2 Yohane 1:1-13

 Ine monga mkulu,+ ndikulembera mayi wosankhidwa+ ndi Mulungu ndiponso ana ake amene ndimawakondadi.+ Ndipo si ine ndekha amene ndimawakonda. Onse amene adziwa choonadi amawakondanso.+  Timakukondani chifukwa cha choonadi chimene chili mumtima mwathu,+ ndipo chidzakhalabe ndi ife mpaka muyaya.+  Tidzalandira kukoma mtima kwakukulu,+ chifundo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate+ wathu ndi kwa Yesu Khristu Mwana wa Atate, limodzi ndi choonadi ndiponso chikondi.+  Ndikusangalala kwambiri kuti ndapeza ena mwa ana+ anu akuyenda m’choonadi,+ mogwirizana ndi lamulo limene tinalandira kwa Atate.+  Chotero ndikukupemphani mayi, kuti tonse tizikondana.+ Sindikukulemberani zimenezi ngati munthu amene ndikukupatsani lamulo latsopano,+ koma lomwe lija limene takhala nalo kuyambira pachiyambi.+  Ndipo chikondi chimenechi chimatanthauza kuti+ tiziyendabe motsatira malamulo ake.+ Monga mmene munamvera kuyambira pachiyambi, lamulo lake ndi lakuti mupitirize kuyenda m’chikondi,+  popeza anthu onyenga ambiri alowa m’dziko,+ amene amatsutsa zakuti kalero Yesu Khristu anabwera monga munthu.+ Amene amachita zimenezi ndi wonyenga+ uja ndiponso wokana Khristu.+  Samalani kuti musalephere kulandira mphoto ya zinthu zimene tazigwirira kale ntchito, kuti mudzalandire mphoto yokwanira.+  Aliyense amene amachita zosemphana ndi zimene Khristu amaphunzitsa,+ ndiye kuti akukana Mulungu.+ Koma amene amachita zinthu mogwirizana ndi zimene iye amaphunzitsa, amavomerezedwa ndi Atate ndiponso Mwana.+ 10  Wina akabwera kwa inu ndi chiphunzitso chosiyana ndi ichi, musamulandire m’nyumba zanu+ kapena kumupatsa moni.+ 11  Aliyense amene wamupatsa moni akugawana naye ntchito zake zoipazo.+ 12  Ngakhale kuti ndili ndi zambiri zoti ndikulembereni, sindikufuna kuzilemba papepala ndi inki,+ koma ndikuyembekezera kubwera kwa inu kuti ndidzalankhule nanu pamasom’pamaso,+ kuti mudzakhale ndi chimwemwe+ chokwanira.+ 13  Ana a m’bale wanu wosankhidwa ndi Mulungu, akupereka moni.+

Mawu a M'munsi