2 Mbiri 15:1-19

15  Tsopano mzimu+ wa Mulungu unafikira Azariya mwana wa Odedi.+  Chotero iye anapita kukaonekera kwa Asa n’kumuuza kuti: “Tamverani mfumu Asa ndi anthu onse a fuko la Yuda ndi Benjamini. Yehova akhala nanu inuyo mukapitiriza kukhala naye.+ Mukamufunafuna+ iye adzalola kuti mum’peze, koma mukamusiya nayenso adzakusiyani.+  Masiku ambiri Aisiraeli+ anakhala opanda Mulungu woona, opanda wansembe woti aziwaphunzitsa+ ndiponso opanda Chilamulo.  Koma iwo atabwerera kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli+ m’mavuto awowo+ n’kumufunafuna, iye analola kuti amupeze.+  M’masiku amenewo, anthu sankayenda mwamtendere+ chifukwa panali zisokonezo zambiri pakati pa anthu onse okhala m’madera a m’dzikoli.+  Anthuwo anagonjetsana chifukwa anaukirana okhaokha. Fuko limodzi linkamenyana ndi fuko lina+ ndiponso mzinda ndi mzinda wina, popeza Mulungu anawasiya pa chisokonezo ndi zowawa zosiyanasiyana.+  Koma inuyo khalani olimba mtima+ ndipo musagwe ulesi,+ pakuti mudzapeza mphoto chifukwa cha ntchito yanu.”+  Asa atangomva mawu amenewa ndi ulosi wa mneneri Odedi,+ analimba mtima n’kuyamba kuchotsa zinthu zonyansa+ m’dziko lonse la Yuda ndi Benjamini ndi m’mizinda imene analanda m’dera lamapiri la Efuraimu.+ Anayambanso kukonza guwa lansembe la Yehova limene linali patsogolo pa khonde la nyumba ya Yehova.+  Atatero anayamba kusonkhanitsa pamodzi Ayuda ndi Abenjamini+ onse, ndi alendo ambirimbiri+ amene anali pakati pawo ochokera ku fuko la Efuraimu, Manase ndi Simiyoni. Alendowa anathawa ku Isiraeli n’kubwera kwa iye ataona kuti Yehova Mulungu wake ali naye.+ 10  Iwo anasonkhana ku Yerusalemu m’mwezi wachitatu wa chaka cha 15 cha ulamuliro wa Asa. 11  Kenako anapereka nsembe kwa Yehova pa tsiku limenelo kuchokera pa zofunkha zimene anabweretsa. Anapereka nsembe ng’ombe 700 ndi nkhosa 7,000. 12  Kuwonjezera apo, anachita pangano+ loti adzafunafuna Yehova Mulungu wa makolo awo ndi mtima wawo wonse ndi moyo wawo wonse.+ 13  Komanso kuti aliyense wosafunafuna Yehova Mulungu wa Isiraeli ayenera kuphedwa,+ kaya ndi wamng’ono kapena wamkulu,+ kaya ndi mwamuna kapena mkazi.+ 14  Choncho analumbira+ kwa Yehova ndi mawu okweza ndi kufuula mwachimwemwe, ndi kuliza malipenga ndi nyanga. 15  Ayuda onse anayamba kusangalala+ chifukwa cha zimene analumbirazo popeza analumbira ndi mtima wawo wonse, komanso chifukwa chakuti anafunafuna Mulungu mokondwa kwambiri moti iye analola kuti amupeze.+ Choncho Yehova anapitiriza kuwapatsa mpumulo pakati pa adani awo onse owazungulira.+ 16  Mfumu Asa+ inachotsa ngakhalenso agogo ake aakazi a Maaka+ pa udindo wawo wokhala mayi wa mfumu,+ chifukwa anapanga fano lonyansa kwambiri+ lopembedzera mzati wopatulika.+ Kenako Asa anagwetsa fanolo ndipo analiperapera n’kukalitentha+ m’chigwa cha Kidironi.+ 17  Koma malo okwezeka+ analipobe mu Isiraeli.+ Ngakhale zinali choncho, mtima wa Asa unali wathunthu masiku ake onse.+ 18  Iye anabweretsa kunyumba ya Mulungu woona zinthu zimene bambo ake anaziyeretsa,+ komanso zinthu zimene iyeyo anaziyeretsa. Zinthuzo zinali siliva, golide, ndi ziwiya zina.+ 19  Pa nthawiyo sipanachitike nkhondo mpaka chaka cha 35 cha ulamuliro wa Asa.+

Mawu a M'munsi