2 Mbiri 23:1-21

23  M’chaka cha 7, Yehoyada+ analimba mtima n’kuitanitsa atsogoleri a magulu a asilikali 100,+ ndipo anachita nawo pangano. Atsogoleriwo anali Azariya mwana wa Yerohamu, Isimaeli mwana wa Yehohanani, Azariya mwana wa Obedi, Maaseya mwana wa Adaya ndi Elisafati mwana wa Zikiri.  Pambuyo pake, iwo anayendayenda m’dziko lonse la Yuda n’kusonkhanitsa Alevi+ kuchokera m’mizinda yonse ya Yuda ndi atsogoleri+ a nyumba za makolo+ a Isiraeli. Atatero anapita ku Yerusalemu.  Kenako mpingo wonsewo unachita pangano+ ndi mfumu m’nyumba+ ya Mulungu woona. Ndiyeno Yehoyada anawauza kuti: “Mwana wa mfumu+ ayenera kulamulira,+ monga momwe Yehova analonjezera ponena za ana a Davide.+  Ndiyeno muchite izi: Gawo limodzi mwa magawo atatu a ansembe+ ndi Alevi+ amene ali pakati panu omwe adzabwere pa sabata,+ lidzakhale alonda a pamakomo.+  Gawo limodzi mwa magawo atatu lidzakhale panyumba ya mfumu,+ ndipo gawo lina limodzi mwa magawo atatu a inu lidzakhale pachipata chotchedwa Maziko.+ Anthu onse adzakhale pamabwalo+ a nyumba ya Yehova.  Musadzalole kuti aliyense alowe m’nyumba ya Yehova+ kupatulapo ansembe ndi Alevi amene azidzatumikira.+ Amenewa ndi amene adzalowe chifukwa ndi gulu loyera+ ndipo anthu onse adzakwaniritsa udindo wawo kwa Yehova mwa kukhala panja.  Alevi adzazungulire mfumuyo kumbali zonse,+ aliyense atatenga zida zake m’manja, ndipo aliyense wolowa m’nyumbayo adzaphedwe. Muzidzakhala limodzi ndi mfumuyo ikamalowa ndiponso ikamatuluka.”  Alevi ndi Ayuda onse anachita mogwirizana ndi zonse zimene wansembe Yehoyada+ analamula.+ Choncho, aliyense anatenga amuna ake amene anali kulowa pa sabata, limodzi ndi amene anali kutuluka pa sabata,+ popeza wansembe Yehoyada anali asanawauze+ kuti azipita.  Kuwonjezera apo, wansembe Yehoyada anapatsa atsogoleri a magulu a asilikali 100 aja+ mikondo, zishango ndi zishango zozungulira+ zimene zinali za Mfumu Davide,+ zomwe zinali m’nyumba ya Mulungu woona.+ 10  Iye anauza anthu onse kuti aimirire,+ kuyambira kumbali yakumanja ya nyumbayo mpaka kukafika kumbali yakumanzere ya nyumbayo. Anaimiriranso pafupi ndi guwa lansembe ndiponso pafupi ndi nyumbayo. Anthuwo anazungulira mfumuyo kumbali zonse, aliyense atatenga chida chake m’manja. 11  Kenako anatulutsa mwana wa mfumu uja.+ Atatero anamuveka chisoti chachifumu+ n’kuika mpukutu wa Chilamulo cha Mulungu pamutu pake.+ Chotero anamulonga ufumu, ndipo Yehoyada ndi ana ake anamudzoza+ n’kuyamba kunena kuti: “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!”+ 12  Ataliya atamva anthu akuchita phokoso komanso akuthamanga ndi kutamanda mfumu,+ nthawi yomweyo anapita kwa anthu amene anali panyumba ya Yehova. 13  Atafika anaona mfumu itaimirira pafupi ndi chipilala chake+ pakhomo. Anaonanso akalonga+ ndi anthu oimba malipenga+ ali pafupi ndi mfumuyo, ndipo anthu onse a m’dzikolo anali kusangalala+ ndi kuimba+ malipenga. Panalinso oimba+ ndi zipangizo zoimbira ndiponso anthu otsogolera poimba nyimbo zotamanda. Nthawi yomweyo Ataliya anang’amba zovala zake n’kuyamba kunena kuti: “Mwandichitira chiwembu! Mwandichitira chiwembu!”+ 14  Koma wansembe Yehoyada anatenga atsogoleri a magulu a asilikali 100, kapena kuti asilikali osankhidwa, n’kuwauza kuti: “M’chotseni pakati pa mizere ya anthu!+ Aliyense amene angam’tsatire pambuyo pake aphedwe ndi lupanga!” Popeza wansembeyo anali atanena kuti: “Musam’phere panyumba ya Yehova.” 15  Choncho anam’gwira n’kutuluka naye. Atangofika pakhomo la kunyumba ya mfumu lolowera mahatchi, anam’phera pomwepo.+ 16  Kenako Yehoyada anachita pangano pakati pa iyeyo, anthu onse, ndi mfumu kuti anthuwo apitiriza kukhala anthu+ a Yehova. 17  Pambuyo pake, anthu onse anapita kukachisi wa Baala n’kukamugwetsa+ ndipo anagwetsanso maguwa ake ansembe.+ Mafano ake anawaphwanyaphwanya,+ ndipo Mateni+ wansembe wa Baala anamupha+ patsogolo pa maguwa ansembewo. 18  Kuwonjezera apo, Yehoyada anapereka ntchito za panyumba ya Yehova kwa ansembe ndi Alevi amene Davide+ anawaika m’magulu panyumba ya Yehova, kuti azipereka nsembe zopsereza za Yehova mogwirizana ndi zimene zinalembedwa m’chilamulo cha Mose.+ Anawauza kuti azizipereka mosangalala poimba nyimbo motsatira ndondomeko imene Davide anakhazikitsa. 19  Choncho anaika alonda a pazipata+ pafupi ndi zipata+ za nyumba ya Yehova kuti aliyense wodetsedwa mwa njira ina iliyonse asalowe. 20  Atatero anatenga atsogoleri a magulu a asilikali 100,+ anthu olemekezeka, atsogoleri a anthuwo, ndi anthu onse a m’dzikolo, n’kutsetsereka nayo mfumuyo kuchokera kunyumba ya Yehova.+ Anthuwo anadzera pachipata chakumtunda n’kukafika kunyumba ya mfumu. Kenako mfumuyo anaikhazika pampando wachifumu+ wa ufumuwo. 21  Anthu onse a m’dzikolo anapitiriza kusangalala,+ ndipo mumzindawo munali bata. Ataliya anali atamupha ndi lupanga.+

Mawu a M'munsi