2 Mbiri 27:1-9

27  Yotamu+ anali ndi zaka 25 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 16. Mayi ake dzina lawo linali Yerusa+ mwana wa Zadoki.  Iye anapitiriza kuchita zoyenera pamaso pa Yehova.+ Anachita mogwirizana ndi zonse zimene Uziya bambo ake anachita,+ kungoti sanakalowe m’kachisi wa Yehova.+ Koma anthu anali kuchitabe zoipa.+  Iye anamanga chipata chakumtunda+ cha nyumba ya Yehova ndipo pakhoma la Ofeli+ anamangapo zinthu zambiri.  M’dera lamapiri la Yuda+ anamangamo mizinda+ ndipo m’dera lankhalango+ anamangamo malo okhala ndi mipanda yolimba kwambiri+ ndiponso nsanja.+  Yotamu anamenyana ndi mfumu ya ana a Amoni+ ndipo pomalizira pake anawaposa mphamvu. Choncho chaka chimenecho ana a Amoni anam’patsa matalente a siliva* 100 ndi tirigu+ wokwana miyezo 10,000 ya kori,*+ komanso balere wokwana miyezo 10,000 ya kori.+ Izi n’zimene ana a Amoni anamulipira. Anamulipiranso zomwezi m’chaka chachiwiri ndi chachitatu.+  Chotero Yotamu anapitiriza kulimbitsa ufumu wake, popeza anakonza njira zake pamaso pa Yehova Mulungu wake.+  Nkhani zina zokhudza Yotamu,+ nkhondo zake ndi njira zake zonse, zinalembedwa m’Buku+ la Mafumu a Isiraeli ndi Yuda.  Iye anali ndi zaka 25 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka 16 ku Yerusalemu.+  Pomalizira pake, Yotamu anagona pamodzi ndi makolo ake+ ndipo anaikidwa m’manda mu Mzinda wa Davide.+ Kenako Ahazi+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 12.
Onani Zakumapeto 12.