2 Mbiri 25:1-28

25  Amaziya+ anali ndi zaka 25 pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 29. Mayi ake anali a ku Yerusalemu ndipo dzina lawo linali Yehoadana.+  Amaziya anapitiriza kuchita zolungama pamaso pa Yehova,+ koma osati ndi mtima wathunthu.+  Ndiyeno ufumuwo utangolimba m’manja mwake, iye anapha+ atumiki ake+ amene anapha bambo ake, omwe anali mfumu.+  Koma ana awo sanawaphe. Anachita mogwirizana ndi zimene zinalembedwa m’chilamulo cha m’buku la Mose,+ chimene Yehova analamula kuti: “Abambo asaphedwe chifukwa cha machimo a ana,+ ndipo ana asaphedwe chifukwa cha machimo a abambo.+ Aliyense aziphedwa chifukwa cha tchimo lake.”+  Kenako Amaziya anasonkhanitsa Ayuda n’kuwaimiritsa motsatira nyumba ya makolo awo.+ Anawaika m’magulu a anthu 1,000+ ndi mtsogoleri wawo, ndiponso m’magulu a anthu 100+ ndi mtsogoleri wawo, a mafuko a Yuda ndi Benjamini. Iye anawalemba mayina anthuwo, kuyambira azaka 20+ kupita m’tsogolo ndipo anapeza kuti analipo 300,000. Anali amuna ochita kusankhidwa a m’gulu la asilikali, onyamula mkondo waung’ono+ ndi chishango chachikulu.+  Kuwonjezera apo, analemba ganyu amuna amphamvu ndi olimba mtima a ku Isiraeli okwanira 100,000, pamtengo wa matalente a siliva* 100.  Ndiyeno munthu winawake wa Mulungu woona+ anapita kwa Amaziya n’kumuuza kuti: “Inu mfumu, musalole kuti gulu lankhondo la Isiraeli lipite nanu limodzi, chifukwa Yehova sali ndi Aisiraeli,+ kutanthauza ana onse a Efuraimu.  Inuyo mupite nokha ndipo limbani mtima kukamenya nkhondo.+ Mulungu woona angakuchititseni kugonja kwa adani anu, chifukwa Mulungu ali ndi mphamvu zomuthandiza+ munthu kapena zom’chititsa kugonja.”+  Pamenepo Amaziya+ anafunsa munthu wa Mulungu woonayo kuti: “Nanga bwanji za matalente 100 amene ndapereka kwa asilikali a ku Isiraeli aja?”+ Munthu wa Mulungu woonayo anayankha kuti: “Yehova akhoza kukupatsani zambiri kuposa pamenepa.”+ 10  Chotero Amaziya anapatula asilikali amene anabwera kwa iye kuchokera ku Efuraimu n’kuwauza kuti abwerere kwawo. Koma asilikaliwo anawakwiyira kwambiri Ayuda moti anabwerera kwawo ali okwiya kwambiri.+ 11  Ndiyeno Amaziya analimba mtima n’kutsogolera anthu ake kupita kuchigwa cha Mchere.+ Kumeneko anapha ana a Seiri+ okwana 10,000.+ 12  Panalinso anthu 10,000 amene ana a Yuda anawagwira amoyo. Choncho anapita nawo pathanthwe lomwe linali pamwamba kwambiri n’kuyamba kuwaponya kuchokera pathanthwepo ndipo onsewo anaphulikaphulika.+ 13  Asilikali amene Amaziya anawabweza kuti asapite naye limodzi kunkhondo aja,+ anayamba kuukira mizinda ya Yuda kuyambira ku Samariya+ mpaka ku Beti-horoni,+ ndipo anapha anthu 3,000 a m’mizindayo ndi kufunkha zinthu zambiri. 14  Koma pobwerera kuchokera kokapha Aedomu, Amaziya anatenga milungu+ ya ana a Seiri n’kukaiimika kuti ikhale milungu yake.+ Kenako anayamba kuigwadira+ ndi kuifukizira nsembe yautsi.+ 15  Choncho mkwiyo wa Yehova unayakira Amaziya ndipo anatumiza mneneri kukam’funsa kuti: “N’chifukwa chiyani mwafunafuna+ milungu+ yomwe sinapulumutse anthu awo m’manja mwanu?”+ 16  Mneneriyo atangonena zimenezi, mfumuyo inamufunsa kuti: “Kodi tinakuika kuti ukhale mlangizi wa mfumu?+ Siya kunena zimenezi.+ Kodi ukufuna kuti akuphe?” Choncho mneneriyo anasiya, koma anati: “Ndithu ndikudziwa kuti Mulungu watsimikiza kuti akuwonongeni+ chifukwa cha zimene mwachitazi,+ ndiponso chifukwa simunamvere malangizo anga.”+ 17  Tsopano Amaziya mfumu ya Yuda anakambirana ndi anthu ena n’kutumiza uthenga kwa Yehoasi, mwana wa Yehoahazi mwana wa Yehu, mfumu ya Isiraeli,+ wakuti: “Bwera tidzamenyane.”+ 18  Yehoasi mfumu ya Isiraeli atamva anamuyankha Amaziya mfumu ya Yuda kuti:+ “Chitsamba chaminga cha ku Lebanoni chinatumiza uthenga kwa mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni,+ wakuti, ‘Ndipatse mwana wako wamkazi kuti mwana wanga wamwamuna amukwatire.’+ Koma nyama yakuthengo+ ya ku Lebanoni inadutsa pamenepo n’kupondaponda chitsamba chaminga chija. 19  Ukunena kuti wagonjetsa Edomu,+ choncho mtima wako+ wayamba kudzikuza ndi kudzitamandira.+ Khala m’nyumba mwako momwemo.+ N’chifukwa chiyani ukufuna kumenya nkhondo pamene uli wofooka?+ Iweyo ndi Ayuda amene uli nawowo mugonja.”+ 20  Koma Amaziya sanamvere, popeza Mulungu woona+ ndi amene anachititsa zimenezi kuti awapereke m’manja mwa adani, chifukwa iwo anafunafuna milungu ya Edomu.+ 21  Chotero Yehoasi, mfumu ya Isiraeli, anabwera+ ndipo iye ndi Amaziya mfumu ya Yuda anamenyana+ ku Beti-semesi+ m’dziko la Yuda. 22  Pa nkhondoyo, Ayuda anagonja pamaso pa Aisiraeli+ moti aliyense anathawira kuhema wake.+ 23  Yehoasi mfumu ya Isiraeli anagwira+ Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yehoasi, mwana wa Yehoahazi ku Beti-semesiko. Kenako Yehoasi anatenga Amaziya n’kupita naye ku Yerusalemu,+ ndipo anakagumula mpanda wa Yerusalemu kuyambira pa Chipata cha Efuraimu+ mpaka kukafika pa Chipata cha Pakona.+ Anagumula mpata waukulu mikono 400. 24  Yehoasi anatenga golide ndi siliva yense, ndi ziwiya zonse zimene anazipeza m’nyumba ya Mulungu woona, ndipo anatenganso Obedi-edomu+ ndi chuma cha m’nyumba ya mfumu.+ Anagwiranso anthu ena n’kubwerera ku Samariya.+ 25  Amaziya+ mfumu ya Yuda mwana wa Yehoasi, anakhalabe ndi moyo zaka 15 pambuyo pa imfa ya Yehoasi+ mwana wa Yehoahazi mfumu ya Isiraeli.+ 26  Nkhani zina zokhudza Amaziya, zoyambirira ndi zomalizira,+ zinalembedwa m’Buku+ la Mafumu a Yuda ndi Isiraeli.+ 27  Amaziya atasiya kutsatira Yehova, anthu anam’konzera chiwembu+ ku Yerusalemu. Patapita nthawi iye anathawira ku Lakisi.+ Koma anthuwo anatumiza anthu ena omwe anamutsatira ku Lakisiko n’kukamuphera komweko.+ 28  Atatero anamunyamula pamahatchi+ n’kukamuika m’manda pamodzi ndi makolo ake mumzinda wa Yuda.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 12.