2 Mbiri 34:1-33

34  Yosiya+ anali ndi zaka 8+ pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka 31 ku Yerusalemu.+  Iye anachita zoyenera pamaso pa Yehova+ ndipo anayenda m’njira za Davide kholo lake.+ Sanapatukire mbali ya kudzanja lamanja kapena lamanzere.+  M’chaka cha 8 cha ulamuliro wa Yosiya, iye akadali mnyamata,+ anayamba kufunafuna+ Mulungu wa Davide kholo lake. M’chaka cha 12 anayamba kuyeretsa+ Yuda ndi Yerusalemu pochotsa malo okwezeka,+ mizati yopatulika,+ zifaniziro zogoba,+ ndi zifaniziro zopangidwa ndi zitsulo zosungunula.  Kuwonjezera apo, anthu anagwetsa maguwa ansembe+ a Abaala+ pamaso pake, ndipo zofukizira+ zimene zinali pamwamba pa maguwawo iye anazigumula. Mizati yopatulika,+ zifaniziro zogoba,+ ndi zifaniziro zopangidwa ndi zitsulo zosungunula, anaziphwanya n’kuziperapera.+ Phulusa lakelo analiwaza pamanda a anthu amene anali kupereka nsembe kwa zinthu zimenezi.+  Mafupa+ a ansembe anawatentha pamaguwa awo ansembe.+ Choncho Yosiya anayeretsa Yuda ndi Yerusalemu.  Komanso, m’mizinda ya Manase,+ Efuraimu,+ Simiyoni, mpaka Nafitali, ndi m’malo onse owonongedwa ozungulira mizindayi,  Yosiya anagwetsamo maguwa ansembe+ ndi mizati yopatulika.+ Zifaniziro zogoba+ anaziphwanya n’kuziperapera,+ ndipo anagumula zofukizira zonse+ m’dziko lonse la Isiraeli. Atatero anabwerera ku Yerusalemu.  M’chaka cha 18+ cha ulamuliro wake, atayeretsa dzikolo ndi nyumba ya Mulungu, iye anatuma Safani+ mwana wa Azaliya, Maaseya mkulu wa mzinda, ndi Yowa mwana wa Yowahazi wolemba zochitika, kuti akakonze+ nyumba ya Yehova Mulungu wake.  Iwo anapita kwa Hilikiya+ mkulu wa ansembe n’kukapereka ndalama zimene anthu anali kubweretsa kunyumba ya Mulungu, zimene Alevi omwe anali alonda a pakhomo,+ anatolera ku fuko la Manase,+ la Efuraimu,+ kwa Aisiraeli onse,+ kwa Ayuda onse, ku fuko la Benjamini, ndi kwa anthu onse okhala mu Yerusalemu. 10  Kenako anapereka ndalamazo m’manja mwa ogwira ntchito osankhidwa a m’nyumba ya Yehova.+ Ndiyeno iwowa anapereka ndalamazo kwa anthu amene anali kugwira ntchito m’nyumba ya Yehova, omwe anazigwiritsa ntchito yokonzera nyumbayo. 11  Anthu ogwira ntchitowa anapereka ndalamazo kwa amisiri ndi kwa omanga+ nyumba kuti agulire miyala yosema+ ndi matabwa opangira zida zomangira zinthu pamodzi, ndiponso kuti akhome mitanda m’nyumba zimene mafumu+ a Yuda anazilekerera kuti ziwonongeke. 12  Anthuwo anali kugwira ntchitoyo mokhulupirika.+ Atsogoleri awo oti aziwayang’anira anali Yahati ndi Obadiya, omwe anali Alevi ochokera mwa ana a Merari,+ ndiponso Zekariya ndi Mesulamu ochokera mwa ana a Akohati.+ Aleviwo, amene aliyense wa iwo anali katswiri wodziwa kuimba ndi zipangizo zoimbira,+ 13  anali kuyang’anira+ anthu onyamula katundu+ ndi anthu onse ogwira ntchito zosiyanasiyana. Panalinso Alevi+ amene anali alembi,+ akapitawo, ndi alonda a pazipata.+ 14  Pamene anali kutulutsa ndalama+ zimene zinali kubwera kunyumba ya Yehova, wansembe Hilikiya+ anapeza buku+ la chilamulo cha Yehova+ loperekedwa ndi dzanja la Mose.+ 15  Chotero Hilikiya anauza Safani+ mlembi kuti: “Ndapeza buku la chilamulo m’nyumba ya Yehova!” Pamenepo Hilikiya anapereka bukulo kwa Safani. 16  Tsopano Safani anapititsa bukulo kwa mfumu n’kuiuza kuti: “Atumiki anu akuchita zonse zimene zaikidwa m’manja mwawo. 17  Iwo akumakhuthula ndalama zimene akuzipeza m’nyumba ya Yehova n’kuzipereka m’manja mwa amuna osankhidwa ndiponso m’manja mwa ogwira ntchito.”+ 18  Kenako Safani mlembi anauza mfumuyo kuti: “Pali buku+ limene wansembe Hilikiya wandipatsa.”+ Ndiyeno Safani anayamba kuwerenga bukulo pamaso pa mfumu.+ 19  Mfumuyo itangomva mawu a chilamulowo, nthawi yomweyo inang’amba zovala zake.+ 20  Kenako mfumuyo inalamula Hilikiya,+ Ahikamu+ mwana wa Safani, Abidoni mwana wa Mika, Safani+ mlembi,+ ndi Asaya+ mtumiki wa mfumu, kuti: 21  “Pitani mukafunsire+ kwa Yehova m’malo mwa ineyo,+ ndiponso m’malo mwa anthu amene atsala mu Isiraeli ndi mu Yuda. Mukafunse zokhudza mawu a m’buku+ limene lapezekali, chifukwa mkwiyo wa Yehova+ umene akuyenera kutitsanulira ndi waukulu, popeza makolo athu sanasunge mawu a Yehova. Iwo sanachite zonse zimene zinalembedwa m’buku ili.”+ 22  Chotero Hilikiya pamodzi ndi anthu amene mfumu inatchula anapita kukanena zimenezi kwa Hulida+ mneneri wamkazi.+ Hulida anali mkazi wa Salumu yemwe anali wosamalira zovala,+ mwana wa Tikiva, mwana wa Harihasi, ndipo Hulidayo anali kukhala kumbali yatsopano ya mzinda wa Yerusalemu. 23  Iye anawauza kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Kauzeni munthu amene wakutumani kwa ineyo kuti: 24  “Yehova wanena kuti, ‘Ndibweretsa tsoka+ pamalo ano ndi anthu ake,+ pokwaniritsa matemberero onse+ amene analembedwa m’buku limene anawerenga pamaso pa mfumu ya Yuda,+ 25  chifukwa chakuti andisiya+ n’kumakafukiza nsembe yautsi kwa milungu ina+ kuti andikwiyitse+ ndi ntchito zonse za manja awo.+ Choncho nditsanulira mkwiyo wanga+ pamalo ano ndipo suzimitsidwa.’”+ 26  Mfumu ya Yuda imene yakutumani kuti mudzafunse kwa Yehova, mukaiuze kuti, “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti,+ ‘Ponena za mawu+ amene wamvawo, 27  chifukwa chakuti mtima wako+ unali wofewa ndipo unadzichepetsa+ chifukwa cha Mulungu utamva mawu ake okhudza malo ano ndi anthu ake, ndipo unadzichepetsa pamaso panga+ n’kung’amba+ zovala zako ndi kulira pamaso panga, ineyo ndamva,+ ndiwo mawu a Yehova. 28  Ine ndidzakugoneka pamodzi ndi makolo ako, ndipo ndithu udzaikidwa m’manda ako mu mtendere.+ Maso ako sadzaona tsoka+ lonse limene ndikulibweretsa pamalo ano ndi anthu ake.’”’”+ Anthuwo anabweretsa mawuwo kwa mfumuyo. 29  Ndiyeno mfumuyo inatumiza uthenga kwa akulu onse a Yuda ndi Yerusalemu n’kuwasonkhanitsa pamodzi.+ 30  Itatero, mfumuyo inapita kunyumba ya Yehova+ limodzi ndi amuna onse a ku Yuda, anthu okhala ku Yerusalemu, ansembe,+ Alevi, ndi anthu onse, wamng’ono ndi wamkulu yemwe. Tsopano mfumuyo inayamba kuwawerengera+ mawu onse a m’buku la pangano limene linapezeka panyumba ya Yehova.+ 31  Mfumuyo inaimirirabe pamalo ake+ ndipo inachita pangano+ pamaso pa Yehova, kuti idzatsatira Yehova ndi kusunga malamulo+ ake ndi maumboni*+ ake. Inanenanso kuti idzachita+ zimenezi ndi mtima wake wonse+ ndi moyo wake wonse,+ mogwirizana ndi mawu a pangano olembedwa m’bukulo.+ 32  Kuwonjezera apo, mfumuyo inachititsa onse amene anali ku Yerusalemu ndi ku Benjamini kuti avomereze panganolo. Anthu okhala ku Yerusalemuwo anachita mogwirizana ndi pangano la Mulungu, Mulungu wa makolo awo.+ 33  Atatero, Yosiya anachotsa zonyansa zonse+ m’mayiko onse a ana a Isiraeli.+ Anachititsanso anthu onse amene anali mu Isiraeli kuti ayambe kutumikira Yehova Mulungu wawo. M’masiku ake onse, iwo sanasiye kutsatira Yehova Mulungu wa makolo awo.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “zikumbutso.”