2 Mafumu 8:1-29

8  Tsopano Elisa anauza mayi amene anamuukitsira mwana uja,+ kuti: “Nyamuka, iwe ndi banja lako, ukakhale monga mlendo kulikonse kumene ungakakhale,+ chifukwa Yehova abweretsa njala.+ Njalayo idzatenga zaka 7.”+  Choncho, mayiyo ndi banja lake+ ananyamuka+ n’kupita kukakhala monga mlendo m’dziko la Afilisiti+ kwa zaka 7, mogwirizana ndi mawu a munthu wa Mulungu woona.  Zaka 7 zija zitatha, mayiyo anabwerera kuchokera kudziko la Afilisiti n’kupita kukadandaulira mfumu+ kuti imupatse nyumba yake ndi munda wake.  Pa nthawiyo, mfumu inali ikulankhula ndi Gehazi+ mtumiki wa munthu wa Mulungu woona, kuti: “Ndifotokozere zinthu zonse zazikulu zimene Elisa wachita.”+  Gehazi akufotokozera mfumuyo mmene Elisa anaukitsira munthu wakufa,+ anangomva mayi wa mwana amene anaukitsidwayo akudandaulira mfumu kuti imupatse nyumba yake ndi munda wake.+ Nthawi yomweyo Gehazi anati: “Mbuye wanga+ mfumu, mayiyo ndi uyu, ndiponso mwana wake amene Elisa anamuukitsa uja ndi uyu.”  Ndiyeno mfumuyo inapempha mayiyo kuti aifotokozere nkhani yonse,+ ndipo mayiyo anafotokozadi. Kenako mfumuyo inauza nduna ya panyumba yake+ kuti: “Mayiyu um’bwezere zinthu zake zonse, ndipo umupatse ndalama zimene akanapeza pa zokolola za kumunda kwake pa nthawi yonse imene anachokapo kufikira lero.”+  Kenako Elisa anapita ku Damasiko.+ Kumeneko Beni-hadadi+ mfumu ya Siriya inali kudwala. Choncho mfumuyo inauzidwa kuti: “Munthu wa Mulungu woona uja+ wafika kuno.”  Mfumuyo itamva zimenezi, inauza Hazaeli kuti:+ “Tenga mphatso,+ upite kukakumana ndi munthu wa Mulungu woonayo. Ukafunsire+ mawu a Yehova kudzera mwa iye kuti, ‘Kodi ndichira matenda angawa?’”  Choncho Hazaeli anatenga mphatsozo n’kupita kukakumana naye. Anatenga chinthu chilichonse chabwino cha m’Damasiko. Mphatsozo anazinyamula pangamira zokwana 40. Atafika, anaima pamaso pa Elisa n’kunena kuti: “Mwana wanu+ Beni-hadadi mfumu ya Siriya wandituma kudzakufunsani kuti, ‘Kodi ndichira matenda angawa?’” 10  Ndiyeno Elisa anayankha Hazaeli kuti: “Pita ukamuuze kuti, ‘Muchira ndithu,’ koma Yehova wandionetsa+ kuti afa ndithu.”+ 11  Pamenepo Elisa anayang’anitsitsa Hazaeli kuti dwii! mpaka Hazaeliyo anachita manyazi. Kenako munthu wa Mulungu woonayo anayamba kulira.+ 12  Hazaeli ataona zimenezi anafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukulira mbuyanga?” Elisa anayankha kuti: “Chifukwa ndikudziwa bwino zoipa+ zimene iweyo udzachitire ana a Isiraeli. Malo awo otetezedwa udzawatentha ndi moto, amuna ochita kusankhidwa pakati pawo udzawapha ndi lupanga, ana awo aang’ono udzawaphwanyaphwanya,+ ndipo akazi awo apakati udzawatumbula.”+ 13  Hazaeli atamva mawu amenewa, anati: “Ndine ndani ine mtumiki wanu, galu ngati ine,+ kuti ndichite zinthu zazikulu ngati zimenezi?” Koma Elisa anati: “Yehova wandionetsa iweyo utakhala mfumu ya Siriya.”+ 14  Pambuyo pake Hazaeli anachoka kwa Elisa ndipo anapita kwa mbuye wake. Ndiyeno mbuye wakeyo anam’funsa kuti: “Kodi Elisa wakuuza kuti chiyani?” Hazaeli anayankha kuti: “Wandiuza kuti, ‘Muchira ndithu.’”+ 15  Tsiku lotsatira, Hazaeli anatenga chofunda n’kuchiviika m’madzi. Kenako anaphimba nacho mfumuyo kumaso+ moti inamwalira,+ ndipo Hazaeli+ anayamba kulamulira m’malo mwake. 16  M’chaka chachisanu cha Yehoramu+ mwana wa Ahabu mfumu ya Isiraeli, pamene Yehosafati anali mfumu ya Yuda, Yehoramu+ mwana wa Yehosafati mfumu ya Yuda, anakhala mfumu. 17  Yehoramu anakhala mfumu ali ndi zaka 32, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 8.+ 18  Iye anayenda m’njira ya mafumu a Isiraeli+ monga mmene ankachitira a m’nyumba ya Ahabu,+ chifukwa anakwatira+ mwana wa Ahabu. Choncho iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova. 19  Koma Yehova sanafune kuwononga ufumu wa Yuda+ chifukwa cha Davide mtumiki wake,+ pakuti anamulonjeza kuti adzam’patsa nyale+ nthawi zonse, iyeyo ndi ana ake. 20  M’masiku a Yehoramu, Aedomu+ anagalukira Yuda. Iwo anachoka m’manja mwa Yuda n’kusankha mfumu+ yoti iziwalamulira. 21  Choncho Yehoramu anapita ku Zairi usiku pamodzi ndi magaleta ake onse. Kumeneko, iye ananyamuka usiku n’kukapha Aedomu amene anamuzungulira. Anaphanso akuluakulu oyang’anira asilikali okwera magaleta, ndipo anthu ena onse anathawira kumahema awo. 22  Koma Aedomu anapitirizabe kugalukira Yuda mpaka lero. Inalinso nthawi imeneyi pamene Libina+ anagalukira Yuda. 23  Nkhani zina zokhudza Yehoramu ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda. 24  Pomalizira pake, Yehoramu anagona pamodzi ndi makolo ake,+ ndipo anaikidwa m’manda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide.+ Kenako mwana wake Ahaziya+ anayamba kulamulira m’malo mwake. 25  M’chaka cha 12 cha Yehoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Isiraeli, Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anakhala mfumu.+ 26  Ahaziya anayamba kulamulira ali ndi zaka 22 ndipo analamulira ku Yerusalemu chaka chimodzi.+ Mayi ake dzina lawo linali Ataliya+ mdzukulu wa Omuri+ mfumu ya Isiraeli. 27  Iye anayenda m’njira ya anthu a m’nyumba ya Ahabu,+ ndipo anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova+ monga mmene anachitira a m’nyumba ya Ahabu, chifukwa anali wachibale wa nyumba ya Ahabu.+ 28  Chotero iye anapita ku nkhondo ndi Yehoramu mwana wa Ahabu kukamenyana ndi Hazaeli+ mfumu ya Siriya ku Ramoti-giliyadi.+ Koma Asiriyawo anakatha+ Yehoramu. 29  Choncho mfumu Yehoramu+ inabwerera n’kupita ku Yezereeli+ kuti ikachire zilonda zimene Asiriya anaivulaza ku Rama,* pamene inali kumenyana ndi Hazaeli mfumu ya Siriya. Chotero Ahaziya+ mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anapita ku Yezereeli kukaona Yehoramu mwana wa Ahabu chifukwa anali kudwala.

Mawu a M'munsi

“Rama” ndi chidule cha Ramoti-giliyadi.