2 Mbiri 10:1-19

10  Tsopano Rehobowamu+ anapita ku Sekemu,+ chifukwa kumeneko n’kumene Aisiraeli onse anasonkhana kuti akamulonge ufumu.  Yerobowamu+ mwana wa Nebati atamva zimenezi ali ku Iguputo,+ (pajatu anathawa mfumu Solomo,) nthawi yomweyo anabwerera kuchokera ku Iguputoko.+  Choncho anthu anatumiza uthenga womuitana, ndipo Yerobowamu ndi Aisiraeli onse anabwera n’kuyamba kulankhula ndi Rehobowamu kuti:+  “Bambo anu anaumitsa goli lathu.+ Tsopano inuyo mufewetse ntchito yowawa ya bambo anu ndi goli lawo lolemera+ limene anatisenzetsa, ndipo tidzakutumikirani.”+  Rehobowamu atamva zimenezi anauza anthuwo kuti: “Pitani kaye kwa masiku atatu, ndipo mukabwerenso kwa ine.” Anthuwo anapitadi.  Ndiyeno Mfumu Rehobowamu inafunsira nzeru+ kwa akulu amene anali kutumikira bambo ake Solomo pamene anali moyo. Inawafunsa kuti: “Kodi mukuganiza kuti anthuwa ndiwayankhe bwanji?”+  Iwo anaiuza kuti: “Mukakhala munthu wabwino kwa anthuwa ndi kuchita zowasangalatsa, ndiponso mukawayankha ndi mawu abwino,+ iwo adzakhala atumiki anu nthawi zonse.”+  Koma iye sanamvere malangizo+ ochokera kwa akulu aja, m’malomwake anayamba kukafunsira malangizo kwa achinyamata amene anakulira naye limodzi,+ omwe anali kum’tumikira.+  Iye anawafunsa kuti: “Kodi mungapereke malangizo+ otani kuti tiwayankhe anthuwa amene andipempha kuti, ‘Fewetsani goli limene bambo anu anatisenzetsa’?”+ 10  Achinyamata amene anakulira naye limodziwo anamuuza kuti: “Izi n’zimene mukanene kwa anthu awa amene akuuzani kuti, ‘Bambo anu anatisenzetsa goli lolemera, koma inuyo mutipeputsireko.’ Muwauze kuti,+ ‘Chala changa chaching’ono chidzakhala chachikulu kuposa chiuno cha bambo anga.+ 11  Bambo anga anakusenzetsani goli lolemera koma ineyo ndiwonjezera goli lanulo.+ Bambo anga anakukwapulani ndi zikwapu koma ineyo ndikukwapulani ndi zikoti zaminga.’”+ 12  Pa tsiku lachitatu, Yerobowamu ndi anthu onse anapita kwa Rehobowamu, monga momwe mfumuyo inanenera kuti: “Mukabwerenso kwa ine pa tsiku lachitatu.”+ 13  Mfumuyo inayamba kuyankha anthuwo mwaukali.+ Chotero Mfumu Rehobowamu inasiya malangizo+ a akulu aja.+ 14  Iyo inayamba kulankhula kwa anthuwo motsatira malangizo amene achinyamata aja anaipatsa.+ Inati: “Ine ndidzakusenzetsani goli lolemera kwambiri, ndipo ndidzawonjezera goli lanulo. Bambo anga anakukwapulani ndi zikwapu, koma ine ndidzakukwapulani ndi zikoti zaminga.”+ 15  Mfumuyo sinamvere anthuwo chifukwa zinthu zinatembenuka chonchi mwa kufuna kwa Mulungu woona,+ kuti Yehova akwaniritse mawu ake+ amene analankhula kwa Yerobowamu mwana wa Nebati,+ kudzera mwa Ahiya+ Msilo.+ 16  Popeza kuti mfumuyo sinawamvere Aisiraeli onsewo, iwo anayankha mfumuyo kuti: “Tili ndi gawo lanji mwa Davide?+ Ife tilibe cholowa mwa mwana wa Jese.+ Aisiraeli inu, aliyense apite kwa milungu yake!+ Tsopano iwe Davide,+ uzisamalira nyumba yako yokha.” Aisiraeliwo atatero, onse anayamba kubwerera kumahema awo. 17  Koma Rehobowamu anapitiriza kulamulira ana a Isiraeli amene anali kukhala m’mizinda ya ku Yuda.+ 18  Kenako Mfumu Rehobowamu inatumiza Hadoramu+ amene anali kuyang’anira anthu ogwira ntchito yokakamiza, koma ana a Isiraeli anam’ponya miyala+ n’kumupha. Komabe, Mfumu Rehobowamu inakwanitsa kukwera galeta lake n’kuthawira ku Yerusalemu.+ 19  Ndipo Aisiraeli anapitiriza kuukira+ nyumba ya Davide mpaka lero.

Mawu a M'munsi