2 Mbiri 20:1-37

20  Pambuyo pake ana a Mowabu,+ ana a Amoni,+ pamodzi ndi Aamonimu+ ena, anabwera kudzamenyana ndi Yehosafati.+  Choncho anthu anapita kukamuuza Yehosafati kuti: “Kwabwera khamu lalikulu la anthu ochokera kuchigawo cha kunyanja,* ku Edomu,+ kudzamenyana nanu. Panopa iwo ali ku Hazazoni-tamara, kapena kuti ku Eni-gedi.”+  Yehosafati atamva zimenezi anachita mantha+ ndipo anatsimikiza mumtima mwake kuti afunefune Yehova.+ Choncho analengeza kuti Ayuda onse asale kudya.+  Ndiyeno Ayudawo anasonkhana pamodzi kuti afunsire kwa Yehova.+ Iwo anachokera m’mizinda yonse ya Yuda n’kubwera kudzafunsira kwa Yehova.+  Kenako Yehosafati anaimirira pakati pa mpingo wa anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu, m’nyumba ya Yehova+ patsogolo pa bwalo latsopano,+  n’kunena kuti:+ “Inu Yehova Mulungu wa makolo athu,+ kodi si inu Mulungu wakumwamba?+ Kodi inu simukulamulira maufumu onse a mitundu ya anthu?+ Kodi m’dzanja lanu si muli mphamvu kotero kuti palibe amene angalimbane nanu?+  Kodi inuyo Mulungu wathu+ si paja munathamangitsa anthu amene anali kukhala m’dziko lino pamaso pa anthu anu Aisiraeli,+ n’kulipereka+ kwa mbewu ya Abulahamu yemwe anali kukukondani,+ kuti likhale lawo mpaka kalekale?  Ndiyeno iwo anayamba kukhalamo ndipo anakumangirani malo opatulika a dzina lanu m’dzikolo,+ n’kunena kuti,  ‘Likatigwera tsoka,+ lupanga, chiweruzo chowawa, mliri+ kapena njala,+ tiziima pamaso pa nyumba iyi+ ndi pamaso panu (popeza dzina lanu+ lili m’nyumba iyi), kuti tifuulire inu kuti mutithandize m’masautso athu, ndipo inu muzimva ndi kutipulumutsa.’+ 10  Tsopano taonani zimene akuchita ana a Amoni,+ ana a Mowabu+ ndi a kudera lamapiri la Seiri.+ Inu simunalole kuti Aisiraeli alowe m’dziko lawo pamene anali kutuluka m’dziko la Iguputo ndipo anawasiya osawawononga.+ 11  Tsopano akutilipira+ mwa kubwera kudzatithamangitsa m’cholowa chanu chimene munatipatsa.+ 12  Inu Mulungu wathu kodi simuwaweruza?+ Ifeyo patokha tilibe mphamvu zotha kulimbana ndi khamu lalikulu limene likubwera kudzamenyana nafeli+ ndipo sitikudziwa chochita,+ koma maso athu ali pa inu.”+ 13  Nthawi yonseyi anthu onse a ku Yuda anali ataimirira pamaso pa Yehova,+ kuphatikizapo akazi awo ndi ana awo, ngakhalenso ana awo ang’onoang’ono.+ 14  Tsopano mzimu+ wa Yehova unafikira Yahazieli yemwe anali pakati pa mpingowo. Iye anali mwana wa Zekariya, Zekariya anali mwana wa Benaya, Benaya anali mwana wa Yeyeli, Yeyeli anali mwana wa Mataniya, Mataniya anali Mlevi, mmodzi wa ana a Asafu.+ 15  Choncho Yahazieli anati: “Tamverani Ayuda nonsenu, anthu okhala mu Yerusalemu, ndi inu Mfumu Yehosafati! Izi n’zimene Yehova wanena kwa inu, ‘Musaope+ kapena kuchita mantha ndi khamu lalikululi, popeza nkhondoyi si yanu ndi ya Mulungu.+ 16  Mawa mupite kukakumana nawo. Iwo akubwera ndipo adzera pampata wa Zizi. Mukawapeza kumapeto kwa chigwa chimene chili kutsogolo kwa chipululu cha Yerueli. 17  Ulendo uno simufunikira kumenya nkhondo.+ Khalani m’malo anu, imani chilili+ ndi kuona Yehova akukupulumutsani.+ Inu Ayuda ndi anthu a ku Yerusalemu, musaope kapena kuchita mantha.+ Mawa mupite kukakumana nawo ndipo Yehova akhala nanu.’”+ 18  Nthawi yomweyo Yehosafati anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi,+ ndipo Ayuda onse ndi anthu okhala mu Yerusalemu anawerama pamaso pa Yehova kuti alambire Yehovayo.+ 19  Kenako Alevi+ omwe anali ana a Kohati+ ndi ana a Kora+ anaimirira ndi kutamanda Yehova Mulungu wa Isiraeli ndi mawu okweza kwambiri.+ 20  Anthuwo ananyamuka m’mawa kwambiri n’kupita kuchipululu+ cha Tekowa.+ Ali m’njira, Yehosafati anaimirira n’kunena kuti: “Tamverani inu Ayuda ndi anthu okhala mu Yerusalemu!+ Khulupirirani+ Yehova Mulungu wanu kuti mukhalitse. Khulupirirani aneneri+ ake kuti zinthu zikuyendereni bwino.” 21  Kenako iye anakambirana+ ndi anthuwo, n’kutenga anthu oimbira+ Yehova ndi omutamanda+ ovala zovala zokongola ndi zopatulika+ n’kuwaika patsogolo pa amuna onyamula zida.+ Iwo anali kunena kuti: “Tamandani Yehova,+ pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhala mpaka kalekale.”+ 22  Pa nthawi imene iwo ananyamuka akufuula mosangalala ndi kutamanda Mulungu, Yehova anaika amuna omwe anabisalira+ ana a Amoni, ana a Mowabu ndi a kudera lamapiri la Seiri omwe anali kupita ku Yuda, ndipo iwo anaphana okhaokha.+ 23  Ana a Amoni ndi ana a Mowabu anaukira anthu okhala kudera lamapiri la Seiri+ ndipo anawapha ndi kuwamaliza. Atatha kupha anthu a ku Seiri, iwo anaphana okhaokha.+ 24  Kenako Ayuda anafika pansanja ya mlonda ya m’chipululu.+ Iwo atatembenuka kuti ayang’ane khamu lija, anangoona mitembo yokhayokha ili pansi+ popanda wopulumuka. 25  Choncho Yehosafati ndi anthu ake anapita kukafunkha+ zinthu zimene adaniwo anali nazo. Iwo anapeza zinthu zochuluka pakati pa anthuwo monga katundu wosiyanasiyana, zovala ndi zinthu zina zabwinozabwino. Chotero anayamba kutenga zinthuzo mpaka zinawakanika kunyamula.+ Kwa masiku atatu anakhala akututa zofunkhazo chifukwa zinalipo zambiri. 26  Pa tsiku lachinayi anasonkhana pachigwa cha Beraka ndipo kumeneko anatamanda Yehova.+ N’chifukwa chake malowo anawatcha dzina+ lakuti chigwa cha Beraka* mpaka lero. 27  Kenako Ayuda ndi anthu onse a ku Yerusalemu anabwerera ku Yerusalemu, Yehosafati ali patsogolo pawo. Iwo anali akusangalala chifukwa Yehova anawathandiza kugonjetsa adani awo.+ 28  Choncho anafika ku Yerusalemu kunyumba ya Yehova+ akuimba ndi zoimbira za zingwe,+ azeze+ ndi malipenga.+ 29  Mantha+ ochokera kwa Mulungu anagwira mafumu onse a m’dzikolo atamva kuti Yehova wagonjetsa adani a Isiraeli.+ 30  Chotero ufumu wa Yehosafati unalibe chosokoneza chilichonse, ndipo Mulungu wake anapitiriza kumupatsa mpumulo pakati pa adani ake onse omuzungulira.+ 31  Yehosafati+ anapitiriza kulamulira ku Yuda. Iye anali ndi zaka 35 pamene anayamba kulamulira ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 25. Mayi ake dzina lawo linali Azuba+ mwana wa Sili. 32  Yehosafati anapitiriza kuyenda m’njira za Asa+ bambo ake. Sanapatuke panjirazo, ndipo anachita zoyenera pamaso pa Yehova.+ 33  Koma sanachotse malo okwezeka+ ndiponso anthuwo anali asanakonze mitima yawo kuti atsatire Mulungu wa makolo awo.+ 34  Nkhani zina zokhudza Yehosafati, zoyambirira ndi zomalizira, zinalembedwa m’mawu a Yehu+ mwana wa Haneni.+ Mawuwa analembedwa m’Buku+ la Mafumu a Isiraeli. 35  Pambuyo pa zimenezi, Yehosafati mfumu ya Yuda anachita mgwirizano ndi Ahaziya+ mfumu ya Isiraeli amene anachita zoipa.+ 36  Chotero anayamba kugwira naye limodzi ntchito yopanga zombo zopita ku Tarisi.+ Zombozo anazipangira ku Ezioni-geberi.+ 37  Koma Eliezere mwana wa Dodavahu wa ku Maresa analankhula mwaulosi motsutsana ndi Yehosafati, kuti: “Popeza mwachita mgwirizano ndi Ahaziya,+ Yehova awononga ntchito zanu.”+ Chotero zombozo zinasweka+ ndipo sizinathenso kupita ku Tarisi.+

Mawu a M'munsi

Kutanthauza Nyanja Yofiira.
Dzinali limatanthauza, “Dalitso.”