2 Mbiri 21:1-20

21  Pomalizira pake, Yehosafati anagona pamodzi ndi makolo ake+ ndipo anaikidwa m’manda pamodzi ndi makolo ake+ mu Mzinda wa Davide. Kenako Yehoramu+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.  Yehoramu anali ndi abale ake, ana a Yehosafati. Abale akewo anali Azariya, Yehiela, Zekariya, Azariya, Mikayeli ndi Sefatiya. Onsewa anali ana a Yehosafati mfumu ya Isiraeli.  Bambo awo anawapatsa mphatso zambiri+ zasiliva, zagolide, zinthu zina zabwinozabwino, ndi mizinda ya ku Yuda+ yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri. Koma ufumu anaupereka kwa Yehoramu+ chifukwa ndiye anali woyamba kubadwa.+  Yehoramu atayamba kulamulira mu ufumu wa bambo ake, iye analimbitsa ufumu wake. Chotero anapha abale ake+ onse ndi lupanga ndiponso akalonga ena a Isiraeli.  Yehoramu anayamba kulamulira ali ndi zaka 32, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 8.+  Iye anayenda m’njira ya mafumu a Isiraeli+ monga mmene ankachitira a m’nyumba ya Ahabu, chifukwa anakwatira mwana wa Ahabu.+ Ndipo iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+  Koma Yehova sanafune kuwononga nyumba ya Davide+ chifukwa cha pangano+ limene anapangana ndi Davide, monga momwe anamuuzira kuti adzam’patsa+ nyale nthawi zonse, iyeyo ndi ana ake.+  M’masiku a Yehoramu, Aedomu+ anagalukira Yuda.+ Iwo anachoka m’manja mwa Yuda n’kusankha mfumu yoti iziwalamulira.+  Choncho Yehoramu ndi akuluakulu a asilikali ake anapita kumeneko pamodzi ndi magaleta ake onse. Kumeneko, iye ananyamuka usiku n’kukapha Aedomu amene anamuzungulira. Anaphanso akuluakulu oyang’anira asilikali okwera magaleta. 10  Koma Aedomu anapitirizabe kugalukira Yuda mpaka lero. Inalinso nthawi imeneyi pamene Libina+ anagalukira Yuda ndi kuchoka m’manja mwa Yehoramu chifukwa iye anali atasiya Yehova Mulungu wa makolo ake.+ 11  Komanso iye anamanga malo okwezeka+ m’mapiri a ku Yuda kuti achititse anthu okhala mu Yerusalemu kuchita zoipa,+ ndiponso kuti asocheretse Yuda.+ 12  Kenako anam’bweretsera kalata+ yochokera kwa mneneri Eliya.+ Kalatayo inati: “Yehova Mulungu wa Davide kholo lanu wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti sunayende m’njira za Yehosafati+ bambo ako, kapena m’njira za Asa+ mfumu ya Yuda, 13  koma wayenda m’njira ya mafumu a Isiraeli+ n’kuchititsa Yuda ndi anthu okhala mu Yerusalemu kuchita zoipa,+ monga mmene a m’nyumba ya Ahabu anachititsira ena kuchita zoipa,+ ndiponso wapha ngakhale abale ako a m’nyumba ya bambo ako amene anali abwino kuposa iwe,+ 14  tamvera tsopano! Yehova adzalanga mwamphamvu+ anthu ako,+ ana ako+ ndi akazi ako, ndipo adzawononga katundu wako yense. 15  Iweyo udzakhala wodwaladwala+ popeza udzadwala matenda a m’matumbo, mpaka matumbo ako adzatuluka chifukwa chodwala tsiku ndi tsiku.’”+ 16  Chotero Yehova anachititsa Afilisiti+ ndi Aluya+ amene anali pafupi ndi Aitiyopiya+ kuukira Yehoramu.+ 17  Choncho iwo anabwera kudzalimbana nawo mpaka analowa mu Yuda. Anthuwo anatenga katundu yense amene anali m’nyumba ya mfumu,+ ana ake ndi akazi ake.+ Sanamusiyire mwana aliyense kupatulapo Yehoahazi+ mwana wake wamng’ono kwambiri. 18  Pambuyo pa zonsezi, Yehova anamudwalitsa matenda a m’matumbo osachiritsika.+ 19  Patatha zaka ziwiri zathunthu iye akudwala, matumbo ake+ anatuluka ndipo anamwalira ndi matenda oipawa. Anthu ake sanamupserezere zofukiza pa maliro ake ngati mmene anachitira+ pa maliro a makolo ake. 20  Yehoramu anali ndi zaka 32 pamene anayamba kulamulira ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 8. Pomalizira pake iye anapita popanda womumvera chisoni.+ Choncho anamuika m’manda mu Mzinda wa Davide,+ koma osati m’manda a mafumu.+

Mawu a M'munsi