2 Mafumu 7:1-20

7  Tsopano Elisa anati: “Amuna inu, mverani mawu a Yehova.+ Yehova wanena kuti, ‘Mawa chapanthawi ngati ino, pachipata cha Samariya, ufa wosalala wokwana muyezo umodzi wa seya,* mtengo wake udzakhala sekeli* limodzi, ndipo balere wokwana miyezo iwiri ya seya, mtengo wake udzakhalanso sekeli limodzi.’”+  Koma msilikali wothandiza mfumu amene anaigwiria ndi dzanja lake,+ anayankha munthu wa Mulungu woonayo, kuti: “Ngakhale Yehova atatsegula zotsekera madzi akumwamba,+ kodi zimenezo zingachitike?”+ Pamenepo Elisa anati: “Uona zimenezi ndi maso ako,+ koma sudya nawo.”+  Ndiyeno panali anthu anayi akhate amene anali pachipata.+ Iwo anayamba kufunsana kuti: “Kodi tikhalirenji pano mpaka kufa?  Tikati, ‘Tiyeni tilowe mumzinda,’ tikafera momwemo chifukwa muli njala.+ Tikatinso tikhale pano, tifa. Ndiye tiyeni tikalowe mumsasa wa Asiriya. Akakatisiya ndi moyo, tikhala ndi moyo, koma akakatipha, chabwino tikafa.”+  Choncho ananyamuka kukungoyamba kumene kuda, n’kukalowa mumsasa wa Asiriyawo. Anakafika m’mphepete mwa msasawo ndipo anadabwa kupeza kuti munalibe aliyense.  Yehova anali atachititsa anthu a mumsasa wa Asiriyawo kumva+ phokoso la magaleta ankhondo, phokoso la mahatchi, ndi phokoso la gulu lalikulu la asilikali amphamvu.+ Choncho anthuwo anauzana kuti: “Taonani! Mfumu ya Isiraeli yaitanitsa mafumu a Ahiti+ ndi mafumu a Iguputo+ kuti abwere kudzamenyana nafe!”  Nthawi yomweyo anthuwo ananyamuka n’kuyamba kuthawa kukungoyamba kumene kuda.+ Anasiya mahema awo, mahatchi awo,+ ndi abulu awo. Msasawo anausiya mmene unalili n’kuthawa kuti apulumutse miyoyo yawo.+  Akhate aja atafika m’mphepete mwa msasawo, analowa m’hema mmodzi ndipo anayamba kudya ndi kumwa. Kenako anatengamo siliva, golide, ndi zovala n’kupita nazo kwina kukazibisa. Atatero anabwereranso n’kudzalowa m’hema wina ndipo anatengamonso zinthu zina n’kukazibisa.+  Pomalizira pake, anayamba kuuzana kuti: “Zimene tikuchitazi si zabwino. Tiyeni tikauze ena nkhani yabwinoyi!+ Tikazengereza n’kudikira mpaka kucha, tidzakhala ndi mlandu.+ Choncho tiyeni tikalowe mumzinda ndipo tikanene kunyumba ya mfumu.” 10  Chotero akhatewo anapita n’kukafuulira alonda a pachipata+ cha mzinda kuti: “Tinapita kumsasa wa Asiriya ndipo tapeza kuti kulibe aliyense. Sikukumveka mawu a munthu aliyense koma kuli mahatchi ndi abulu omangidwa ndipo mahema ali mmene analili.”+ 11  Nthawi yomweyo, alonda a pachipatawo anafuulira anthu amene anali m’nyumba ya mfumu. 12  Mfumuyo itangomva inadzuka usiku, ndipo inauza atumiki ake kuti:+ “Ndikuuzeni zimene Asiriyawa atichita.+ Iwo akudziwa bwino kuti ife tili ndi njala,+ choncho achoka mumsasamo n’kukabisala kutchire.+ Maganizo awo ndi akuti, ‘Atuluka mumzindamo ndipo tiwagwira amoyo. Kenako ifeyo tikalowa mumzindamo.’” 13  Ndiyeno mtumiki mmodzi wa mfumu anayankha kuti: “Uzani anthu atenge mahatchi asanu pa mahatchi amene atsala mumzinda ndipo muwatume kuti akaone. Anthuwo n’chimodzimodzi ndi gulu lonse la Aisiraeli amene atsala mumzindamu,+ ndiponso n’chimodzimodzi ndi gulu lonse la Aisiraeli amene afa.”+ 14  Choncho iwo anatenga magaleta awiri ndi mahatchi, ndipo mfumu inawatuma kumsasa wa Asiriya ndi kuwauza kuti: “Pitani mukaone.” 15  Anthuwo anatsatira Asiriyawo mpaka kukafika ku Yorodano, ndipo m’njira monsemo munali zovala ndi ziwiya+ zimene Asiriyawo anataya pothawa.+ Kenako anthuwo anabwerera n’kukanena kwa mfumu. 16  Tsopano anthu anapita kukafunkha+ msasa wa Asiriya. Choncho ufa wosalala wokwana muyezo umodzi wa seya, mtengo wake unafika pa sekeli imodzi, ndipo balere wokwana miyezo iwiri ya seya, mtengo wake unafikanso pa sekeli imodzi, mogwirizana ndi mawu+ a Yehova. 17  Mfumu inaika msilikali woithandiza amene anaigwira+ ndi dzanja uja kuti akhale woyang’anira pachipata. Koma anthu anam’pondaponda+ pachipatapo moti anafa, monga mmene munthu wa Mulungu woona uja ananenera,+ pamene mfumu inabwera kwa iye. 18  Chotero zinachitikadi monga mmene munthu wa Mulungu woona uja ananenera kwa mfumu, kuti: “Balere wokwana miyezo iwiri ya seya mtengo wake udzafika pa sekeli imodzi, ndipo ufa wosalala wokwana muyezo umodzi wa seya, mtengo wake udzafikanso pa sekeli imodzi mawa, pa nthawi ngati ino pachipata cha Samariya.”+ 19  Koma msilikali wothandiza mfumu uja anamuyankha munthu wa Mulungu woonayo kuti: “Ngakhale Yehova atatsegula zotsekera madzi akumwamba, kodi mawu anuwa angakwaniritsidwe?”+ Pamenepo Elisa anati: “Uona zimenezi ndi maso ako, koma sudya nawo.”+ 20  Choncho zinam’chitikiradi motero+ pamene anthu anam’pondaponda+ pachipata mpaka kufa.

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 12.
“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli limodzi linali lofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.