2 Mbiri 26:1-23

26  Kenako anthu onse+ a ku Yuda anatenga Uziya+ yemwe pa nthawiyo anali ndi zaka 16, n’kumulonga+ ufumu m’malo mwa bambo ake Amaziya.+  Mfumu itagona ndi makolo ake,+ Uziya anamanganso mzinda wa Eloti+ n’kuubwezeretsa ku Yuda.  Uziya+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 16, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 52. Amayi ake anali a ku Yerusalemu, ndipo dzina lawo linali Yekoliya.+  Iye anapitiriza kuchita zoyenera pamaso pa Yehova,+ mogwirizana ndi zonse zimene Amaziya bambo ake anachita.+  Uziya anali kufunafuna+ Mulungu m’masiku a Zekariya yemwe anali kumulangiza kuti aziopa Mulungu woona.+ M’masiku amene iye anafunafuna Yehova, Mulungu woonayo anachititsa kuti zinthu zizimuyendera bwino.+  Iye anapita kukamenyana ndi Afilisiti+ ndipo anagumula mpanda wa ku Gati,+ wa ku Yabine+ ndi wa ku Asidodi.+ Kenako anamanga mizinda m’chigawo cha Asidodi+ ndiponso pakati pa Afilisiti.  Mulungu woona anapitiriza kumuthandiza+ kumenyana ndi Afilisiti, Aluya+ amene anali kukhala ku Gurubaala, ndiponso Ameyuni.+  Ndiyeno Aamoni+ anayamba kupereka msonkho+ kwa Uziya. Pomalizira pake, kutchuka kwake+ kunafika mpaka ku Iguputo chifukwa anasonyeza mphamvu zochuluka zedi.  Kuwonjezera apo Uziya anamanga nsanja+ ku Yerusalemu pafupi ndi Chipata cha Pakona,+ Chipata cha Kuchigwa,+ ndiponso pafupi ndi Mchirikizo wa Khoma, ndipo nsanjazo anazilimbitsa. 10  Iye anamanganso nsanja+ m’chipululu ndipo anakumba zitsime zambiri (popeza anakhala ndi ziweto zambiri). Anapanganso zomwezo ku Sefela+ ndi kudera lokwererapo. Kumapiri ndi ku Karimeli kunali alimi ndi anthu osamalira minda ya mpesa popeza iye ankakonda ulimi. 11  Komanso Uziya anali ndi asilikali amene ankapita kunkhondo m’magulumagulu.+ Yeyeli mlembi+ ndi Maaseya anawerenga ndi kulemba mayina+ asilikali a m’magulu amenewa. Amuna awiri amenewa anali kuyang’aniridwa+ ndi Hananiya mmodzi wa akalonga a mfumu.+ 12  Atsogoleri onse a nyumba za makolo awo,+ amuna amphamvu+ ndi olimba mtima,+ analipo 2,600. 13  Atsogoleri amenewa ankayang’anira gulu lankhondo la asilikali 307,500, omenya nkhondo mwamphamvu pothandiza mfumu kulimbana ndi adani.+ 14  Uziya anapitiriza kukonzera gulu lankhondo lonselo zishango,+ mikondo ing’onoing’ono,+ zisoti,+ zovala za mamba achitsulo,+ mauta,+ ndi miyala yoponya ndi gulaye.*+ 15  Kuwonjezera apo, ku Yerusalemu anapanga makina ankhondo opangidwa ndi anthu aluso, oti aziwaika pansanja+ ndi pamakona a mpanda, kuti aziponyera mivi ndi miyala ikuluikulu. Chotero anatchuka+ mpaka kutali kwambiri, popeza anathandizidwa kwambiri mpaka anakhala wamphamvu. 16  Koma atangokhala wamphamvu, mtima wake unadzikuza+ mpaka kufika pom’pweteketsa.+ Choncho anachita zosakhulupirika kwa Yehova Mulungu wake ndipo anapita m’kachisi wa Yehova kukafukiza paguwa lansembe zofukiza.+ 17  Nthawi yomweyo wansembe Azariya pamodzi ndi ansembe a Yehova okwanira 80, amuna amphamvu, anam’tsatira. 18  Kenako iwo anatsutsa mfumu Uziya+ n’kuiuza kuti: “Mfumu Uziya, si ntchito yanu+ kufukiza kwa Yehova koma ntchito yofukizayi ndi ya ansembe, ana a Aroni,+ amene anayeretsedwa. Tulukani m’nyumba yopatulikayi popeza mwachita zosakhulupirika, ndipo sizikubweretserani ulemerero uliwonse+ pamaso pa Yehova Mulungu.” 19  Koma Uziya anakwiya kwambiri+ atanyamula chiwaya chofukizira+ m’manja mwake. Atawakwiyira choncho ansembewo, khate+ linabuka+ pamphumi pake ali pamaso pa ansembewo m’nyumba ya Yehova pambali pa guwa lansembe zofukiza. 20  Wansembe wamkulu Azariya ndi ansembe ena onse atamuyang’ana, anangoona kuti wachita khate pamphumi.+ Choncho anayamba kumutulutsa msangamsanga, ndipo mwiniwakeyonso anatuluka mofulumira chifukwa Yehova anali atamulanga.+ 21  Mfumu Uziya+ inakhalabe yakhate mpaka tsiku limene inamwalira. Iyo inali kungokhala m’nyumba ina chifukwa cha khatelo+ osagwiranso ntchito, popeza inali itachotsedwa m’nyumba ya Yehova. Pa nthawiyi, Yotamu mwana wake ndiye anali kuyang’anira nyumba ya mfumu ndi kuweruza anthu a m’dzikolo. 22  Nkhani zina zokhudza Uziya,+ zoyambirira ndi zomalizira, zinalembedwa ndi mneneri Yesaya+ mwana wa Amozi.+ 23  Pomalizira pake, Uziya anagona pamodzi ndi makolo ake ndipo anamuika m’manda pamodzi ndi makolo ake, koma anamuika kunja kwa manda a mafumu+ chifukwa anati: “Ndi wakhate.” Kenako Yotamu+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

Mawu a M'munsi

Gulaye ndi chipangizo choponyera miyala ndi dzanja chimene amachita kupukusa. M’madera ena amati mvuluma kapena ulaya.