2 Mbiri 22:1-12

22  Kenako anthu okhala mu Yerusalemu analonga ufumu Ahaziya*+ mwana wake wamng’ono kwambiri, kukhala mfumu m’malo mwake (chifukwa gulu la achifwamba limene linabwera ndi Aluya+ kumsasa linapha ana ake onse akuluakulu).+ Tsopano Ahaziya mwana wa Yehoramu anayamba kulamulira monga mfumu ya Yuda.  Iye anayamba kulamulira+ ali ndi zaka 22 ndipo analamulira ku Yerusalemu chaka chimodzi. Amayi ake dzina lawo linali Ataliya+ mdzukulu wa Omuri.+  Ahaziya nayenso anayenda m’njira za anthu a m’nyumba ya Ahabu+ chifukwa amayi ake+ ndi amene anali kumulangiza kuti azichita zoipa.  Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova monga anachitira a m’nyumba ya Ahabu, chifukwa iwowo anakhala alangizi+ ake pambuyo pa imfa ya bambo ake, ndipo anam’pweteketsa.  Anatsatira malangizo+ awo ndipo anapita kunkhondo ndi Yehoramu+ mwana wa Ahabu mfumu ya Isiraeli, kukamenyana ndi Hazaeli+ mfumu ya Siriya ku Ramoti-giliyadi.+ Kumeneko oponya mivi analasa Yehoramu.+  Choncho Yehoramu anabwerera n’kupita ku Yezereeli+ kuti akachire zilonda zimene anam’vulaza ku Rama,+ pamene anali kumenyana ndi Hazaeli mfumu ya Siriya. Chotero Azariya*+ mwana wa Yehoramu+ mfumu ya Yuda anapita ku Yezereeli kukaona Yehoramu+ mwana wa Ahabu chifukwa anali kudwala.+  Koma Mulungu ndi amene anachititsa+ kuti Ahaziya awonongeke+ mwa kupita kwa Yehoramu. Atafika kumeneko, anatengana+ ndi Yehoramu n’kupita kukakumana ndi Yehu+ mdzukulu wa Nimusi,+ yemwe Yehova anam’dzoza+ kuti aphe a m’nyumba ya Ahabu.+  Yehu atangoyamba kulimbana ndi a m’nyumba ya Ahabu,+ anapeza akalonga a Yuda ndi ana a abale ake a Ahaziya,+ omwe anali atumiki a Ahaziya, ndipo anawapha.+  Kenako iye anayamba kufunafuna Ahaziya ndipo anthu anam’gwira+ akubisala ku Samariya+ n’kupita naye kwa Yehu. Atatero iwo anamupha n’kumuika m’manda+ popeza anati: “Iye ndi mdzukulu wa Yehosafati,+ yemwe anafunafuna Yehova ndi mtima wake wonse.”+ Tsopano panalibe aliyense wa m’nyumba ya Ahaziya amene akanatha kulamulira ufumuwo. 10  Kenako Ataliya,+ mayi wa Ahaziya ataona kuti mwana wake wafa, anapha ana onse achifumu a nyumba ya Yuda.+ 11  Koma Yehosabati+ mwana wamkazi wa mfumu, anaba Yehoasi+ mwana wamwamuna wa Ahaziya, pakati pa ana aamuna a mfumu amene anayenera kuphedwa. Anatenga Yehoasi pamodzi ndi mlezi wake n’kukamubisa m’chipinda chamkati chogona. Yehosabati, mwana wamkazi wa Mfumu Yehoramu,+ mkazi wa wansembe Yehoyada,+ (popeza iye anali mlongo wake wa Ahaziya,) anabisa mwanayo chifukwa choopa Ataliya, ndipo mwanayo sanaphedwe.+ 12  Anapitiriza kubisidwa m’nyumba ya Mulungu woona zaka 6,+ pamene Ataliya+ anali mfumukazi ya dzikolo.+

Mawu a M'munsi

Ahaziya ameneyu ndi “Yehoahazi” pa 2Mb 21:17.
Ameneyu akutchedwa “Ahaziya” pa vesi 1, 2, 7-11.