2 Mbiri 12:1-16

12  Ufumu wa Rehobowamu utangokhazikika+ ndiponso iye atangokhala wamphamvu, iye ndi Aisiraeli onse+ anasiya chilamulo cha Yehova.+  M’chaka chachisanu cha Mfumu Rehobowamu,+ Sisaki+ mfumu ya Iguputo anabwera kudzaukira Yerusalemu (chifukwa iwo anachita zosakhulupirika kwa Yehova).+  Anabwera ndi magaleta 1,200+ ndi amuna okwera pamahatchi 60,000. Anabweranso ndi anthu osawerengeka+ kuchokera ku Iguputo. Anthuwo anali Alibiya,+ Asuki ndi Aitiyopiya.+  Sisakiyo analanda mizinda ya Yuda+ yomwe inali ndi mipanda yolimba kwambiri, ndipo pamapeto pake anafika ku Yerusalemu.+  Tsopano mneneri Semaya+ anapita kwa Rehobowamu ndi kwa akalonga a Yuda amene anasonkhana ku Yerusalemu chifukwa cha Sisaki. Iye anawauza kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Inuyo mwandisiya,+ choncho inenso ndakusiyani+ ndipo ndakuperekani m’manja mwa Sisaki.’”  Akalonga a Isiraeliwo ndi mfumuyo atamva zimenezi, anadzichepetsa+ n’kunena kuti: “Yehova ndi wolungama.”+  Yehova ataona+ kuti anthuwo adzichepetsa, mawu a Yehova anafika kwa Semaya,+ kuti: “Anthuwa adzichepetsa,+ choncho sindiwawononga. Posachedwapa ndiwapulumutsa, ndipo sinditsanulira mkwiyo wanga pa Yerusalemu kudzera m’manja mwa Sisaki.+  Koma iwo akhala atumiki ake+ kuti adziwe kusiyana kokhala atumiki anga+ ndi kokhala atumiki a maufumu a m’dzikoli.”+  Chotero Sisaki+ mfumu ya Iguputo anaukira Yerusalemu ndi kutenga chuma cha m’nyumba ya Yehova+ ndi chuma cha m’nyumba ya mfumu.+ Anatenga chilichonse kuphatikizapo zishango zagolide zimene Solomo anapanga.+ 10  Choncho Mfumu Rehobowamu inapanga zishango zamkuwa m’malo mwake, ndipo inazipereka kwa akulu a asilikali othamanga,+ omwe anali alonda+ a pakhomo la nyumba ya mfumu, kuti aziziyang’anira.+ 11  Nthawi iliyonse imene mfumuyo ikupita kunyumba ya Yehova, asilikali othamangawo ankanyamula zishangozo, ndipo kenako ankazibwezera kuchipinda cha alonda.+ 12  Chifukwa chakuti Rehobowamu anadzichepetsa, Yehova anabweza mkwiyo wake+ ndipo sanaganizenso zoti awawononge anthu onsewo.+ Komanso mwa anthu a ku Yuda munapezeka ntchito zabwino.+ 13  Mfumu Rehobowamu inapitiriza kulimbitsa ufumu wake ndi kulamulira ku Yerusalemu. Rehobowamu+ anali ndi zaka 41 pamene anayamba kulamulira, ndipo kwa zaka 17 analamulira ku Yerusalemu, mzinda+ umene Yehova anasankha pakati pa mafuko onse a Isiraeli kuti aike dzina lake kumeneko.+ Mayi ake dzina lawo linali Naama+ Muamoni.+ 14  Koma iye anachita zoipa+ chifukwa sanatsimikize kufunafuna Yehova ndi mtima wake wonse.+ 15  Nkhani zina zokhudza Rehobowamu, zoyambirira ndi zomalizira,+ zinalembedwa m’mawu a mneneri Semaya+ ndiponso m’mawu a Ido+ wamasomphenya, motsatira mndandanda wa mayina a makolo. Nthawi zonse panali kuchitika nkhondo pakati pa Rehobowamu+ ndi Yerobowamu.+ 16  Pomalizira pake, Rehobowamu anagona pamodzi ndi makolo ake+ ndipo anaikidwa m’manda mu Mzinda wa Davide.+ Kenako Abiya+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

Mawu a M'munsi