2 Mbiri 17:1-19

17  Ndiyeno Yehosafati+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake, ndipo analimbitsa ufumu wake mu Isiraeli.  Iye anaika magulu ankhondo m’mizinda yonse ya Yuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri. Anamanganso midzi ya asilikali m’dziko la Yuda ndi m’mizinda ya Efuraimu imene Asa bambo ake analanda.+  Yehova anapitiriza kukhala ndi Yehosafati+ chifukwa anayenda m’njira zimene Davide kholo lake+ anayenda kalekale, ndipo sanafunefune Abaala.+  Iye anafunafuna Mulungu wa bambo ake+ ndipo anayenda+ motsatira chilamulo chake, sanatsatire zochita za Aisiraeli.+  Yehova anachititsa kuti ufumuwo ukhazikike m’manja mwake+ ndipo Ayuda onse anapitiriza kupereka+ mphatso kwa Yehosafati. Chotero iye anakhala ndi chuma chambiri ndi ulemerero wochuluka.+  Komanso analimba mtima potsatira njira+ za Yehova ndipo anachotsa m’dziko la Yuda malo okwezeka+ ndi mizati yopatulika.+  M’chaka chachitatu cha ulamuliro wake, anaitana akalonga ake kuti aziphunzitsa m’mizinda ya Yuda. Akalongawo anali Beni-hayili, Obadiya, Zekariya, Netaneli ndi Mikaya,  pamodzi ndi Alevi. Aleviwo anali Semaya, Netaniya, Zebadiya, Asaheli, Semiramoti, Yehonatani, Adoniya, Tobiya ndi Tobi-adoniya, pamodzi ndi ansembe Elisama ndi Yehoramu.+  Iwo anayamba kuphunzitsa+ mu Yuda pogwiritsira ntchito buku la chilamulo cha Yehova.+ Ankayendayenda m’mizinda yonse ya Yuda n’kumaphunzitsa anthu. 10  Mantha+ ochokera kwa Yehova anagwira maufumu onse a m’mayiko ozungulira Yuda, ndipo sanachite nkhondo ndi Yehosafati.+ 11  Afilisiti anali kubweretsa+ mphatso ndi ndalama kwa Yehosafati monga msonkho.+ Aluya+ nawonso anali kum’bweretsera ziweto. Ankabweretsa nkhosa zamphongo 7,700 ndi mbuzi zamphongo 7,700.+ 12  Zinthu zinapitiriza kumuyendera bwino Yehosafati ndipo mphamvu zake zinapitiriza kukula kwambiri.+ Iye anayamba kumanga m’dziko la Yuda malo okhala ndi mipanda yolimba kwambiri,+ ndiponso mizinda yosungirako zinthu.+ 13  Panali zinthu zambiri m’mizinda ya Yuda zimene zinakhala zake. Ku Yerusalemu anali ndi asilikali,+ amuna amphamvu+ ndi olimba mtima. 14  Awa ndiwo anali maudindo awo potsata nyumba ya makolo awo: Adinala anali mmodzi wa atsogoleri a magulu a asilikali 1,000 a fuko la Yuda. Iye anali ndi amuna amphamvu ndi olimba mtima okwana 300,000.+ 15  Adinalayo ankayang’anira Yehohanani mkulu wa asilikali, yemwe anali ndi asilikali 280,000. 16  Iye ankayang’aniranso Amasiya mwana wa Zikiri, yemwe anadzipereka kutumikira+ Yehova. Amasiyayo anali ndi amuna amphamvu ndi olimba mtima okwana 200,000. 17  Kuchokera m’fuko la Benjamini+ panali Eliyada, mwamuna wamphamvu ndi wolimba mtima yemwe anali ndi asilikali 200,000 onyamula mauta ndi zishango.+ 18  Iye ankayang’anira Yehozabadi yemwe anali ndi asilikali 180,000 okonzekera kumenya nkhondo. 19  Amenewa ndiwo anali kutumikira mfumu, kuwonjezera pa anthu amene mfumuyo inawaika m’mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri+ m’dziko lonse la Yuda.

Mawu a M'munsi