3 Yohane 1:1-14

 Ine monga mkulu,+ ndikulembera wokondedwa Gayo, amene ndimamukonda kwambiri.+  Wokondedwa,+ ndimapemphera kuti zinthu zonse zikuyendere bwino+ ndiponso kuti ukhale ndi thanzi labwino,+ monga mmenenso moyo wako ukuyendera bwino.+  Ndinasangalala kwambiri pamene abale anabwera ndi kupereka umboni wa mmene ukupitira patsogolo m’choonadi, ndipo ndikusangalala chifukwa ukupitirizabe kuyenda m’choonadi.+  Palibe chimene chimandisangalatsa kwambiri kuposa kumva kuti ana anga akuyendabe m’choonadi.+  Wokondedwa, ukugwira ntchito mokhulupirika pa chilichonse chimene ukuchitira abale,+ amene sukuwadziwa n’komwe.+  Abalewo achitira umboni ku mpingo za chikondi chako. Anthu oterewa akamachoka, utsanzikane nawo m’njira imene Mulungu angasangalale nayo,+  chifukwa iwo anapita kukalalikira za dzina la Mulungu, ndipo sanatenge chilichonse+ kwa anthu a mitundu ina.  Choncho, ife tili ndi udindo wolandira bwino anthu amenewa ndi kuwachereza,+ kuti akhale antchito anzathu m’choonadi.+  Ndinalemba nkhani inayake kumpingo, koma Diotirefe, amene amakonda kukhala woyamba+ pakati pawo, salandira mwaulemu+ chilichonse chochokera kwa ife.+ 10  N’chifukwa chake ndikadzabwera, ndidzaulula ntchito zake zimene akupitirizabe kuchita.+ Iye amatinenera zamwano,+ komanso chifukwa chosakhutira ndi zinthu zimenezi, iye salandira abalewo+ mwaulemu, ndipo amene amafuna kulandira+ abalewo, amawatsekereza+ ndi kuwachotsa+ mumpingo. 11  Wokondedwa, usamatsanzire zinthu zoipa koma uzitsanzira zabwino.+ Munthu amene amachita zabwino ndi wochokera kwa Mulungu.+ Koma wochita zoipa sadziwa Mulungu.+ 12  Anthu onse amuchitira umboni Demetiriyo.+ Choonadinso chikumuchitira umboni. Ifenso tikuchitira umboni,+ ndipo iwenso ukudziwa kuti umboni umene timapereka ndi woona.+ 13  Ndinali ndi zambiri zoti ndikulembere, koma sindikufuna kuti ndipitirize kukulembera ndi inki ndi cholembera.+ 14  Koma ndikuyembekezera kukuona posachedwapa ndipo tidzalankhulana pamasom’pamaso.+ Mtendere ukhale nawe.+ Anzathu kuno akukupatsa moni.+ Iwenso undiperekere moni+ kwa anzathu kumeneko aliyense payekhapayekha.

Mawu a M'munsi