2 Mbiri 11:1-23

11  Rehobowamu atafika ku Yerusalemu,+ nthawi yomweyo anasonkhanitsa amuna ochita kusankhidwa odziwa kumenya nkhondo okwanira 180,000+ a nyumba yonse ya Yuda ndi ya Benjamini.+ Anawasonkhanitsa kuti akamenyane ndi Isiraeli pofuna kuti ufumu ubwerere kwa Rehobowamu.  Kenako mawu a Yehova anafikira Semaya+ munthu wa Mulungu woona, kuti:  “Kauze Rehobowamu mwana wa Solomo, mfumu ya Yuda,+ ndi Aisiraeli onse ku Yuda ndi ku Benjamini, kuti,  ‘Yehova wati: “Musapite kukamenyana ndi abale anu.+ Aliyense abwerere kunyumba kwake, chifukwa zimene zachitikazi, zachitika mwa kufuna kwanga.”’”+ Choncho anamvera mawu a Yehova n’kubwerera, osakamenyana ndi Yerobowamu.+  Rehobowamu anapitiriza kukhala ku Yerusalemu, ndipo anamanga mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri m’dziko la Yuda.  Anamanganso mizinda ya Betelehemu,+ Etami,+ Tekowa,+  Beti-zuri,+ Soko,+ Adulamu,+  Gati,+ Maresha,+ Zifi,+  Adoraimu, Lakisi,+ Azeka,+ 10  Zora,+ Aijaloni+ ndi Heburoni.+ Imeneyi inali mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri imene inali ku Yuda ndi ku Benjamini. 11  Kuwonjezera apo, analimbitsanso malo okhala ndi mipanda yolimba kwambiri+ n’kuikamo atsogoleri.+ Atatero m’mizindamo anaikamo chakudya, mafuta ndi vinyo. 12  M’mizinda yonse yosiyanasiyana anaikamo zishango zazikulu+ ndi mikondo ing’onoing’ono.+ Mizindayo anailimbitsa kwambiri, ndipo iye anapitiriza kulamulira Yuda ndi Benjamini. 13  Ansembe ndi Alevi m’madera awo onse mu Isiraeli yense, anakhala kumbali ya Rehobowamu. 14  Aleviwo anasiya malo awo odyetserako ziweto+ ndi madera awo+ n’kupita ku Yuda ndi ku Yerusalemu,+ chifukwa Yerobowamu+ ndi ana ake anachotsa+ Aleviwo pa udindo wokhala ansembe a Yehova. 15  Iye anadziikira ansembe m’malo okwezeka+ kuti azitumikira ziwanda zooneka ngati mbuzi*+ ndi mafano a ana a ng’ombe amene iye anapanga.+ 16  Koma anthu a m’mafuko onse a Isiraeli amene anali ndi mtima wofunafuna Yehova Mulungu wa Isiraeli, anatsatira ansembe ku Yerusalemu+ kukapereka nsembe+ kwa Yehova Mulungu wa makolo awo. 17  Iwo analimbitsa ufumu wa Yuda+ ndi kulimbikitsa Rehobowamu mwana wa Solomo kwa zaka zitatu, popeza anthuwo anayenda m’njira ya Davide ndi ya Solomo kwa zaka zitatu.+ 18  Rehobowamu anakwatira Mahalati mwana wamkazi wa Yerimoti mwana wa Davide. Amayi ake a Mahalati anali Abihaili mwana wamkazi wa Eliyabu+ mwana wa Jese. 19  M’kupita kwa nthawi, Mahalatiyo anaberekera Rehobowamu ana. Anawo anali Yeusi, Semariya ndi Zahamu. 20  Pambuyo pake Rehobowamu anakwatira Maaka+ mdzukulu wa Abisalomu.+ Kenako mkaziyo anam’berekera ana awa: Abiya,+ Atai, Ziza ndi Selomiti. 21  Rehobowamu anali kukonda kwambiri Maaka mdzukulu wa Abisalomu kuposa akazi ake ena onse+ ndi adzakazi* ake, pakuti iye anakwatira akazi 18, ndiponso anali ndi adzakazi 60. Iye anabereka ana aamuna 28 ndi ana aakazi 60. 22  Chotero Rehobowamu anasankha Abiya mwana wa Maaka kuti akhale mtsogoleri wa abale ake. Anatero chifukwa iye ankafuna kuti adzam’patse ufumu. 23  Komabe anachita mozindikira+ chifukwa anagawa ana akewo n’kuwaika m’madera onse a ku Yuda ndi ku Benjamini.+ Anawaika m’mizinda yonse yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri,+ ndipo anawapatsa chakudya chambiri+ ndi kuwapezera akazi ambirimbiri.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Le 17:7.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.