachikulu, makhalidwe anu akhale oyenera+ uthenga wabwino wa Khristu. Kuti kaya ndabwera kudzakuonani kapena pamene ine kulibe, ndizimva za inu, kuti mukulimbikira mu mzimu umodzi. Ndipo ndi mtima umodzi,+ mukulimbika pamodzi chifukwa cha chikhulupiriro cha uthenga wabwino. 28  Komanso simukuchita mantha m’njira iliyonse ndi okutsutsani.+ Kwa iwo, chimenechi ndi chizindikiro chakuti adzawonongedwa, koma kwa inu, ndi chizindikiro cha chipulumutso.+ Chizindikiro chimenechi n’chochokera kwa Mulungu. 29  Zili choncho chifukwa inu munapatsidwa mwayi. Osati mwayi wokhulupirira+ Khristu wokha, komanso wovutika+ chifukwa cha iye. 30  Ndiye chifukwa chake inunso muli ndi mavuto ofanana ndi amene munawaona kwa ine,+ ndiponso amene mukumva kuti ndikukumana nawo panopa.+

Mawu a M'munsi