2 Mbiri 32:1-33

32  Pambuyo pa zimenezi ndiponso pambuyo pa ntchito zokhulupirika+ za Hezekiya, Senakeribu+ mfumu ya Asuri+ anabwera n’kudzazungulira Yuda ndipo anamanga misasa pafupi ndi mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+ Iye anali kuganiza zogonjetsa mizindayo kuti ikhale yake.  Hezekiya ataona kuti Senakeribu wabwera n’cholinga chochita nkhondo+ ndi mzinda wa Yerusalemu,  anagwirizana ndi akalonga ake+ ndi amuna ake amphamvu kuti atseke akasupe a madzi amene anali kunja kwa mzindawo,+ choncho iwo anamuthandiza.  Chotero anthu ambiri anasonkhana ndipo anapita kukatseka akasupe onse ndi mtsinje+ umene unkasefukira kudutsa pakati pa dzikolo, popeza anati: “Sitikufuna kuti mafumu a Asuri akabwera adzapeze madzi ochuluka.”  Kuwonjezera apo, iye analimba mtima n’kumanga makoma onse a mpanda amene anali ogumuka.+ Anamanga nsanja+ pamwamba pa mpandawo ndipo kunja kwake anamangako mpanda wina.+ Anakonzanso Chimulu cha Dothi*+ cha mu Mzinda wa Davide ndipo anapanga zida+ zambiri ndi zishango.+  Kenako anaika akuluakulu a asilikali+ kuti aziyang’anira anthuwo, ndipo anawauza kuti akumane naye pabwalo+ la mzindawo limene linali pachipata. Kumeneko iye anawalankhula mowalimbitsa mtima+ kuti:  “Limbani mtima ndipo muchite zinthu mwamphamvu.+ Musaope+ kapena kuchita mantha+ ndi mfumu ya Asuri+ ndi khamu lalikulu limene ili nalo,+ chifukwa ife tili ndi ambiri kuposa amene ali ndi mfumuyo.  Iyo ikudalira mphamvu za anthu,*+ koma ife tili ndi Yehova Mulungu wathu+ kuti atithandize ndi kutimenyera nkhondo zathu.”+ Pamenepo anthuwo anayamba kulimba mtima chifukwa cha mawu a Hezekiya mfumu ya Yuda.+  Pambuyo pa zimenezi, Senakeribu+ mfumu ya Asuri ali ku Lakisi+ pamodzi ndi asilikali ake onse,+ anatumiza atumiki ake ku Yerusalemu kwa Hezekiya mfumu ya Yuda ndi kwa anthu onse okhala ku Yudeya ku Yerusalemu. Anawatuma kukanena kuti: 10  “Senakeribu mfumu ya Asuri yanena kuti,+ ‘Kodi mukudalira chiyani poti mukungokhala mosatekeseka, Yerusalemu atazunguliridwa?+ 11  Hezekiyatu+ akungokunyengererani+ kuti mufe ndi njala ndi ludzu pokuuzani kuti: “Yehova Mulungu wathu atipulumutsa m’manja mwa mfumu ya Asuri.”+ 12  Kodi si Hezekiya yemweyo amene anachotsa malo ake okwezeka+ ndi maguwa ake ansembe+ kenako n’kuuza anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu kuti: “Muziwerama+ pamaso pa guwa lansembe limodzi lokha+ ndipo nsembe yautsi muzifukiza pamenepo”?+ 13  Kodi simukudziwa zimene ineyo ndi makolo anga tinachita kwa anthu onse a mayiko ena?+ Kodi milungu+ ya mitundu ya mayiko ena inatha kupulumutsa mayiko awo m’manja mwanga? 14  Ndi mulungu uti pa milungu ya mitundu imeneyi, yomwe makolo anga anaiwononga, yemwe anatha kupulumutsa anthu ake m’manja mwanga, kuti Mulungu wanu athe kukupulumutsani m’manja mwanga?+ 15  Tsopano musalole kuti Hezekiya akupusitseni+ kapena kukunyengererani+ chonchi ndipo musamukhulupirire, chifukwa palibe ufumu uliwonse kapena mulungu wa mtundu uliwonse wa anthu amene anatha kupulumutsa anthu akewo m’manja mwanga ndiponso m’manja mwa makolo anga. Ndiye mukuganiza kuti Mulungu wanu angakupulumutseni m’manja mwanga?’”+ 16  Atumiki a Senakeribuwo analankhula zinthu zinanso zonyoza Yehova Mulungu woona+ ndi Hezekiya mtumiki wake. 17  lye analembanso makalata+ onyoza Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ komanso omutonza kuti: “Mofanana ndi milungu+ ya mitundu ya mayiko ena imene sinapulumutse anthu ake m’manja mwanga,+ Mulungu wa Hezekiya sapulumutsa anthu ake m’manja mwanga.” 18  Iwo+ anapitiriza kulankhula mokuwa+ m’chilankhulo cha Ayuda,+ kwa anthu a ku Yerusalemu amene anali pamwamba pa mpanda, kuti awachititse mantha+ ndi kuwasokoneza n’cholinga choti alande mzindawo. 19  Anapitiriza kulankhula monyoza+ Mulungu wa Yerusalemu+ mofanana ndi mmene ankanyozera milungu ya mitundu ya anthu a padziko lapansi, yopangidwa ndi manja a anthu.+ 20  Koma mfumu Hezekiya+ ndi mneneri+ Yesaya+ mwana wa Amozi,+ anali kupempherera nkhani imeneyi+ ndi kufuulira Mulungu kumwamba kuti awapulumutse.+ 21  Tsopano Yehova anatumiza mngelo+ yemwe anapha mwamuna aliyense wamphamvu ndi wolimba mtima,+ komanso mtsogoleri ndi mkulu wa asilikali aliyense mumsasa wa mfumu ya Asuri,+ moti mfumuyo inabwerera kwawo mwamanyazi. Kenako inalowa m’kachisi wa mulungu wake ndipo ili mmenemo, ena mwa ana ake anaipha ndi lupanga.+ 22  Chotero, Yehova anapulumutsa Hezekiya ndi anthu okhala ku Yerusalemu m’manja mwa Senakeribu mfumu ya Asuri+ komanso m’manja mwa ena onse, ndipo anawapatsa mpumulo kwa adani awo onse owazungulira.+ 23  Pambuyo pa zimenezi, panali anthu ambiri amene ankabweretsa mphatso+ kwa Yehova ku Yerusalemu ndi zinthu zabwinozabwino kwa Hezekiya mfumu ya Yuda,+ moti iye anakwezeka+ m’maso mwa mitundu yonse. 24  M’masiku amenewo, Hezekiya anadwala mpaka kutsala pang’ono kufa,+ ndipo anapemphera+ kwa Yehova. Choncho iye analankhula ndi Hezekiya+ n’kumupatsa chizindikiro cholosera zam’tsogolo.+ 25  Koma Hezekiya sanabwezere zabwino zimene anachitiridwa,+ pakuti mtima wake unayamba kudzikuza+ ndipo mkwiyo wa Mulungu+ unayakira iyeyo, Yuda, ndi Yerusalemu. 26  Komabe, Hezekiya anadzichepetsa+ pambuyo pa kudzikuza kwa mtima wake. Anadzichepetsa limodzi ndi anthu a ku Yerusalemu, ndipo mkwiyo wa Yehova sunawagwere m’masiku a Hezekiya.+ 27  Hezekiya anakhala ndi chuma chambiri ndi ulemerero wochuluka zedi.+ Anadzimangira nyumba zosungiramo siliva, golide,+ miyala yamtengo wapatali,+ mafuta a basamu,+ zishango,+ ndi zinthu zonse zabwinozabwino.+ 28  Anamanganso mosungira+ mbewu, vinyo watsopano+ ndi mafuta, ndipo anamanganso makola+ a zinyama zonse zosiyanasiyana ndi a magulu a ziweto. 29  Anakhala ndi mizinda ndiponso nkhosa+ ndi ng’ombe+ zochuluka, chifukwa Mulungu anam’patsa katundu wambiri.+ 30  Hezekiya ndiye anatseka+ kasupe wapamtunda wa madzi+ a ku Gihoni+ ndipo anawapatutsa n’kuwalunjikitsa kumunsi kumadzulo, ku Mzinda wa Davide.+ Ntchito iliyonse imene Hezekiya anali kuchita inali kumuyendera bwino.+ 31  Ndiyeno zinachitika kuti pamene akalonga a ku Babulo+ anatumiza nthumwi zawo kwa iye,+ kuti zikam’funse za chizindikiro cholosera zam’tsogolo+ chimene chinachitika m’dzikolo, Mulungu woona anamusiya+ kuti amuyese+ ndi kuona zonse zimene zinali mumtima mwake.+ 32  Nkhani zina+ zokhudza Hezekiya ndi zochita zake zosonyeza kukoma mtima kosatha,+ zinalembedwa m’masomphenya a mneneri Yesaya mwana wa Amozi,+ m’Buku+ la Mafumu a Yuda ndi Isiraeli. 33  Pomalizira pake, Hezekiya anagona pamodzi ndi makolo ake,+ ndipo anamuika m’manda pachitunda chopita kumanda a ana a Davide.+ Pamaliro ake, Ayuda onse ndi anthu okhala ku Yerusalemu anamusonyeza ulemu waukulu.+ Kenako Manase+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 5:9.
Mawu ake enieni, “dzanja la thupi lanyama.”