2 Mbiri 16:1-14

16  M’chaka cha 36 cha ulamuliro wa Asa, Basa+ mfumu ya Isiraeli anapita kukaukira Yuda. Kenako anayamba kumanga mpanda wolimba kwambiri kuzungulira mzinda wa Rama,+ kuti anthu asamapite kwa Asa mfumu ya Yuda kapena kubwera kuchokera kwa Asa.+  Tsopano Asa anatenga siliva ndi golide pa chuma cha m’nyumba ya Yehova+ ndiponso cha m’nyumba ya mfumu,+ n’kuzitumiza kwa Beni-hadadi+ mfumu ya Siriya+ amene anali kukhala ku Damasiko.+ Anam’tumiziranso mawu akuti:  “Pali pangano pakati pa ine ndi iwe, ndi pakati pa bambo anga ndi bambo ako. Taona, ndakutumizira siliva ndi golide. Pita ukaphwanye pangano lako ndi Basa+ mfumu ya Isiraeli kuti achoke kwa ine.”+  Choncho Beni-hadadi anamvera Mfumu Asa ndipo anatumiza akuluakulu a gulu lake lankhondo kuti akamenyane ndi mizinda ya Isiraeli. Iwo anawononga Iyoni,+ Dani,+ Abele-maimu,+ ndi malo onse osungiramo zinthu+ a m’mizinda ya Nafitali.+  Basa atangomva zimenezi, nthawi yomweyo anasiya kumanga Rama n’kuimitsa ntchito yake.+  Ndiyeno mfumu Asa inatenga Ayuda onse,+ ndipo iwo anapita kukatenga miyala ya ku Rama+ ndi matabwa ake, zimene Basa ankamangira.+ Mfumuyo inatenga zinthu zimenezo n’kuyamba kukamangira Geba+ ndi Mizipa.+  Pa nthawi imeneyo, wamasomphenya* Haneni+ anapita kwa Asa mfumu ya Yuda n’kumuuza kuti: “Chifukwa chakuti munadalira mfumu ya Siriya,+ osadalira Yehova Mulungu wanu,+ gulu lankhondo la mfumu ya Siriya lathawa m’manja mwanu.  Kodi Aitiyopiya+ ndi Alibiya+ sanali gulu lankhondo lalikulu, la anthu ambiri, magaleta ambiri, ndi okwera pamahatchi ambirinso?+ Chifukwa chakuti munadalira Yehova, kodi iye sanawapereke m’manja mwanu?+  Pajatu maso a Yehova+ akuyendayenda padziko lonse lapansi+ kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo+ uli wathunthu kwa iye. Mwachita zopusa+ pankhani imeneyi, chifukwa kuyambira tsopano anthu azichita nanu nkhondo.”+ 10  Koma Asa anamukwiyira wamasomphenyayo. Kenako anamuika m’ndende n’kumumanga m’matangadza+ popeza anamupsera mtima kwambiri chifukwa cha nkhani imeneyi.+ Pa nthawi yomweyo, Asa anayamba kuponderezanso+ anthu ake ena. 11  Nkhani zokhudza Asa, zoyambirira ndi zomalizira, zinalembedwa m’Buku+ la Mafumu a Yuda ndi Isiraeli. 12  M’chaka cha 39 cha ulamuliro wa Asa, iye anadwala nthenda ya mapazi+ mpaka matendawo anakula kwambiri. Koma ngakhale pamene anali kudwala, iye anafunafuna ochiritsa+ osati Yehova.+ 13  Pomalizira pake, Asa anamwalira m’chaka cha 41 cha ulamuliro wake ndipo anagona pamodzi ndi makolo ake.+ 14  Choncho anamuika m’manda ake olemekezeka kwambiri,+ amene iye anadzikumbira mu Mzinda wa Davide.+ Pomuika m’mandamo, anamugoneka pabedi pomwe anathirapo mafuta a basamu ambiri+ ndi msakanizo wapadera wa mafuta onunkhira.+ Kuwonjezera apo, pamaliro ake anapserezapo zofukiza+ zochuluka kwambiri.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa 1Mb 29:29