2 Mbiri 5:1-14

5  Pa mapeto pake, Solomo anamaliza ntchito yonse ya panyumba ya Yehova imene anayenera kugwira.+ Kenako Solomo anayamba kubweretsa zinthu zimene Davide bambo ake+ anaziyeretsa. Siliva, golide, ndi ziwiya zonse anaziika mosungira chuma cha panyumba ya Mulungu woona.+  Pa nthawi imeneyo m’pamene Solomo anauza akulu a Isiraeli,+ mitu yonse ya mafuko,+ ndi atsogoleri a nyumba za makolo+ a ana a Isiraeli kuti asonkhane ku Yerusalemu. Anawauza kuti akatenge likasa+ la pangano la Yehova ku+ Mzinda wa Davide,+ kutanthauza Ziyoni.+  Choncho anthu onse a mu Isiraeli anasonkhana kwa mfumu pachikondwerero cha m’mwezi wa 7.+  Akulu onse a Isiraeli anabwera,+ ndipo Alevi anayamba kunyamula Likasa.+  Ansembe achilevi+ ananyamula Likasa,+ chihema chokumanako,+ ndi ziwiya zonse zopatulika+ zimene zinali m’chihemacho.  Mfumu Solomo ndi msonkhano wonse wa Aisiraeli, onse amene anabwera atawaitana, anafika pamaso pa Likasa n’kuyamba kupereka nsembe+ zambiri za nkhosa ndi ng’ombe, zomwe sanathe kuziwerenga chifukwa chochuluka.  Kenako ansembe anabweretsa likasa la pangano la Yehova kumalo ake, kuchipinda chamkati+ cha nyumbayo, Malo Oyera Koposa,+ ndipo analiika pansi pa mapiko a akerubi.+  Mapiko a akerubiwo anali otambasukira pamwamba pa malo okhala Likasa, moti akerubiwo anatchinga pamwamba+ pa Likasa ndi pamwamba pa mitengo yake yonyamulira.+  Koma mitengo yonyamulirayo inali yaitali, moti nsonga zake zinali kuonekera ku Malo Oyera kutsogolo kwa chipinda chamkati, koma sizinali kuoneka kunja. Mitengo yonyamulirayo ikadali pomwepo mpaka lero.+ 10  Mu Likasalo munalibe chilichonse kupatulapo miyala iwiri yosema+ imene Mose anaikamo ku Horebe.+ Anaiikamo nthawi imene Yehova anachita pangano+ ndi ana a Isiraeli, pamene anali kutuluka m’dziko la Iguputo.+ 11  Tsopano ansembe anatuluka m’malo oyera (chifukwa ansembe onse amene analipo anali atadziyeretsa+ ndipo panalibe chifukwa choti atumikire motsatira magulu awo).+ 12  Ndipo Alevi+ oimba a m’gulu la Asafu,+ Hemani,+ Yedutuni,+ ana awo ndi abale awo, onsewa atavala zovala zabwino kwambiri atanyamula zinganga,+ zoimbira za zingwe+ ndi azeze,+ anaimirira kum’mawa kwa guwa lansembe pamodzi ndi ansembe okwanira 120 oimba malipenga.+ 13  Tsopano anthu oimba malipenga ndi oimba pakamwa anayamba kuimba mogwirizana+ n’kumamveka ngati mawu amodzi otamanda ndi kuthokoza Yehova. Komanso anayamba kuimba+ ndi malipenga, zinganga, ndi zoimbira zina potamanda+ Yehova ndi mawu akuti, “chifukwa iye ndi wabwino,+ pakuti kukoma mtima kwake kosatha+ kudzakhala mpaka kalekale.” Kenako mtambo unadzaza nyumbayo,+ nyumba ya Yehova.+ 14  Chifukwa cha mtambowo,+ ansembewo analephera kupitiriza kutumikira, popeza ulemerero+ wa Yehova unadzaza nyumba ya Mulungu woona.

Mawu a M'munsi