2 Mbiri 29:1-36

29  Hezekiya+ anakhala mfumu ali ndi zaka 25, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 29. Mayi ake dzina lawo linali Abiya mwana wa Zekariya.+  Iye anapitiriza kuchita zoyenera pamaso pa Yehova,+ mogwirizana ndi zonse zimene Davide kholo lake anachita.+  M’chaka choyamba cha ulamuliro wake, m’mwezi woyamba,* iye anatsegula zitseko za nyumba ya Yehova n’kuyamba kuzikonza.+  Kenako anasonkhanitsa pamodzi ansembe ndi Alevi pabwalo+ mbali yakum’mawa.  Ndiyeno anawauza kuti: “Tamverani Alevi inu. Dziyeretseni+ ndipo muyeretsenso nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo anu. Mutulutse chinthu chodetsedwa m’malo oyera.+  Pakuti makolo athu achita zosakhulupirika+ ndipo achita zoipa pamaso pa Yehova Mulungu wathu.+ Iwo anamusiya+ n’kufulatira chihema chopatulika cha Yehova+ n’kulozetsako nkhongo.  Anatseka zitseko+ za khonde, anazimitsa nyale,+ ndiponso anasiya kupsereza zofukiza+ ndi kupereka nsembe zopsereza kwa Mulungu wa Isiraeli m’malo oyera.+  Chotero mkwiyo wa Yehova+ unayakira Yuda ndi Yerusalemu, moti anawachititsa kuti akhale chinthu chonthunthumiritsa,+ chinthu chodabwitsa,+ ndiponso chinthu chochititsa anthu kuimba mluzu,+ monga momwe mukuonera ndi maso anu.  Pa chifukwa chimenechi, makolo athu anaphedwa ndi lupanga+ ndipo ana athu aamuna ndi aakazi ndiponso akazi athu anapita ku ukapolo.+ 10  Tsopano ineyo ndikufunitsitsa mumtima mwanga kuchita pangano+ ndi Yehova Mulungu wa Isiraeli, kuti mkwiyo wake umene watiyakira utichokere. 11  Ndiyeno inu ana anga musapumule,+ chifukwa inu ndi amene Yehova wakusankhani kuti muziima pamaso pake ndi kum’tumikira+ ndiponso kuti mukhalebe atumiki ake+ ndi ofukiza nsembe yautsi.”+ 12  Pamenepo Alevi+ anaimirira. Alevi ake anali Mahati mwana wa Amasai ndi Yoweli mwana wa Azariya ochokera mwa ana a Kohati.+ Kuchokera mwa ana a Merari,+ panali Kisi mwana wa Abidi ndi Azariya mwana wa Yehaleleli. Kuchokera mwa Agerisoni+ panali Yowa mwana wa Zima ndi Edeni mwana wa Yowa. 13  Kuchokera mwa ana a Elizafana+ panali Simuri ndi Yeweli. Kuchokera mwa ana a Asafu+ panali Zekariya ndi Mataniya. 14  Kuchokera mwa ana a Hemani+ panali Yehiela ndi Simeyi. Kuchokera mwa ana a Yedutuni+ panali Semaya ndi Uziyeli. 15  Iwo anasonkhanitsa abale awo pamodzi n’kudziyeretsa.+ Ndiyeno anabwera kudzayeretsa+ nyumba ya Yehova mogwirizana ndi lamulo la mfumu potsatira mawu+ a Yehova. 16  Tsopano ansembe analowa m’nyumba ya Yehova kukayeretsamo, ndipo anatulutsa zonyansa zonse zimene anazipeza m’kachisi wa Yehova n’kupita nazo pabwalo+ la nyumba ya Yehova. Kenako Alevi anazitenga n’kupita nazo kunja kuchigwa cha Kidironi.+ 17  Chotero anayamba kuyeretsa pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, ndipo pa tsiku la 8 la mweziwo anafika pakhonde+ la nyumba ya Yehova. Choncho anayeretsa nyumba ya Yehova m’masiku 8. Pa tsiku la 16 la mwezi woyamba+ anamaliza ntchitoyo. 18  Atatero analowa kumene kunali mfumu Hezekiya n’kukaiuza kuti: “Tayeretsa nyumba yonse ya Yehova, guwa lansembe+ zopsereza ndi ziwiya zake zonse,+ ndiponso tebulo+ loikapo mkate wosanjikiza ndi ziwiya zake zonse.+ 19  Ziwiya zonse+ zimene Mfumu Ahazi+ anasiya kuzigwiritsira ntchito mu ulamuliro wake chifukwa cha kusakhulupirika kwake,+ tazikonza ndi kuziyeretsa+ ndipo zili pafupi ndi guwa lansembe la Yehova.” 20  Tsopano mfumu Hezekiya+ inadzuka m’mawa kwambiri+ n’kusonkhanitsa akalonga+ a mzindawo, n’kupita kunyumba ya Yehova. 21  Iwo anabweretsa ng’ombe zamphongo 7,+ nkhosa zamphongo 7, ana a nkhosa amphongo 7 ndi mbuzi zamphongo 7 kuti azipereke monga nsembe yamachimo+ ya ufumuwo, ya malo opatulika, ndi ya Yuda. Chotero Hezekiya anauza ana a Aroni, omwe anali ansembe,+ kuti apereke nsembeyo paguwa lansembe la Yehova. 22  Iwo anapha+ ng’ombezo ndipo ansembe anatenga magazi+ ake n’kuwaza+ paguwa lansembe. Kenako anapha nkhosa zamphongo+ zija n’kuwaza magazi ake paguwa lansembe. Atatero anapha ana a nkhosa amphongo aja n’kuwaza magazi+ ake paguwa lansembe. 23  Kenako anatenga mbuzi zamphongo+ za nsembe yamachimo zija n’kuzibweretsa pafupi ndi mfumu ndi mpingo wonse, ndipo iwo anasanjika manja awo pambuzizo.+ 24  Tsopano ansembe anazipha n’kuzipereka nsembe yamachimo pamodzi ndi magazi ake paguwa lansembe kuti aphimbe machimo a Aisiraeli onse,+ popeza mfumu inati nsembe yopsereza ndi yamachimoyo+ ikhale ya Aisiraeli onse.+ 25  Pa nthawi imeneyi, Hezekiya anaika Alevi+ panyumba ya Yehova atanyamula zinganga,+ zoimbira za zingwe,+ ndi azeze.+ Iwo anali kutsatira ndondomeko yoimbira imene anaikhazikitsa Davide,+ Gadi+ yemwe anali wamasomphenya wa mfumu, ndi mneneri Natani,+ popeza ndondomekoyo inachokera kwa Yehova kudzera mwa aneneri ake.+ 26  Choncho Aleviwo anaimirirabe atanyamula zipangizo zoimbira+ za Davide. Iwo anaimirira pamodzi ndi ansembe omwe ananyamula malipenga.+ 27  Kenako Hezekiya anawauza kuti apereke nsembe yopsereza paguwa lansembe. Atayamba kupereka nsembe yopserezayo, nyimbo+ ya Yehova inayamba kuimbidwa limodzi ndi malipenga amene ankatsatira zipangizo zoimbira za Davide mfumu ya Isiraeli. 28  Mpingo wonse unagwada+ n’kuwerama pamene nyimboyo inali kuimbidwa mokuwa+ ndiponso pamene malipenga anali kulizidwa mokweza. Mpingowo unakhala chowerama choncho mpaka anamaliza kupereka nsembe yopsereza. 29  Atangomaliza kupereka nsembeyo, mfumu ndi onse amene anali nayo anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi.+ 30  Tsopano mfumu Hezekiya ndi akalonga+ anauza Alevi kuti atamande Yehova ndi mawu a Davide+ ndi a wamasomphenya Asafu.+ Chotero iwo anayamba kutamanda Mulungu mosangalala+ ndipo anakhalabe chogwada atawerama mpaka mphumi zawo pansi.+ 31  Pomalizira pake Hezekiya anati: “Tsopano mwayeneretsedwa kuti mukhale ansembe+ otumikira Yehova. Bweretsani nsembe zoyamikira+ ndi nsembe zina+ kunyumba ya Yehova.” Ndiyeno mpingowo unayamba kubweretsa nsembe zoyamikira ndi nsembe zina, ndipo aliyense wa mtima wofunitsitsa anali kubweretsa nsembe zopsereza.+ 32  Nsembe zopsereza zimene mpingowo unabweretsa zinakwana ng’ombe 70, nkhosa zamphongo 100, ndi ana a nkhosa amphongo 200. Zonsezi anazipereka kwa Yehova monga nsembe yopsereza.+ 33  Anabweretsanso zopereka zopatulika zokwana ng’ombe 600 ndi nkhosa 3,000. 34  Koma ansembe+ anali ochepa kwambiri ndipo sanathe kusenda nyama zonse za nsembe zopsereza.+ Choncho abale awo+ Alevi anawathandiza mpaka ntchitoyo inatha+ ndiponso kufikira pamene ansembewo anadziyeretsa,+ popeza Alevi ankafunitsitsa kudziyeretsa kuposa ansembe.+ 35  Komanso, nsembe zopsereza+ ndiponso mafuta+ a nsembe zachiyanjano+ zinali zambiri. Nazonso nsembe zachakumwa+ zimene zinaperekedwa limodzi ndi nsembe zopserezazo zinali zambiri. Chotero utumiki wa panyumba ya Yehova unakonzedwa.+ 36  Choncho Hezekiya ndi anthu onse anasangalala chifukwa Mulungu woona anathandiza anthuwo,+ pakuti zinthuzo zinachitika mosayembekezereka.+

Mawu a M'munsi

Umenewu ndi mwezi wa Abibu kapena kuti Nisani, umene ndi mwezi woyamba pa kalendala yopatulika ya Ayuda kuyambira pamene anachoka ku Iguputo. Mwezi wa Abibu umayambira chakumapeto kwa mwezi wa March mpaka mkatikati mwa mwezi wa April. Onani Zakumapeto 13.